40 days English and Nyanja conversation with Flores.

Hello!
This is KYUHWAN, your contact at All in one Language!


In this session, we will learn a conversation in English and Chi-Chewa languages using the 'Flores200' data provided by 'MetaAI.' This data consists of a total of 997 sentences, so if you read 25 sentences per day, you can see your language skills improve within 40 days.


Furthermore, this data has translations in the same content for 204 languages, so you can use the blog search function at the top to search for the desired language. However, please note that this data will be reflected in the blog starting from June 2023, and it takes six months for all the data to be incorporated. If the language you search for is not available, it means it hasn't been included yet, so please understand.

The language list is provided at the bottom of this post.


[Day1]

English : On Monday, scientists from the Stanford University School of Medicine announced the invention of a new diagnostic tool that can sort cells by type: a tiny printable chip that can be manufactured using standard inkjet printers for possibly about one U.S. cent each.

Nyanja : Tsiku Lolemba, asayansi ochokera ku Stanford University School of Medicine analengeza zakupangidwa kwa chida chatsopano chomwe chitha kusiyanitsa ma cell ndi mtundu: kachipangizo kakang´ono kosindikizidwaka kakhoza kupangidwa pogwiritsa ntchito ma inkjet osindikizika apamwamba pafupifupi cent imodzi ya U.S iliyonse.



English : Lead researchers say this may bring early detection of cancer, tuberculosis, HIV and malaria to patients in low-income countries, where the survival rates for illnesses such as breast cancer can be half those of richer countries.

Nyanja : Akatswiri otsogolera kafukufuku akuti izi zimabweretsa kuziwa mwansanga Khansa, Chifuwa Chachikulu, HIV ndi Malungo kwa odwala omwe ali m´mayiko omwe chuma chawo chili chochepa, komwe mapulumukidwe kumatenda monga Khansa ya m´mawere kutha kukhala theka la mayiko olemera.



English : The JAS 39C Gripen crashed onto a runway at around 9:30 am local time (0230 UTC) and exploded, closing the airport to commercial flights.

Nyanja : Ndege yamtundu wa JAS 39C Gripen idagwa munsewu wowulukira ndege cham´ma 09:30 m´mawa nthawi yakumeneko (0230 UTC), ndipo idaphulika, kupangitsa kuti ndege zisayendenso.



English : The pilot was identified as Squadron Leader Dilokrit Pattavee.

Nyanja : Munthu woyendetsa ndegeyo anadziwika ngati mtsogoleri wa Squadron, Dilokrit Pattavee.



English : Local media reports an airport fire vehicle rolled over while responding.

Nyanja : Atolankhani akonko akuti galimoto yozimitsa moto kubwalo la ndege idagudubuzika pamene imagwira ntchito.



English : 28-year-old Vidal had joined Barça three seasons ago, from Sevilla.

Nyanja : Vidal wazaka 28 , adalowa Barca nyengo zitatu zapitazo kuchoka ku Sevilla.



English : Since moving to the Catalan-capital, Vidal had played 49 games for the club.

Nyanja : Chipitileni ku likulu Catalan, Vidal adasewera masewero 49 mukalabu yake.



English : The protest started around 11:00 local time (UTC+1) on Whitehall opposite the police-guarded entrance to Downing Street, the Prime Minister´s official residence.

Nyanja : Chionetsero chinayamba nthawi ya 11 nthawi yao (UCT+1) ku Whitehall moyang´anizana ndi chipata chotetezedwa ndi apoliso cholowela ku Downing Street kumene kuli nyumba Nduna Yaikulu.



English : Just after 11:00, protesters blocked traffic on the northbound carriage in Whitehall.

Nyanja : Itangokwana 11 koloko aziwonetsero zokwiya atsekela magalimoto onse wodutsa kupita ku Northbound carriage ku Whitehall.



English : At 11:20, the police asked the protesters to move back on to the pavement, stating that they needed to balance the right to protest with the traffic building up.

Nyanja : Pamene nthawi idali 11:20, apolisi adafunsa anthu kuti abwerele ku njira, kunena kuti akuyenera ku linganiza ufulu wawo wotsutsa ndi kuyamba kwa unyinji wa magalimoto.



English : Around 11:29, the protest moved up Whitehall, past Trafalgar Square, along the Strand, passing by Aldwych and up Kingsway towards Holborn where the Conservative Party were holding their Spring Forum in the Grand Connaught Rooms hotel.

Nyanja : Cha m´ma 11:29, chiwonetserochi chinapita ku Whitehall, kudutsa Trafalgar Square, kudutsa Strand, ndikudutsa Aldwych ndikukwera Kingsway kulowera ku Holborn komwe chipani cha Conservative chimachita msonkhano wao mchipinda china ku Grand Connaught Hotel.



English : Nadal´s head to head record against the Canadian is 7–2.

Nyanja : Mbiri yazotsatira pamasewero pakati pa Nadal ndi Canada ndi 7-2.



English : He recently lost against Raonic in the Brisbane Open.

Nyanja : Posachedwa adagonja kwa a Raonic ku masewera aku Brisbane.



English : Nadal bagged 88% net points in the match winning 76 points in the first serve.

Nyanja : Nadal adagoletsa zigoli zokwana 88% pamasewerowo ndikupambana ndima point 76 mchigawo choyamba.



English : After the match, King of Clay said, ¨I am just excited about being back in the final rounds of the most important events. I am here to try to win this.¨

Nyanja : Masewera atatha, King of Clay adati, "Ndili wokondwa kuti ndafikaso ndime zomaliza zazochitika zofunikira zimenezi. Ndili pano kuyesa kupambana zimenezi."



English : ¨Panama Papers¨ is an umbrella term for roughly ten million documents from Panamanian law firm Mossack Fonseca, leaked to the press in spring 2016.

Nyanja : "Panama papers", ndi liwu lomangirira la pafupifupi makalata mamiliyoni khumi ochokera ku kampani ya za malamulo ya Panama ya a Mossack Fonseca, yomwe idatulutsidwa mosayenera kwa atolankhani nthawi yachilimwe mchaka cha 2016.



English : The documents showed fourteen banks helped wealthy clients hide billions of US dollars of wealth to avoid taxes and other regulations.

Nyanja : Zikalata zinaonetsa kuti ma banki khumi ndi anayi anathandizila ma kasitomala achuma kubisa ma biliyoni a ndalama kuti apewe kukhoma misonkho ndi malamulo ena.



English : British newspaper The Guardian suggested Deutsche Bank controlled roughly a third of the 1200 shell companies used to accomplish this.

Nyanja : Nyuzipepala ya ku Britain yotchedwa the Guardina yati Deutsche bank imalamulira pafupifupi gawo limodzi mwa atatu la ma kampani mazana khumi ndi awiri a shell kuti izi zitheke.



English : There were protests worldwide, several criminal prosecutions, and the leaders of the governments of Iceland and Pakistan both resigned.

Nyanja : Panali zionetselo dziko lonse lapansi, ena kuimbana milandu ya umbanda ndipo atsogoleri amaiko a Iceland ndi Pakistani anatula pansi maudindo awo.



English : Born in Hong Kong, Ma studied at New York University and Harvard Law School and once held an American permanent resident ¨green card¨.

Nyanja : Adabadwira ku Hong Kong, a Ma adaphunzira ku New York University komanso ku Sukulu ya Zamalamulo ya Harvard choncho nthawi ina yake adali nzika yokhazikika ya America yokhala ndi "green card".



English : Hsieh implied during the election that Ma might flee the country during a time of crisis.

Nyanja : Zimene amatanthauza aHsieh panthawi ya zisankho ndizakuti a Ma akhoza kuthawa mu dziko nthawi ya zovuta.



English : Hsieh also argued that the photogenic Ma was more style than substance.

Nyanja : Hsieh adatinso kuti a Ma omwe amaoneka bwino mzithunzi adali opanda mfundo koma wokonda kupanga zachibwana.



English : Despite these accusations, Ma won handily on a platform advocating closer ties with the Chinese mainland.

Nyanja : Ngakhale izi zinanenedwa moteromo, Ma anapambana masankho polimbikitsa kulumikizana ndi mainland China.



English : Today´s Player of the Day is Alex Ovechkin of the Washington Capitals.

Nyanja : Katswiri wathu wosewera walero ndi Alex Ovechkin wa timu ya Washington Capitals.



English : He had 2 goals and 2 assists in Washington´s 5-3 win over the Atlanta Thrashers.

Nyanja : Adagoletsa zigoli ziwiri ndipo adathandizira ziwili pakumbana kwa Washington ndi 5-3 ndi Atlanta Thrashers.



[Day2]

English : Ovechkin´s first assist of the night was on the game-winning goal by rookie Nicklas Backstrom;

Nyanja : Kuthandiza koyamba kwa Ovechkin usikuwu kunali kwa chigoli chimene chinawapambanitsa masewera chomwe adachinya ndi watsopano a Nicklas Backstrom;



English : his second goal of the night was his 60th of the season, becoming the first player to score 60 or more goals in a season since 1995-96, when Jaromir Jagr and Mario Lemieux each reached that milestone.

Nyanja : Chigoli chake chachiwiri usikuwo chinali cha nambala 60 munyengoyo, kukhala osewera oyamba kugoletsa zigoli 60 kapena kuchulukilapo mu nyengo kuyambira 1995-96, pamene Jaromir Jagr ndi Mario Lemieux aliyese anakwanitsa kuchita zoterezi.



English : Batten was ranked 190th on the 2008 400 Richest Americans list with an estimated fortune of $2.3 billion.

Nyanja : A Batten adayikidwa pamulingo wa nambala 190 pamndandanda wa chaka cha 2008 wa anthu 400 wolemera aku America ndi chuma chochuluka kufikira $2.3 biliyoni.



English : He graduated from the College of Arts & Sciences of the University of Virginia in 1950 and was a significant donor to that institution.

Nyanja : Anamaliza maphunziro awo ku College ya Arts & Sciences ku University of Virginia mu 1950 ndipo ankathandiza kwambiri bungweli.



English : Iraq´s Abu Ghraib prison has been set alight during a riot.

Nyanja : Ndende ya Abu Ghraib ku Iraq yayatsidwa moto pa chiwawa.



English : The jail became notorious after prisoner abuse was discovered there after US forces took over.

Nyanja : Ndende imeneyi idatchuka pamene kudadziwika kuti akayidi amazuzidwa kumeneko pamene asilikali adziko la US adatenga ndendeyo.



English : Piquet Jr. crashed in the 2008 Singapore Grand Prix just after an early pit stop for Fernando Alonso, bringing out the safety car.

Nyanja : Piquet Jr. anachita ngozi muchaka cha 2008 ku Singapore Grand Prix atangoyima koyambilira pa piti Fenando Alonso, kupangitsa kutulutsa galimoto yachitetezo.



English : As the cars ahead of Alonso went in for fuel under the safety car, he moved up the pack to take victory.

Nyanja : M´mene magalimoto apatsogolo pa Alonso adalowa kukathira mafuta pambuyo pagalimoto yachitetezo, adasuntha kuyandikira kuti apambane.



English : Piquet Jr. was sacked after the 2009 Hungarian Grand Prix.

Nyanja : A Piquet Jr. ntchito yawo idathetsedwa pamene mpikisano wa 2009 Hungarian Grand Prix utatha.



English : At exactly 8:46 a.m. a hush fell across the city, marking the exact moment the first jet struck its target.

Nyanja : Nthawi itakwana ndendende 8:46 m´mawa bata linadzadza munzinda onse, kukumbukira nthawi imene ndege yoyamba idakantha.



English : Two beams of light have been rigged up to point skywards overnight.

Nyanja : Magetsi awiri adayikwa msangamsanga kuloza kumwamba usiku wonse.



English : Construction is ongoing for five new skyscrapers at the site, with a transportation center and memorial park in the middle.

Nyanja : Ntchito yomanga manyumba asanu ataliatali kwambiri ikupitilirabe pamalopo, pakati pazakhala malo azamayendedwe komaso paki ya chikumbutso.



English : The PBS show has more than two-dozen Emmy awards, and its run is shorter only than Sesame Street and Mister Rogers´ Neighborhood.

Nyanja : Chiwonetsero cha PBS chili ndi mphoto zoposa makumi awiri ndi zinayi za Emmy, ndipo kuthamanga kwake ndikochepera chabe kuposa nsewu wa Sesame ndi kumene amakhala bambo Rodgers.



English : Each episode of the show would focus on a theme in a specific book and then explore that theme through multiple stories.

Nyanja : Gawo lililonse la chiwonetselo limayika chidwi pa mutu m´buku lakelake ndipo limawunika ngati mutu uli ndi nkhani zingapo.



English : Each show would also provide recommendations for books that children should look for when they went to their library.

Nyanja : Chiwonetsero chilichonse chimaperekanso zoyenera kwamabuku a ana kuti akafunefune pamene akupita ku nyumba zowerengerako zawo.



English : John Grant, from WNED Buffalo (Reading Rainbow´s home station) said ¨Reading Rainbow taught kids why to read,... the love of reading — [the show] encouraged kids to pick up a book and to read.¨

Nyanja : John Grant, ochokera ku WNED Buffalo (Malo owerenga utawaleza) anati "kuwerenga utawaleza zimamphunzitsa ana chifukwa chakuti aziwerenga, ...kukonda kuwerenga-[chiwonetsero] kuwalimbikitsa ana kuti atenge buku ndi kuwerenga."



English : It is believed by some, including John Grant, that both the funding crunch and a shift in the philosophy of educational television programming contributed to ending the series.

Nyanja : Anthu ena amakhulupira kuti , kuphatikiza a John Grant, kuti kutsika kobwereketsa ndalama ndikusintha mu chikhulupiliro cha mndandanda wa maphunziro pa kanema kudanthandiza kuthetsa mndandanda wa zochitika.



English : The storm, situated about 645 miles (1040 km) west of the Cape Verde islands, is likely to dissipate before threatening any land areas, forecasters say.

Nyanja : Mkuntho umene uli pa ntunda wamamayilosi 645 (makilomita 1040) ku madzulo kwa zilumba za Carpe Verde, utha kutha isanafike kuntunda, olosela za nyengo akutero.



English : Fred currently has winds of 105 miles per hour (165 km/h) and is moving towards the northwest.

Nyanja : Fred pano tikunena ali ndi mphepo yokwana mamayilosi 105 (makilomita 165 pa ola) kuyenda chakumpoto waku zambwe.



English : Fred is the strongest tropical cyclone ever recorded so far south and east in the Atlantic since the advent of satellite imagery, and only the third major hurricane on record east of 35°W.

Nyanja : Fred ndi mphepo yakuntho yomwe sidachitikepo ku mwera ndi kuzambwe ku Atlantic chiyambireni zinthuzi, ndipo mphepo yina yachitatu kufika 35◦W.



English : On September 24, 1759, Arthur Guinness signed a 9,000 year lease for the St James´ Gate Brewery in Dublin, Ireland.

Nyanja : Pa 24 Seputembala mchaka cha 1759 a Arthur Guinnes adasaina pangano la zaka 9,000 kupeleka kampani yophika mowa ya St James Gate ku Dublin ku Ireland.



English : 250 years later, Guinness has grown to a global business that turns over 10 billion euros (US$14.7 billion) every year.

Nyanja : Kenako muzaka za 250, Guiness idapambana busines ya dziko lonse yomwe yidabweletsa ndalama pafupifupi mabiliyoni $10 chaka chilichonse.



English : Jonny Reid, co-driver for the A1GP New Zealand team, today made history by driving the fastest over the 48-year-old Auckland Harbour Bridge, New Zealand, legally.

Nyanja : A John Reid , wothandizira woyendetsa A1GP wagulu la New Zealand , lero wapanga mbiri atayendetsa mwachangu kudutsa mtsinje wazakalekale umene uli ndi zaka 48 wa Auckland Harbour Bridge, ku New Zealand, movomelezeka.



English : Mr Reid managed to drive the New Zealand´s A1GP car, Black Beauty at speeds over 160km/h seven times over the bridge.

Nyanja : Bambo Reid anakwanilitsa kuyendetsa galimoto ya mtundu wa A1GP ku New Zealand, Black Beauty pa liwiro loposa 160km/h kasanu ndi kawiri pa mulatho.



English : The New Zealand police had trouble using their speed radar guns to see how fast Mr Reid was going because of how low Black Beauty is, and the only time the police managed to clock Mr Reid was when he slowed down to 160km/h.

Nyanja : Apolisi aku New Zealand amalephera kugwiritsa ntchito zida zawo zoyezera mathamangidwe agalimoto kuti awone m´mene Bambo Reid amathamangira chifukwa chakuchepa kwa Black Beauty, nthawi yokhayo adakwanitsa kuyeza m´mene amathamangisira galimoto Bambo Reid ndipamene kuthamanga kwawo kudachepa kufika pa 160km /h.



[Day3]

English : In the last 3 months, over 80 arrestees were released from the Central Booking facility without being formally charged.

Nyanja : Pa miyezi itatu yapitayo, anthu 80 amene adamangidwa adatulutsidwa ku malo a Central Booking facility wosazengedwa mlandu.



English : In April this year, a temporary restaining order was issued by Judge Glynn against the facility to enforce the release of those held more than 24 hours after their intake who did not receive a hearing by a court commissioner.

Nyanja : Mu Epulo chaka chino, chiletso cha kanthawi kochepa chidapelekedwa ndi oweluza milandu a Glyn motsutsana ndi malowo kuti akakamize kutulutsidwa kwa omwe adasungidwa koposa maola 24 atatengedwa pamene sanalandire chigamulo ndi mkulu wa khothi.



English : The commissioner sets bail, if granted, and formalizes the charges filed by the arresting officer. The charges are then entered into the state´s computer system where the case is tracked.

Nyanja : Munthu amene adapatsidwa mphamvu amapereka belo, ngati yapelekedwa, ndipo amakhazikitsa ndondomeko ya milandu imene yayikidwa pamodzi ndi wapolisi amene anakamanga munthu. Milanduyo imalowetsedwa mu makina a kompuyuta aboma kumene mulandu umatsatidwa.



English : The hearing also marks the date for the suspect's right to a speedy trial.

Nyanja : Kuyamba kumva mulanduyu zaonetsaso chiyambi cha ufulu wawoganiziridwa kuti azengedwe mwachangu.



English : Peter Costello, Australian treasurer and the man most likely to succeed Prime Minister John Howard as Liberal party leader has thrown his support behind a nuclear power industry in Australia.

Nyanja : Peter Costello, msungichuma waku Australia, amene akuyembekezeleka kuzalowa mpando wa Prime Minister wa a John Howard ngati mtsogoleri wa chipani cha Liberal wathira mang´ombe ake pa nkhani yamafakitale a Nuclear ku Australia.



English : Mr Costello said that when nuclear power generation becomes economically viable, Australia should pursue its use.

Nyanja : A Costello adanena kuti pamene magetsi a nyukiliya azakhale aphindu pazachuma, dziko la Australia lizalondoloza kuti lizigwiritsa ntchito magetsiwa.



English : ¨If it becomes commercial, we should have it. That is, there´s no in-principle objection to nuclear energy¨ Mr Costello said.

Nyanja : "Zikafika pokhala zamalonda, tikhale nazo. Ndiye kuti, palibe mfundo yotsutsa za mphamvu ya nyukilia bambo" Costello adatero.



English : According to Ansa, ¨police were concerned by a couple of top-level hits they feared might spark a full-blown war of succession.

Nyanja : Malingana ndi Ansa, "apolisi anali okhudzidwa ndi ziwopsezo zingapo zimene amawopa kuti zikhoza kubweretsa nkhondo zotsagana.



English : Police said Lo Piccolo had the upper hand because he had been Provenzano´s right-hand man in Palermo and his greater experience won him the respect of the older generation of bosses as they pursued Provenzano´s policy of keeping as low as possible while strengthening their power network.

Nyanja : Apolisi adati a Lo Piccolo adali patsogolo chifukwa adakhala omuthandizira Provenzano ku Palermo ndipo zomwe adakumana nazo zidampezetsa ulemu wama bwana akuluakulu akale pamene amatsata lamulo la Provenzano la kudekha pamene amalimbikitsa mphamvu yawo ya netiweki.



English : These bosses had been reined in by Provenzano when he put an end to the Riina-driven war against the state that claimed the lives of Mafia crusaders Giovanni Falcone and Paolo Borsellino in 1992.¨

Nyanja : Mabwana amalamulidwa ndi Provenzano atathetsa nkhondo imene inayambitsidwa ndi Riina polimbana ndi boma limene linaphanso zigawenga zotchedwa Giovanni Falcone ndi Paolo Borsellino mu chaka cha 1992."



English : Apple CEO Steve Jobs unveiled the device by walking onto the stage and taking the iPhone out of his jeans pocket.

Nyanja : Mtsogoleri wamkulu wa Apple a Steve Jobs anawulula zachipangizo pobwera pa nsanja ndikutulutsa iPhone mthumba lawo lachovala cha jeans.



English : During his 2 hour speech he stated that ¨Today Apple is going to reinvent the phone, We are going to make history today¨.

Nyanja : Mukuyankhula kwake kwama ola awiri ananena kuti "Lero Apple ipanganso foni, Tipanga mbiri lero".



English : Brazil is the largest Roman Catholic country on Earth, and the Roman Catholic Church has consistently opposed the legalization of same-sex marriage in the country.

Nyanja : Ku Brazil ndiku likuli la Tchalitchi ya Katolika padziko pano ndipo tchalitchi Chakatolika chimatsutsa mosindika zokwatilana amuna kapena akazi wokhawokha.



English : The National Congress of Brazil has debated legalization for 10 years, and such civil marriages are currently only legal in Rio Grande do Sul.

Nyanja : National Congress ku dziko la Brazil yakambirana pazovomerezeka kwa zaka 10, ndipo maukwati aboma pakanali pano ndi ovomerezeka ku Rio Grande do Sul kokha.



English : The original bill was drafted by former mayor of São Paulo, Marta Suplicy. The proposed legislation, after being amended, is now in the hands of Roberto Jefferson.

Nyanja : Lamulo loyambilira adalemba ndi Mfumu yakale ya mzinda wa São Paulo, a Marta Suplicy. Lamulo lomwe limaperekedwali, litasinthidwa, panopa lili m´manja mwa Roberto Jefferson.



English : Protesters hope to collect a petition of 1.2 million signatures to present to the National Congress in November.

Nyanja : Ochita ziwonetsero ali ndiyembekezo kuti atolera zosayinira zokwana 1.2 miliyoni kuti akapereke ku National Congress mu Novembala.



English : After it became apparent that many families were seeking legal help to fight the evictions, a meeting was held on March 20 at the East Bay Community Law Center for the victims of the housing scam.

Nyanja : Pamene zinadziwika kuti mabanja wochuluka akufuna chithandizo chokhudza malamulo kuti alimbane ndi kuchotsedwa mnyumba kumene kunachitika, msonkhano udalipo pa 20 Marichi ku East Bay Community Law Center kwa amene adakhuzidwa ndi chinyengo chokhudza nyumbazi.



English : When the tenants started sharing what had occurred to them, most of the families involved suddenly realized that Carolyn Wilson of the OHA had stolen their security deposits, and skipped out of town.

Nyanja : Pamene okhala m´manyumbamo atayamba kugawa zomwe zawachitikira, mabanja ambiri omwe adali okhuzidwa mwadzidzi adazindikira kuti a Carolyn Wilson wa OHA adaba ndalama zawo zoyikidwa ngati zachitetezo, ndikuthawa mumzinda waung´onowo.



English : Tenants at Lockwood Gardens believe that there may be another 40 families or more to face eviction, since they learned that OHA police are also investigating other public housing properties in Oakland that may be caught up in the housing scam.

Nyanja : Anthu okhala m´manyumba ku Lockwood Gardens akukhulupilira kuti pakhoza kukhala mabanja ena 40 kapena kupitilira apo womwe atulutsidwe mnyumbamo, chifukwa amva kuti apolisi aku OHA akufufuzanso nyumba zina za boma ku Oakland zomwe zitha kukhuzidwa ndi zachinyengo zamanyumba.



English : The band canceled the show at Maui´s War Memorial Stadium, which was set to be attended by 9,000 people, and apologized to fans.

Nyanja : Gulu loyimbali lidasintha chikonzero choimba ku Maui´s War Memorial Stadium kumene kumayembekezeleka kubwela anthu okwana 9,000, ndipo iwo anapepesa kwa anthu okonda gululi.



English : The band´s management company, HK Management Inc., gave no initial reason when they canceled on September 20, but blamed logistical reasons by the next day.

Nyanja : Kampani yoyang´anira gulu loyimba ya HK Management Inc., poyambilira sinapereke chifukwa pamene adati sayimbaso pa 20 Seputembala, ndipo adati chinali chifukwa cha zina zokhuza mayendedwe ndi magonedwe.



English : The famous Greek lawyers, Sakis Kechagioglou and George Nikolakopoulos have been imprisoned in the Athens´ jail of Korydallus, as they were found guilty of graft and corruption.

Nyanja : Woyimira milandu wotchuka kwambiri aku Greece, a Sakis Kechagioglou komanso a George Nikolakopoulos adaponyedwa mchitokosi ya Atene ku Korydallus, kamba kopezeka wolakwa pankhani ya ziphuphu ndi katangale.



English : As a result of this, a big scandal within the Greek legal community has been raised through the exposure of illegal actions that judges, lawyers, solicitors and attorneys have done during the previous years.

Nyanja : Pachifukwa ichi, nkhani zosakhala bwino zidaululika zomwe zimakhudza a zamalamulo ku Greece ngati woweluza milandu, woyimila anthu pamilandu, ma solicitor, ndi ma attorney, makamaka zomwe anachita zaka zam´mbuyomu.



English : A few weeks ago, after the information published by the journalist Makis Triantafylopoulos in his popular Television show ¨Zoungla¨ in Alpha TV, the member of Parliament and lawyer, Petros Mantouvalos was abdicated as members of his office had been involved in illegal graft and corruption.

Nyanja : Masabata angapo apitawo, mauthenga atafalitsidwa ndi mtolankhani Makis Triantafylopoulos mu pologalamu yake yotchuka ya Television Show "Zoungla" mu Alpha TV, membala wa nyumba ya malamulo komanso woyimilira pamulandu, Petros Mantouvalos anatengedwa chifukwa mamembala ogwira naye ntchito amazembetsa ndalama zaboma komanso kupanga katangale.



English : Moreover, top judge Evangelos Kalousis is imprisoned as he found guilty of corruption and degenerate behaviour.

Nyanja : Kuphatikizira pamenepo, oweruza wamkulu Evangelos Kalousisi wamangidwa pamene wapezeka wolakwa pa chinyengo ndi khalidwe loyipa.



[Day4]

English : Roberts flatly refused to say about when he believes life begins, an important question when considering the ethics of abortion, saying that it would be unethical to comment on the specifics of likely cases.

Nyanja : Roberts adakanitsitsa kukambapo za nthawi imene amakhulupirira kuti moyo umayamba, funso labwino kwambiri poganizira pazoyenera kutsatira pochotsa pathupi, adati sikoyenera kuyankhapo mwapadera pazimene zitha kuchitika.



English : He did, however, reiterate his earlier statement that Roe v. Wade was the ¨settled law of the land¨, emphasizing the importance of consistent Supreme Court rulings.

Nyanja : Adatero, choncho, adabwelezapo zimene zidanenedwapo kale kuti Roe v. Wade ndi "lamulo lokhazikika mdzikomo", ndikutsimikizira kwakufunikira kwa zigamulo zosasinthasintha za Bwalo Lalikulu la Apilo.



English : He also confirmed that he believed in the implied right to privacy which the Roe decision depended upon.

Nyanja : Adatsimikizaso kuti amakhulupilira ndi kupereka ufulu wachinsisi umene chigamulo cha Roe chidadalirapo.



English : Maroochydore had finished on top of the ladder, six points clear of Noosa in second.

Nyanja : Maroochydore adamalizira mpaka pamwamba pa mulingo, ma point asanu ndi imodzi patsogolo pa Noosa womwe ndi achiwiri.



English : The two sides would meet in the major semi final where Noosa ran out winners by 11 points.

Nyanja : Mbali zonse ziwiri zimakumana mu mumasewero a semifinal pamene Noosa adapambana ndi ma point khumi ndi imodzi.



English : Maroochydore then defeated Caboolture in the Preliminary Final.

Nyanja : Maroochydore nthawi imeneyo adagonjetsa Caboolture pamapeto amasewero oyamba.



English : Hesperonychus elizabethae is a species of the family Dromaeosauridae and is a cousin of Velociraptor .

Nyanja : Hesperonychus elizabethae ndiwochokera kubanja lama Dromaeosauridae yemwe ali msuweni wake wa Velociraptor.



English : This fully feathered, warm blooded bird of prey was believed to have walked upright on two legs with claws like the Velociraptor.

Nyanja : Zinawonetsera kwambiri, amakhulupilira kuti mbalame imene matenthedwe athupi amasiyana ndi malo amene ili inayenda ndimiyendo iwiri ndi zikhadabo ngati Velociraptor.



English : Its second claw was larger, giving rise to the name Hesperonychus which means ¨western claw.¨

Nyanja : Chikhadabo chake chachiwiri chinali chokulirapo, chidabweletsa dzina la Hesperonychus limene limatanthauza "chikhadabo chakumadzulo".



English : In addition to the crushing ice, extreme weather conditions have been hampering rescue efforts.

Nyanja : Chifukwaso cha madzi ouma oundana, komaso nyengo yoyipa kwambiri zakhala zikulepheretsa kuthekera kopulumutsa.



English : Pittman suggested that conditions wouldn´t improve until sometime next week.

Nyanja : Pittman adati zinthu sizichita bwino mpaka sabata yamawa.



English : The amount and thickness of the pack ice, according to Pittman, is the worst it has been for sealers in the past 15 years.

Nyanja : Kuchuluka ndi makulidwe amadzi owuma akulu oyendayenda, malingana ndi a Pittman, zidali zoyipa kwambiri zomwe omatamata sadakomane nazopo mzaka 15 zapitazo.



English : News spread in the Red Lake community today as funerals for Jeff Weise and three of the nine victims were held that another student was arrested in connection with the school shootings of March 21.

Nyanja : Nkhani inafalikila ku dera la Red Lake lero ngati maliro a jeff Weiss ndi atatu mwa asanu ndi anai okhuzidwa ndi ngoziyo achitika ndipo wophunzila m´modzi anamangidwa pokhuzidwa ndi kuombera ku sukulu pa 21 Marichi.



English : Authorities said little officially beyond confirming today´s arrest.

Nyanja : Akuluakulu adayankhula zochepa kupatulako kutsimikiza za kumangidwa kwa lero.



English : However, a source with knowledge of the investigation told the Minneapolis Star-Tribune that it was Louis Jourdain, 16-year old son of Red Lake Tribal Chairman Floyd Jourdain.

Nyanja : Choncho, amene amadziwa zakufufuzaku adafotokozera a Minneapolis Star-Tribune kunena kuti iye ndi Louis Jourdain, mwana wazaka 16 wa a Floyd Jourdain omwe ndiwapampando wa Red Lake Tribal.



English : It is not known at this time what charges will be laid or what led authorities to the boy but juvenile proceedings have begun in federal court.

Nyanja : Pakadali pano sizinaziwike kuti mulandu wake ukakhala otani kapena chinachitisa audindo kwa nyamatayo koma milandu idayamba ku khohi.



English : Lodin also said officials decided to cancel the runoff in order to save Afghans the expense and security risk of another election.

Nyanja : A Lodin adanenanso kuti akuluakulu a boma adasankha kusiya chisankho chachibwereza ndicholinga chopulumutsa ndalama komaso chiopsezo chachitetezo chomwe chingabwere kamba ka chisankho china.



English : Diplomats said that they had found enough ambiguity in the Afghan constitution to determine the runoff as unnecessary.

Nyanja : Akazembe anati anapeza zambiri zosamveka bwino mu malamulo akulu a dziko la Afghanistan kuti ngati masankho achibwereza siwofunikira.



English : This contradicts earlier reports, which said that cancelling the runoff would have been against the constitution.

Nyanja : Izi zikutsutsana ndi malipoti amene ananveka poyamba oti kulepheletsa kuvota kachiwiri nkosephana ndi malamulo aakulu oyendetsela dziko.



English : The aircraft had been headed to Irkutsk and was being operated by interior troops.

Nyanja : Ndege imeneyi idapititsidwa ku Irkutsk komanso inkayendetsedwa ndi asilikali ankhondo.



English : An inquiry was established to investigate.

Nyanja : Kafukufuku adakhazikitsidwa kuti afufuze.



English : The Il-76 has been a major component of both the Russian and Soviet military since the 1970s, and had already seen a serious accident in Russia last month.

Nyanja : Il-76 yakhala mbali yayikulu ya asilikali a dziko la Russia komanso Soviet kuchokera mzaka zam´ma 1970, choncho adawonapo kale ngozi yowopsa ku Russia mwezi watha.



English : On October 7 an engine separated on takeoff, without injuries. Russia briefly grounded Il-76s after that accident.

Nyanja : Pa Okutobala 7 injini idalekana pamene imanyamuka, padalibe amene adavulala. Russia idayimitsa mwachidule Il-76s chifukwa changoziyo.



English : 800 miles of the Trans-Alaska Pipeline System were closed down following a spill of thousands of barrels of crude oil south of Fairbanks, Alaska.

Nyanja : Payipi yayitali mamayilosi 800 yaku Trans-Alaska adayitseka potsatira kutayika kwamafuta kumwera kwa Fairbank , ku Alaska.



English : A power failure following a routine fire-command system test caused relief valves to open and crude oil overflowed near the Fort Greely pump station 9.

Nyanja : Kukanika kwa magetsi pambuyo pa njira yoyeserera moto monga mwamasiku wonse kudachititsa mavavu amene amathandiza kutseguka ndipo mafuta osasefa adasefukira moyandikana ndi station yamagalimoto ya Fort Greely 9.



[Day5]

English : The valves opening allowed a pressure release for the system and oil flowed on a pad to a tank that can hold 55,000 barrels (2.3 million gallons).

Nyanja : Kutsegula kwama valve kumalora kuti kudzadzana kwa mpweya mu makina kutuluke ndipo mafuta ofewetsa zitsulo adutse muma pad mpakana ku thanki imene ingathe kusunga migolo yokwana 55,000 (zigubu zokwana mamiliyoni 2.3).



English : As of Wednesday afternoon, the tank vents were still leaking probably from thermal expansion inside the tank.

Nyanja : Kuyambira Lachitatu, mapayipi amathanki amachucha mwina chifukwa chakutetha nkati mwathanki.



English : Another secondary containment area below the tanks capable of holding 104,500 barrels was not yet filled to capacity.

Nyanja : Chigawo china chachiwili chidali pansi pama thanki chosunga migolo 104,500 ndipo chinali chosadzaza konse.



English : The comments, live on television, were the first time that senior Iranian sources have admitted that the sanctions are having any effect.

Nyanja : Ndemanga zomwe zinali pa wailesi yakanema za nthawi yomweyo, ndizoyamba kuti akuluakulu aku Iran adavomereza kuti ziletso zomwe alinazo zikubweretsa zovuta.



English : They include financial restrictions and a ban by the European Union on the export of crude oil, from which the Iranian economy receives 80% of its foreign income.

Nyanja : Amaphatikiza zochepetsa zachuma komanso kuletsa kwa bugwe la ku Ulaya kutumiza kunja mafuta osakonzedwa, pamene chuma cha dziko la Iran chimalandira 80% ya ndalama zake zakunja.



English : In its most recent monthly report, OPEC said exports of crude had fallen to their lowest level for two decades at 2.8 million barrels per day.

Nyanja : Mulipoti latsopano la OPEC, yasonyeza kuti mafuta womwe amatulutsidwa agwa kwambiri mudzaka makumi awiri apitawo pa zigubu mamiliyoni 2.8 patsiku.



English : The country´s supreme leader, Ayatollah Ali Khamenei, has described the dependency on oil as ¨a trap¨ dating from before Iran´s Islamic revolution in 1979 and from which the country should free itself.

Nyanja : Munthu wankulu kwambiri, Ayatollah Ali Khameni, wati kudalira mafuta ngati "nsampha" kuchokera nthawi imenekusintha kwa chisilamu kusadayambe mu 1997 komanso kuti dzikolo likhale pamtendere.



English : When the capsule gets to Earth and enters the atmosphere, at about 5am (eastern time), it is expected to put on quite a light show for folks in Northern California, Oregon, Nevada, and Utah.

Nyanja : Pamene kapisozi walowa mdziko ndikulowa mumlengalenga, pa nthawi ya 5 koloko m´mawa (nthawi yakum´mawa), pali chiyembekezero choti pazakhala chionetsero chochepa kwa anthu aku Mpoto kwa California, Oregon, Nevada komaso Utah.



English : The capsule will look much like a shooting star going across the sky.

Nyanja : Kapisozi adzawoneka kwambiri ngati nyenyezi yowombera kudutsa m´mulengalenga.



English : The capsule will be traveling at about 12.8 km or 8 miles per second, fast enough to go from San Francisco to Los Angeles in one minute.

Nyanja : Kapasulu aziyenda pa ntunda wa makilomita khumi ndi awiri kapena mamilosi asanu ndi atatu pa mphindi iliyonse, kutanthauza kuti atha kuchoka ku San Fansisco kupita ku Los Angeles mu mphindi makumi asanu ndi imodzi.



English : Stardust will set a new all-time record for being the fastest spacecraft to return to Earth, breaking the previous record set in May of 1969 during the return of the Apollo X command module.

Nyanja : Stardust apanga mbiri yatsopano ngati ndege yothamanga kwambiri kubwerera ku dziko, kuphwanya mbiri imene anapanga mu May wa 1969 nthawi ya kubwera kwa malamulo a Apollo X.



English : "It will move over the west coast of northern California and will light the sky from California through central Oregon and on through Nevada and Idaho and into Utah," Tom Duxbury, Stardust´s project manager said.

Nyanja : "Idzachoka kupita kumadzulo kwa kumpoto kwa Califonia ndipo idzawala mumlengalenga kuchokera ku California kudzera pakati pa Oregon ndikudzera ku Navada ndi Idaho, ndikulowa ku Utah; a Tom Duxbury, mkulu woyang´anira ntchito ya Stardust adatero.



English : Mr. Rudd´s decision to sign the Kyoto climate accord isolates the United States, which will now be the only developed nation not to ratify the agreement.

Nyanja : Chiganizo cha a Rudd kusayina za nyengo a Kyoto Accord zikuchotsa America, lomwe ndi dziko lokhalo lotukuka osayikidwamo mugwilizanuwu.



English : Australia´s former conservative government refused to ratify Kyoto, saying it would damage the economy with its heavy reliance on coal exports, while countries like India and China were not bound by emissions targets.

Nyanja : Boma lakale la Australia lakana kuvomereza Kyoto ponena kuti liwononga chuma kamba kodalira kwambiri kugulitsa malasha kunja, pomwe maiko ngati India ndi China sadakhuzidwe ndi mulingo wotulutsa mpweya.



English : It is the biggest acquisition in eBay´s history.

Nyanja : Uku nkugula kwa wakukulu zedi mu mbiri ya eBay.



English : The company hopes to diversify its profit sources and gain popularity in areas where Skype holds a strong position, such as China, Eastern Europe, and Brazil.

Nyanja : Kampani ikuyembekezeranso kusintha kumene kumachokera phindu lake ndikuti itchuke kumadera komwe Skype ili yamphamvu, monga China, Kum´mawa ku Ulaya, ndi ku Brazil.



English : Scientists have suspected Enceladus as geologically active and a possible source of Saturn´s icy E ring.

Nyanja : Azasayansi akuganiza kuti mwezi wa Saturn ngati zokhudzana ndi dziko zimagwira ntchito mwachilengedwe komanso chiyambi cha E ring ya Saturn.



English : Enceladus is the most reflective object in the solar system, reflecting about 90 percent of the sunlight that hits it.

Nyanja : Enceladus ndi chinthu chimene chimabweza kuwala kwambiri pazonse zadzuwa zili mumlengalenga, pafupifupi 90 pelesenti ya kuwala kwa dzuwa imene imayiwomba.



English : The game publisher Konami stated today in a Japanese newspaper that they will not be releasing the game Six Days in Fallujah.

Nyanja : Ofalitsa nkhani za masewera a Konami analankhula ku nyuzipapala ya ku Japan kuti atulutsa game yotchedwa Six Days ku Falluja..



English : The game is based on the Second Battle of Fallujah, a vicious battle between American and Iraqi forces.

Nyanja : Masewera ankhondo akanema opangidwa malingana ndi nkhondo yachiwiri yaku Fallujar, nkhondo yowopsa kwambiri yapakati pa asilikali aku America ndi Iraq.



English : The ACMA also found that despite the video being streamed on the Internet, Big Brother had not breached online content censorship laws as the media had not been stored on Big Brother´s website.

Nyanja : Bungwe la ACMA lidapezanso kuti ngakhale kanemayo adali kuwoneredwa pamatsamba a intaneti, Big Brother sidaphwanye malamulo azoletsa zapa intaneti chifukwa kanemayo sadasungidwe patsamba lawo intaneti la Big Brother.



English : The Broadcasting Services Act provides for the regulation of Internet content, however to be considered Internet content, it must physically reside on a server.

Nyanja : Lamulo lakaulutsidwe kazinthu la Broadcasting Services Act limathandiza kuwunikira zapa intaneti, komabe kuti ziwoneke momwe zilili zimayenera kudutsa pamikina akulu a kompuyuta otchedwa server.



English : The United States embassy located in Nairobi, Kenya has issued a warning that ¨extremists from Somalia¨ are planning to launch suicide bomb attacks in Kenya and Ethiopia.

Nyanja : Nyumba yawu kazembe ya United States imene ili ku Nairobi, Kenya yapereka chenjezo loti "anthu achiwembe ochokera ku Somalia" akukonza mabomba atinke nawo ku Kenya ndi Ethiopia.



English : The U.S. says it has received information from an undisclosed source that specifically mentions the use of suicide bombers to will blow up ¨prominent landmarks¨ in Ethiopia and Kenya.

Nyanja : Boma la U.S. lati lalandira zambiri kuchokera kwa amene sadafune kuzitchula mayina awo kukamba mwapaderadera zokhuza anthu omwe amaphulitsa mabomba atinkenawo amene akukaphulitsa "malo ofunikira" ku Ethiopia ndiku Kenya.



English : Long before The Daily Show and The Colbert Report, Heck and Johnson envisioned a publication that would parody the news—and news reporting—when they were students at UW in 1988.

Nyanja : Kalekale kulibe Daily Show ndi Colbert Report a Heck ndi a Johnstone anali ndi masomphenya olemba monyogodola nyuzi pamene anali ophunzila ku UW mchaka cha 1988.



[Day6]

English : Since its inception, The Onion has become a veritable news parody empire, with a print edition, a website that drew 5,000,000 unique visitors in the month of October, personal ads, a 24 hour news network, podcasts, and a recently launched world atlas called Our Dumb World.

Nyanja : Kuyambira pa chiyambi pake, The Onion yakhala nkhani zabwino zosililika, yokhala ndi potsindikizidwa, tsamba la pa intaneti lomwe lidafikiridwa ndi anthu 5,000,000 osiyanasiyana mu mwezi wa Okutobala, uthenga wamalonda waumwini, Nkhani zamaola 24, ma podcast, ndi mapu adziko lonse lapansi omwe akhazikitsidwa kumene otchedwa Our Dumb World.



English : Al Gore and General Tommy Franks casually rattle off their favorite headlines (Gore´s was when The Onion reported he and Tipper were having the best sex of their lives after his 2000 Electoral College defeat).

Nyanja : Al Gore ndi General Tommy Franks amatchula mobwerezabwereza mwachibwana mitu yomwe amakonda (A Gore ndi pamene Onion adanena kuti iye ndi Tipper amagonana bwino kwambiri m´moyo mwawo atagonjetsedwa pa 2000 Electoral College).



English : Many of their writers have gone on to wield great influence on Jon Stewart and Stephen Colbert´s news parody shows.

Nyanja : Olemba awo ambiri adapitiliza kupereka mangolomera kwa Jon Stewart ndi pulogalamu ya zazifanifani zankhani yomwe amapanga a Stephen Colbert.



English : The artistic event is also part of a campaign by the Bucharest City Hall that seeks to relaunch the image of the Romanian capital as a creative and colourful metropolis.

Nyanja : Mwambo wa anthu a zaluso m´magawo osiyanasiyana ndi gawo limodzi la kampeni ya Bucharest City Hall imene imafuna kukonzanso chithunzithunzi cha likulu la Romania ngati mzinda wopanga zinthu zaluso komanso wokongola.



English : The city will be the first in southeastern Europe to host CowParade, the world´s largest public art event, between June and August this year.

Nyanja : Mzinda umenewu ndi oyamba kum´mwera chakum´mawa ku Ulaya kuchititsa CowParade, chimodzi mwa ziwonetsero zaluso zazikulu padziko lonse, pakati pa mwezi wa Juni ndi ndi mwezi wa Ogasiti chaka chino.



English : Today´s announcement also extended the government´s commitment made in March of this year to fund extra carriages.

Nyanja : Zolengeza za lero zikuonjezerapo lonjezo lomwe boma lidapanga mu Malichi kuonjezerapo magaleta ena.



English : An additional 300 brings the total to 1,300 carriages to be acquired to relieve overcrowding.

Nyanja : Zowonjezera 300 zikwanitsa kuti pakhale magaleta 1,300 omwe akufunika kuti athetse kuchuluka kwa anthu.



English : Christopher Garcia, a spokesperson of the Los Angeles Police Department, said the suspected male offender is being investigated for trespassing rather than vandalism.

Nyanja : A Christopher Garcia, Mneneri wa apolisi waku Dipatiment ya Los Angeles, adati yemwe akumuganizira kuti ndi wolakwa akufufuzidwa pa chifukwa cholowa pamalo aeni ake wopanda chilolezo osati kuwononga zinthu ayi.



English : The sign was not physically damaged; the modification was done using black tarpaulins decorated with signs of peace and heart to alter the ¨O¨ to read lowercase ¨e¨.

Nyanja : Chizindikirocho sichidaphwanyidwe chidangosinthidwa zolemba; kusinthaku kudachitika pogwiritsa ntchito masaka akuda wokongoletsa ndi zizindikiro zamtendere ndi mtima kuti asinthe "O" kukhala zilembo zazing´ono "e".



English : Red tide is caused by a higher than normal concentration of Karenia brevis, a naturally-occurring single-celled marine organism.

Nyanja : Mafunde wofiyira amayambitsidwa ndi kukwera kwa Karenia brevis, zinthu zamoyo zomwe zimakhala ndi cell imodzi zokhala m´madzi.



English : Natural factors can intersect to produce ideal conditions, allowing this algae to increase in number dramatically.

Nyanja : Zachilengedwezi pamene zadutsana kuti zidzetse nyengo zabwino, zimene zimapangitsa kuti ndelezi zikhale zambiri.



English : The algae produces a neurotoxin that can disable nerves in both humans and fish.

Nyanja : Ndere zimatulutsa poyizoni otchedwa neurotoxin amene amatha kuononga mitsepha ya anthu ndi nsomba.



English : Fish often die because of the high concentrations of the toxin in the waters.

Nyanja : Kawirikawiri nsomba zikumafa kamba kochuluka poizoni m´madzi.



English : Humans can be affected by breathing affected water taken into the air by wind and waves.

Nyanja : Anthu atha kukhuzidwa ndikupuma mpweya womwe wabwera ndi madzi oyipa podzera mu mphepo ndi mafunde.



English : At its peak, Tropical Cyclone Gonu, named for a bag of palm leaves in the language of the Maldives, reached sustained winds of 240 kilometers an hour (149 miles per hour) .

Nyanja : Pampondachimera, mphepo ya nkuntho ya Tropical Cyclone Gonu, yomwe inatchulidwa chifukwa cha thumba la masamba amgwalagwala muchilankhulo chaku Maldives, idafika pa mphepo yowomba makilomita 240 pa ola limodzi (mamayilosi 149 pa ola).



English : By early today, winds were around 83 km/h, and it was expect to keep weakening.

Nyanja : Momwe kumacha nkuti mphepo yili pafupifupi makumi asanu ndi atatu ndi mphamvu zitatu ndipo tinayembekeza kuti zichepa.



English : On Wednesday, the United States´ National Basketball Association (NBA) suspended its professional basketball season due to concerns regarding COVID-19.

Nyanja : Lachitatu, bungwe la National Basketball Association (NBA) laku United States linayimitsa nyengo yake ya professional basketball chifukwa cha nkhawa zokhudza COVID-19.



English : The NBA´s decision followed a Utah Jazz player testing positive for the COVID-19 virus.

Nyanja : Ganizo la NBA lidabwera kamba ka osewera wa Utah Jazz yemwe adapezeka ndi ka chirombo ka COVID-19.



English : ¨Based on this fossil, that means the split is much earlier than has been anticipated by the molecular evidence.

Nyanja : Kutengera pa zomwe zapezeka zakalezi, zikutanthauza kuti kulekanitsaku kwafulumira kusiyana ndi m´mene zikuyembekezeredwa ndi umboni wa molecule.



English : That means everything has to be put back,¨ said researcher at the Rift Valley Research Service in Ethiopia and a co-author of the study, Berhane Asfaw.

Nyanja : "Zimenezi zikusonyeza kuti zonse zifunika kubwezedwa," Adatero katswiri wazakafukufuku ku Rift Valley Research Service ku Ethiopia pamodzi ndi wothandizana naye kulemba zakafukufukuyu a Berhane Asfaw.



English : Until now, AOL has been able to move and develop the IM market at its own pace, due to its widespread use within the United States.

Nyanja : Mpaka panopa, AOL yatha kusutha ndi kukhazikitsa msika wa IM pa malo ake, chifukwa choyigwiritsa ntchito kwambiri komweko ku United States.



English : With this arrangement in place, this freedom might end.

Nyanja : Ndi chikonzero chimenechi, ufulu umenewu utha kutha.



English : The number of users of the Yahoo! and Microsoft services combined will rival the number of AOL´s customers.

Nyanja : Nambala ya anthu womwe amagwilitsa Yahoo ndi Microsoft kuwaphatikiza angathe kulimbana ndi nambala ya makasitomala AOL.



English : The Northern Rock bank had been nationalised in 2008 following the revelation that the company had received emergency support from the UK Government.

Nyanja : Banki ya Northern Rock inasinthidwa mu 2008 kutsatira zomwe zadziwika kuti kampaniyo inalandirapo thandizo ladzidzidzi kuchokera ku Boma la UK.



English : Northern Rock had required support due to its exposure during the subprime mortgage crisis in 2007.

Nyanja : Northern Rock amafuna chithandizo chifukwa cha zomwe zinachitika nthawi yamavuto a ngongole ku subprime mu 2007.



[Day7]

English : Sir Richard Branson´s Virgin Group had a bid for the bank rejected prior to the bank's nationalisation.

Nyanja : Kampani ya Sir Richard Branson yotchedwa Virgin Group analemphera ndi lingaliro lake lofuna kugula bank koyambilira chifukwa cha mfundo zoteteza mabizinesi amudziko.



English : In 2010, while nationalised, the current high street bank Northern Rock plc was split from the 'bad bank', Northern Rock (Asset Management).

Nyanja : Mu chaka cha 2010 pamene bankiyi idakhala yaboma, panopa bankiyi ya Northern Rock plc yomwe ikupezeka mu mseu waukulu idagawidwa kuchokera ku 'banki yoyipa' , Northern Rock (Asset Management).



English : Virgin have only purchased the 'good bank' of Northern Rock, not the asset management company.

Nyanja : Virgin yangogula 'good bank' yaku North Rock osati kampani yoyendetsa chuma.



English : This is believed to be the fifth time in history that people have observed what turned out to be chemically confirmed martian material falling to Earth.

Nyanja : Anthu adawona zomwe zinali ngati mankhwala a Martian akugwa kuchokera kumwamba, kachinayi mu mbiri.



English : Out of the approximately 24,000 known meteorites to have fallen to Earth, only about 34 have been verified to be martian in origin.

Nyanja : Mwa ma meteorite okwana 24,000 omwe adagwera pa dziko lapansi, 34 okha ndi omwe adatsimikizidwa ndi ma martian.



English : Fifteen of these rocks are attributed to the meteorite shower last July.

Nyanja : Miyala khumi ndi isanu mwayina idagwa kuchokera kumwamba mu Julayi chaka chatha.



English : Some of the rocks, which are very rare on Earth, are being sold from US$11,000 to $22,500 per ounce, which is about ten times more than the cost of gold.

Nyanja : Miyala ina, yomwe ndi yosowa kwambiri pa Dziko lapansi, ikugulitsidwa pa mitengo ya US $ 11,000 mpaka $ 22,500 papaundi iliyonse, yomwe ili pafupifupi kakhumi kuposa mtengo wa golide.



English : Following the race, Keselowski remains the Drivers´ Championship leader with 2,250 points.

Nyanja : Kutsatira mpikisanowu, Keselowski wapitilira kukhala wopambana woyendetsa magalimoto ndi ma point 2,250.



English : Seven points behind, Johnson is second with 2,243.

Nyanja : Kusalira ndima point 7, Johnson adakhala wachiri ndi 2,243.



English : In third, Hamlin is twenty points behind, but five ahead of Bowyer. Kahne and Truex, Jr. are fifth and sixth respectively with 2,220 and 2,207 points.

Nyanja : Panambala 3, Hamlin ali kumbuyo ndi ma points okwana 20, koma ali patsogolo pa Bowyer ndi ma points okwana 5. Kahne ndi Truex, Jr. ali panambala 5 ndi 6 motsagana ndima point 2,220 komanso 2,207.



English : Stewart, Gordon, Kenseth, and Harvick round out the top-ten positions for the Drivers´ Championship with four races remaining in the season.

Nyanja : Stewart, Gordon, Kenseth, ndi Harvick adamalizira m´malo khumi apamwamba pa Mpikisano wa Woyendetsa magalimoto pamene kwatsala masewero anayi munyengo imeneyi.



English : The US Navy also said they were investigating the incident.

Nyanja : Asilikali ankhondo aku America ananenanso kuti akufufuza za nkhaniyi.



English : They also said in a statement, ¨The crew is currently working to determine the best method of safely extracting the ship¨.

Nyanja : Anatsindikanso kuti, Ogwira ntchito ali kalikiliki kuti apeze njira yabwino yopezera sitimayo.



English : An Avenger class mine countermeasures ship, the ship was on its way to Puerto Princesa in Palawan.

Nyanja : Sitima ya m´madzi yankhondo yochotsa mabomba yotchedwa Avenger, idali paulendo wake wopita ku Puerto Princesa ku Palawan.



English : It is assigned to the U.S. Navy's Seventh Fleet and based in Sasebo, Nagasaki in Japan.

Nyanja : Idapatsidwa kugulu la Seventh Fleet limene ndila U.S. Navy komanso imene ili ku Sasebo, Nagasaki ku Japan.



English : The Mumbai attackers arrived via boat on Novemeber 26, 2008, bringing with them grenades, automatic weapons and hit multiple targets including the crowded Chhatrapati Shivaji Terminus railway station and the famous Taj Mahal Hotel.

Nyanja : Anthu amene anachita za chipongwe ku Mumbai anafika pa ngalawa pa Novembara 26, 2008, atabweretsa mabomba, zida zotchera ndikuombera malo angapo kuphatikiza njanji ya Chhatrapati Shivaji Terminus kodzadza ndi gulu la anthu komanso malo wogona otchuka a Taj Mahal.



English : David Headley´s scouting and information gathering had helped to enable the operation by the 10 gunmen from the Pakistani militant group Laskhar-e-Taiba.

Nyanja : Kufufuza ndikusonkhanitsa mauthenga kwa David Headley zinathandizira zochitika za anthu 10 owopseza ndi amfuti ochokera gulu la Pakistani Laskhar-e-Taiba.



English : The attack put a huge strain on relations between India and Pakistan.

Nyanja : Zantopola zimapangitsa mpungwepungwe ndikusokonekera kwa ubale pakati pa Pakistani ndi India.



English : Accompanied by those officials, he assured Texas citizens that steps were being taken to protect the public´s safety.

Nyanja : Pamene adaperekezedwa ndi akuluakuluwo, adatsimikizira nzika zaku Texas kuti njira zoyenera zikutengedwa kuti anthu akhale otetezedwa.



English : Perry specifically said, ¨There are few places in the world better equipped to meet the challenge that is posed in this case.¨

Nyanja : Mwapadera a Perry adati, "Pali malo abwino ochepa omwe ali ndizoyenereza kuthana ndi vuto lilipoli."



English : The governor also stated, ¨Today, we learned that some school aged children have been identified as having had contact with the patient.¨

Nyanja : Bwanamkubwa adanenaso kuti, "Lero tamva ana amsinkhu wopita ku sukulu ena apezeka kuti adakomana ndi amene adali kudwala."



English : He went on to say, ¨This case is serious. Rest assured that our system is working as well as it should.¨

Nyanja : Adapitiriza kunenetsa kuti, "Izi ndizowopsa kwambiri. Tikakhale ndichikhulupiliro kuti makina athu akugwira bwino ntchito m´mene ayenera kugwilira."



English : If confirmed, the find completes Allen´s eight-year search for the Musashi.

Nyanja : Ngati zitsimikizika, zopezekazi zikumaliza kusakasaka kwa a Alleni kwa zaka zisanu ndi zinai kufuna za Musashi.



English : Following seabed mapping the wreck was found using an ROV.

Nyanja : Kutengera ndimomwe map a m´madzi, zotsallira za chowonongekacho chidapezeka pogwilitsa ntchito ROV.



English : One of the world´s richest people, Allen has reportedly invested much of his wealth in marine exploration and began his quest to find the Musashi out of a lifelong interest in the war.

Nyanja : M´modzi mwamakhumucha padziko lonse lapansi, a Allen akuti ayika chuma chawo chochuluka pa nkhani yazofufuza zamnyanja ndipo adayamba kufunafuna kuti apeze Musashi kamba ka chidwi chawo cha nthawi yaitali pa nkhondo imeneyi.



[Day8]

English : She gained critical acclaim during her time in Atlanta and was recognized for innovative urban education.

Nyanja : Adayamikiridwa zedi panthawi imene adali ku Atlanta komanso adadziwika ndi maphunziro apamwamba am´mizinda.



English : In 2009 she was awarded the title of National Superintendent of the Year.

Nyanja : Mchaka cha 2009 analandira ulemu wa National Superintendent wa Chakacho.



English : At the time of the award, Atlanta schools had seen a large improvement on test scores.

Nyanja : Pamene zimachitika za mphotoyo, masukulu aku Atlanta adawona kusintha kwambiri pa mulingo wa mayeso.



English : Shortly after, The Atlanta Journal-Constitution published a report showing problems with test results.

Nyanja : Atangomaliza kumene, Bungwe la Atlanta Journal-Constitution idasindikiza zotsatira zosonyeza zovuta zazotsatira zoyeserera.



English : The report showed test scores had increased implausibly fast, and alleged the school internally detected problems but didn´t act on the findings.

Nyanja : Lipoti lidaonetsa kuti mulingo wamayeso udakwera mosadziwika bwino mwachangu, ndipo akuti mavutowa adawawona pasukulupo koma sadachitepo kanthu pa zomwe adapezazo.



English : Evidence thereafter indicated test papers were tampered with Hall, along with 34 other education officials, was indicted in 2013.

Nyanja : Umboni kenako udasonyeza kuti, mapepala amayeso adasokonezedwa ndi Hall, pamodzi ndiakuluakulu 34 ena amaphunziro , adapezeka ndi mulandu mu chaka cha 2013.



English : The Irish government is stressing the urgency of parliamentary legislation to rectify the situation.

Nyanja : A boma la Ireland akutsindika kuti gawo lopanga malamulo achite machawi pokonza zithu.



English : ¨It is now important from both a public health and criminal justice perspective that the legislation be enacted as soon as possible¨, said a government spokesperson.

Nyanja : "Tsopano nkofunika kutengela pa umoyo wabwino komanso chilungamo kuti malamulo akhazikidwe posakhalitsa", anatelo m;neneri wa boma.



English : The Health Minister expressed concern both for the welfare of individuals taking advantage of the temporary legality of the substances involved, and for drug-related convictions handed down since the now-unconstitutional changes came into effect.

Nyanja : A Nduna a Zaumoyo adandaula za umoyo wa anthu amene atenga mwai wampata wochepa umene lamulo lapeleka pa mankhwala amene akukhuzidwa komanso zilango zokhuza mankhwala chifukwa choti malamulo anapezeka olakwika ndipo anasinthidwa.



English : Jarque was practicing during pre-season training at Coverciano in Italy earlier in the day. He was staying in the team hotel ahead of a match planned for Sunday against Bolonia.

Nyanja : Jarque amapanga masewera okonzekera pa Coverciano mu Italy m´mamawa kukacha. Amakhala mu malo wogona alendo ndi timu yonse yawosewera pokonzekera masewero oyikika pa Sabata ndi Bolonia.



English : He was staying in the team hotel ahead of a match planned for Sunday against Bolonia.

Nyanja : Ankakhala mumalo wogona a timu yawo pamene amayembekezera kusewera masewero awo la Sabata ndi timu ya Bolonia.



English : The bus was headed to Six Flags St. Louis in Missouri for the band to play to a sold-out crowd.

Nyanja : Basi idalunjika ku Six Flags St Louis ku Missouri kuti gulu liyimbe kwa khamu lomwe llokondwa lidali kudikilira.



English : At 1:15 a.m. Saturday, according to witnesses, the bus was going through a green light when the car made a turn in front of it.

Nyanja : Nthawi ya 1:15 m´mawa Loweluka, malingana ndi mboni, basi imadutsa maloboti ataonetsa magetsi amtundu obiriwira ndi pamene galimoto ina inadzakhota kutsogola kwa basiyi.



English : As of the night of August 9, the eye of Morakot was about seventy kilometres away from the Chinese province of Fujian.

Nyanja : Kufikila pa usiku wapa 9 Ogasiti, diso la Morakot linali motalikilana ndi dela la Fujian kwamakumi asanu ndi awiri.



English : The typhoon is estimated to be moving toward China at eleven kph.

Nyanja : Mkuntho ukuthamangira ku China pa liwiro la makilomita khumi ndi imodzi pa ola.



English : Passengers were given water as they waited in 90(F)-degree heat.

Nyanja : Apaulendo anapatsidwa madzi pamene amadikira kunali kutentha madigiri 90 (F).



English : Fire captain Scott Kouns said, ¨It was a hot day in the Santa Clara with temperatures in the 90s.

Nyanja : Mkulu oyang´anira ozimitsa moto a Scott Kouns adati, "lidali tsiku lotentha kwambiri ku Santa Clara ndi kutentha kwa m´ma 90.



English : Any length of time trapped on a roller coaster would be uncomfortable, to say the least, and it took at least an hour to get the first person off the ride.¨

Nyanja : Nthawi liyonse yomwe munthu ungapezeke kuti wakanilira mu basi yozungulira yitha kukhala yosasangalatsa mwina tinene choncho, ndipo zimatenga pafupifupi ola kuti munthu woyamba atuluke."



English : Schumacher who retired in 2006 after winning the Formula 1 championship seven times, was due to replace the injured Felipe Massa.

Nyanja : Schumacher amene adapuma ntchito mu chaka cha 2006 atapambana mu mpikisano wa Formula 1 kokwana ka 7, amafunika kuti alowe m´malo mwa Felipe Massa amene adavulala.



English : The Brazilian suffered a serious head injury after a crash during the 2009 Hungarian Grand Prix.

Nyanja : Munthu wa Brazil adavulala kwambiri m´mutu , patachitika ngozi muchaka cha 2009 pa Hungarian Grand Prix.



English : Massa is due to be out for at least the rest of the 2009 season.

Nyanja : Massa sapanga nao masewero kwa nyengo yonse ya yotsala ya 2009.



English : Arias tested positive for a mild case of the virus, Presidential Minister Rodrigo Arias said.

Nyanja : Nduna ya President a Rodrigo Arias adanena kuti Pulezidenti Arias adampeza ndi kachilombo ka virus koma kosadetsa nkhawa.



English : The president´s condition is stable, though he will be isolated at home for several days.

Nyanja : Mtsogoleri wa dziko lino akupeza bwino ngakhale kuti adzikhala m´malo aokha kaye.



English : ¨Apart from the fever and a sore throat, I feel well and in good shape to carry out my work by telecommuting.

Nyanja : Kupatula kutentha kwa thupi komanso zilonda za pakhosi, ndikumva bwino ndipo ndingakwanitse kugwira ntchito yanga pogwiritsa ntchito makina a intanet.



English : I expect to return to all my duties on Monday,¨ Arias said in a statement.

Nyanja : "Ndikuyembekeza kubwerera kuzintchito zanga Lolemba", Arias anatero polankhula kwake.



[Day9]

English : Felicia, once a Category 4 storm on the Saffir-Simpson Hurricane Scale, weakened to a tropical depression before dissipating Tuesday.

Nyanja : Felicia, nthawi ina adali mkuntho wa gulu la chinayi pa mulingo wa Saffir-Simpson Hurricane, adafooka ndi mphepo ina yotentha lisanafike lachiwiri idatheratu.



English : Its remnants produced showers across most of the islands, though as of yet, no damage or flooding has been reported.

Nyanja : Zotsalira zake zidabweretsa mawawa amvula pazilumba zochuluka, choncho pano, kulibe zomwe zawonongeka kapena madzi wosefukira.



English : The precipitation, reaching 6.34 inches at a gauge on Oahu, was described as ¨beneficial¨.

Nyanja : Mvula yofika mlingo wa mainchesi 6.34 ku Oahu, inanenedwa kuti inali "yopindulitsa".



English : Some of the rainfall was accompanied by thunderstorms and frequent lightning.

Nyanja : Mvula ina idali ndi mabingu komaso ziphaliwali pafupipafupi.



English : The Twin Otter had been trying to land at Kokoda yesterday as Airlines PNG Flight CG4684, but had aborted once already.

Nyanja : Twin Otter imayesera kuti itere ku Kokoda dzulo ngati Ndege PNG Flight CG4684, koma idalephera mkamodzi komwe.



English : About ten minutes before it was due to land from its second approach it disapeared.

Nyanja : Itangotsala mphindi khumi kuti yitere yidanyamukanso.



English : The crash site was located today and is so inaccessable that two policemen were dropped into the jungle in order to hike to the scene and seek survivors.

Nyanja : Malo omwe panachitikira ngozi apezeka lero koma ndiwosafikika motero apolisi awiri adachita kusiyidwa mtchire kuti ayende kukafika pamalopo ndikufuna ngati pali omwe adapulumuka.



English : The search had been hampered by the same bad weather that had caused the aborted landing.

Nyanja : Kusaka kunasokonekera ndi nyengo yoyipa imene inapangitsa kuti ndege isatere.



English : According to reports, an apartment on Macbeth Street exploded due to a gas leak.

Nyanja : Malingana ndizimene zanenedwa, nyumba ina mu msewu wa Macbeth idaphulika chifukwa chakutayika kwa gasi.



English : An official with the gas company was reporting to the scene after a neighbor called about a gas leak.

Nyanja : Wogwira ntchito pakampani ya gasi adapitaa kumaloko pamene adawuzidwa ndiwokhala naye pafupi kuti gasi akutayika.



English : When the official arrived, the apartment exploded.

Nyanja : Momwe wogwira ntchitoyo atafika , nyumbayo idaphulika.



English : No major injuries were reported, but at least five people on scene at the time of the explosion were treated for symptoms of shock.

Nyanja : Palibe amene wavulala kwambiri, koma pafupifupi anthu asanu omwe analipo pomwe kunaphulika anawathandiza chifukwa anali wozizimutsidwa.



English : No one was inside the apartment.

Nyanja : Munalibe aliyense m´nyumbamo.



English : At the time, nearly 100 residents were evacuated from the area.

Nyanja : Panthawiyo anthu pafupifupi zana limodzi adachotsedwa mderalo.



English : Both golf and rugby are set to return to the Olympic Games.

Nyanja : Masewero onse a Golf ndi rugby akonzeka kubwerera ku masewera a Olimpiki.



English : The International Olympic Committee voted to include the sports at its executive board meeting in Berlin today. Rugby, specifically rugby union, and golf were selected over five other sports to be considered to participate in the Olympics.

Nyanja : Komiti ya Masewero Yapadziko lonse inasankha lero kuphatikizila masewero kunsonkhano wake ku Berlin. Rugby, makamaka oimilira masewero a rugby ndi masewero a gofu anasankhidwa pa masewela asanu kuti ndi omwe azapikisane pa Masewelo Apadziko lonse.



English : Squash, karate and roller sports tried to get onto the Olympic program as well as baseball and softball, which were voted out of the Olympic Games in 2005.

Nyanja : Masewera a squash, karate, ndi maroller adati awaike nawo pa mndandanda wa masewera a Olympic kuonjezerapo baseball ndi softball pomwe muchaka cha 2005 adawachotsa.



English : The vote must still be ratified by the full IOC at it´s October meeting in Copenhagen.

Nyanja : Voti imeneyi iyenerabe kuti ikavomerezedwe ndi IOC yonse pa mkumano wawo wa mwezi wa Okutobala ku Copenhagen.



English : Not all were supportive of the inclusion of the women's ranks.

Nyanja : Siwonse amene adakondwera pakukwezedwa udindo kwa azimai.



English : 2004 Olympic silver medallist Amir Khan said, ¨Deep down I think women shouldn't fight. That's my opinion.¨

Nyanja : Amir Khan yemwe adalandira mendulo ya siliva mu chaka cha 2004 adati, "Kuchokera pansi pa mtima wanga ndikuganiza kuti azimayi asamamenyane. Amenewo ndi maganizo anga."



English : Despite his comments he said he will be supporting the British competitors at the 2012 Olympics being held in London.

Nyanja : Ngakhale adalankhulapo adati iye akakhala kumbuyo kwa wosewera aku Britain pa mpiksano wa Olimpiki yachaka cha 2012 yomwe ikuchitikira ku London.



English : The trial took place at Birmingham Crown Court and concluded on August 3.

Nyanja : Mlandu unachitikira ku bwalo la Birmingham Crown ndipo unatha pa 3 Ogasiti.



English : The presenter, who was arrested at the scene, denied the attack and claimed he used the pole to protect himself from bottles being thrown at him by up to thirty people.

Nyanja : Wolankhulayo, yemwe adamangidwa pamalopo, adatsutsa chiwembucho ndipo adati adagwiritsa ntchito mzati kuti adziteteze ku mabotolo omwe amaponyedwa kwa iye ndi anthu makumi atatu.



English : Blake was also convicted of attempting to pervert the course of justice.

Nyanja : Blake adamuweluza mlandu wofuna kuzemba chilungamo.



English : The judge told Blake it was ¨almost inevitable¨ he was going to be sent to jail.

Nyanja : Woweruza mlandu adauza a Blake kuti "ndizachidziwikiretu" kuti akagwira ukayidi ku ndende.



[Day10]

English : Dark energy is a completely invisible force that is constantly acting upon the universe.

Nyanja : Mphamvu zosadziwika bwino zolimbana ndi chilengedwe komanso zosaoneka ndimaso zomwe zimagwira ntchito mlengalenga nthawi zonse.



English : Its existence is known only because of its effects on the expansion of the universe.

Nyanja : Kudziwika kwake kuli choncho chifukwa chazotsatira chakukula kwa dziko lonse.



English : Scientists have discovered landforms littered across the moon´s surface called lobate scarps that have apparently resulted from the moon´s shrinking very slowly.

Nyanja : Akatswiri aza Sayansi apeza malo ena okhala pamwamba pa mwezi otchedwa ma labote scarp omwe adza kamba kakuchepa kwa mwezi pang´onopang´ono.



English : These scarps were found all over the moon and appear to be minimally weathered, indicating that the geologic events that created them were fairly recent.

Nyanja : Ma scarps amenewa anapezeka malo ambiri pa mwezipo ndipo anaoneka kuti sanakhuzidwe kwambiri ndi nyengo kutanthauza kuti anali atsopano.



English : This theory contradicts the claim that the moon is completely devoid of geologic activity.

Nyanja : Maganizowa akutsutsana ndi zimene zimanenedwa zoti mwezi sukhaliratu ndizochitika zachilengedwe.



English : The man allegedly drove a three-wheeled vehicle armed with explosives into a crowd.

Nyanja : Mzibamboyo adayendetsa galimoto yamatayala atatu yomwe yinali ndi mabomba.



English : The man suspected of detonating the bomb was detained, after sustaining injuries from the blast.

Nyanja : Bambo yemwe amamuganizira kuti adaphulitsa bomba anamumanga ngakhale anali atavulala.



English : His name is still unknown to authorities, although they do know he is a member of the Uighur ethnic group.

Nyanja : Adindo sakumudziwabe dzina la munthuyo, choncho akumudziwa kuti amachokera ku mtundu wa Uighur.



English : Nadia, born on September 17, 2007, by Cesarean section at a maternity clinic in Aleisk, Russia, weighed in at a massive 17 pounds 1 ounce.

Nyanja : Nadia amene anabadwa pa 17 Supitembala kudzela opaleshoni ku chipatala cha azimai ku Aleisk, Russia anali ndi sikelo kwambiri pa 17 pounds ndi ounce imodzi.



English : ¨We were all simply in shock,¨ the mother stated.

Nyanja : "Tonse tidali wodabwa", mayiyo adatero.



English : When asked what the father said, she answered ¨He couldn´t say a thing - he just stood there blinking.¨

Nyanja : Atamufunsa kuti bambo anati chani, adati "sadayakhepo kalikonse, adangoima ndikuphethira".



English : ¨It´s going to behave like water. It´s transparent just the way water is.

Nyanja : Idzachita makhalidwe ngati amadzi. Ndiyowoneka ngati m´mene madzi alili.



English : So if you were standing by the shoreline, you would be able to see down to whatever pebbles or gunk that was on the bottom.

Nyanja : Ngati mwayima m´mbali mwa gombe, mukhoza kuwona miyala yosalala ing´onoing´ono imene kapena zinthu zafungo zokhala ngati madzi zimene zili ku malo otsika.



English : As far as we know, there is only one planetary body that displays more dynamism than Titan, and its name is Earth,¨ added Stofan.

Nyanja : "Malingana ndi momwe tikudziwira, pali planet imodzi yokha imene inawonetsa mphamvu kuposa Titan, ndipo dzina lake ndi Dziko," anawonjezera Stofan.



English : The issue started on January 1st when dozens of local residents started complaining to the Obanazawa Post Office that they hadn´t received their traditional and regular New Year cards.

Nyanja : Vutoli lidayamba pa 1 Januware pamene anthu ambiri mdelari anadandaula ku Obanazawa Post Office kuti sanalandire ma card a Chaka Chatsopano monga mwa chizolowezi.



English : Yesterday, the post office released their apology to citizens and the media after discovering that the boy had hidden more than 600 postal documents, including 429 New Year postcards, which weren´t delivered to their intended recipients.

Nyanja : Dzulo, kampani ya zamtengatenga ndi mtokoma idapepesa kwa anthu komaso kwa atolankhani pomwe adadziwa kuti mnyamata adabisa zikalata zoposa 600 kuphatikizapo makalata 429 ofunirana zabwino za chaka chatsopano, amene sanaperekedwe kwa eni ake.



English : The unmanned lunar orbiter Chandrayaan-1 ejected its Moon Impact Probe (MIP), which hurtled across the surface of the Moon at 1.5 kilometres per second (3000 miles per hour), and successfully crash landed near the Moon´s south pole.

Nyanja : Chombo cha Chandrayaan-1 chomwe chidalibe woyendetsa popita kumwezi chidatulutsa Moon Impact Probe (MIP), chidadutsa pamwamba pa mwezi mothamanga kwambiri paliwiro lokwana makilomita 1.5 pa second (mamayilosi 3000 pa ola limodzi), ndipo idayima mogunda pansi bwinobwino pafupi ndi chakumwera kwa mwezi.



English : Besides carrying three important scientific instruments, the lunar probe also carried the image of the Indian national flag, painted on all sides.

Nyanja : Pambali ponyamula zinthu zitatu zofunika kwambiri pa nkhani zasayansi, kauniuni wamwezi amaonesa kuti pali chithunzi cha mbendera ya dziko la India, yokhala ndi utoto mbali zonse.



English : ¨Thanks for those who supported a convict like me,¨ Siriporn was quoted as saying at a press conference.

Nyanja : "Tithokoze kwa omwe anathandiza munthu wopezeka ndi mlandu ngati ine", a Siriporn akuti ananena izi pa nsonkhano wa atolankhani.



English : ¨Some may not agree but I don´t care.

Nyanja : Ena sangagwilizane nazo koma ndilibe nazo ntchito.



English : I am happy that there are people willing to support me.

Nyanja : Ndine wosangalala chifukwa cha anthu amene akufuna kundithandiza.



English : Since Pakistani independence from British rule in 1947, the Pakistani President has appointed ¨Political Agents¨ to govern FATA, who exercise near-complete autonomous control over the areas.

Nyanja : Kuchokela pamene dziko la PakistanI linapeza ufulu kuchokela ku dziko la Britain mu chaka cha 1947, atsogoleri a Pakistani akhala akusankha "oimilira a ndale" kuti azilamulira FATA, amene amakhala ndi mphanvu zambiri polamulira ma dera wa.



English : These agents are responsible for providing government and judicial services under Article 247 of the Pakistani Constitution.

Nyanja : Amkhala pakatiwa ntchito yawo ndiyochita zaboma ndi zamabwalo amilandu malingana ndi Lamulo nambala 247 lamumalamulo akulu adziko la Pakistani.



English : A hostel collapsed in Mecca, the holy city of Islam at about 10 o´clock this morning local time.

Nyanja : Ku Mecca nyumba yogonamo gulu la anthu inagwa, m´mzinda wopatulikawu wa Chisilamu nthawi yama 10 koloko lero m´mawa nthawi yakomweko.



English : The building housed a number of pilgrims who came to visit the holy city at the eve of hajj pilgrimage.

Nyanja : Nyumbayi idali ndi anthu ambiri woyenda chifukwa chachipembedzo omwe adabwera kuti akawone mzinda wopatulika madzulo a hajj.



[Day11]

English : The hostel´s guests were mostly citizens of the United Arab Emirates.

Nyanja : Ambiri mwa alendo anagona kumalo ogona gulu la alendo anali nzika zaku United Arab Emirates.



English : The death toll is at least 15, a figure which is expected to rise.

Nyanja : Chiwelengero cha anthu akufa chafika pa 15, chomwe chikuyembekezera kukweranso.



English : Leonov, also known as ¨cosmonaut No. 11¨, was part of the Soviet Union´s original team of cosmonauts.

Nyanja : Leonov, yomwenso yimatchedwa "Cosmonauts No. 11", yinali mbali ya Soviet Union mu timu ya cosmonauts.



English : On March 18, 1965, he performed the first manned extravehicular activity (EVA), or ¨spacewalk¨, remaining alone outside the spacecraft for just over twelve minutes.

Nyanja : Mu 18 Marichi, 1965 kadali koyamba kuyendesa extravehicular activity (EVA) kapena "spacewalk" adakhala yekha kunja kwa chombo cha m´mwamba kwa mphindi zopitilira khumi ndi ziwiri.



English : He received the ¨Hero of the Soviet Union¨, the Soviet Union´s highest honor, for his work.

Nyanja : Iwo adalandira ulemu wa "´Hero of the Soviet Union´" ulemu waukulu wa mgwirizano wa Soviet, chifukwa cha ntchito yawo.



English : Ten years later, he led the Soviet part of the Apollo–Soyuz mission symbolizing that the Space Race was over.

Nyanja : Patapita zaka khumi, adatsogolera mbali ya Soviet yotchedwa Apollo-Soyuz kumene kunali kutanthauza kuti Space Race idatha.



English : She said, ¨There is no intelligence to suggest that an attack is expected imminently.

Nyanja : Iye adati, "Palibe nzeru poganiza kuti chiwembu chitha kuchita nthawi iliyonse.



English : However, the reduction of the threat level to severe does not mean the overall threat has gone away.¨

Nyanja : Choncho, kachepedwe ka mulingo wa chiopsezo kufikira pa mulingo ochuluka sikukutanthauza kuti chiopsezo chonse chatha."



English : While authorities are unsure of the credibility of the threat, the Maryland Transportaion Authority made the closure with the urging of the FBI.

Nyanja : Ngakhale akuluakulu sakudzikwa kuti kuwopsezako mkwenikweni, a Maryland Transportation Authority adatseka kamba kolimbikitsidwa ndi FBI.



English : Dump trucks were used to block tube entrances and assistance of 80 police were on hand to direct motorists to detours.

Nyanja : Galimoto ya zinyalala yimatseka malowedwe atsewu ndipo apolisi 80 ndiwomwe anathandizira anthu komwe nseu udalunjika.



English : There were no heavy traffic delays reported on the beltway, the city´s alternate route.

Nyanja : kunalibe kuchedwa modetsa nkhawa kunaperekedwa ku beltway, nseu wina wa nzindawu.



English : Nigeria previously announced it planned to join the AfCFTA in the week leading up to the summit.

Nyanja : Nigeria idalengeza kuti idzalowa ku AFCFTA sabata ya msonkhano isadakwane.



English : AU trade and industry commissioner Albert Muchanga announced Benin was to join.

Nyanja : A Muchanga omwe ndimkulu woyang´anira za malonda ndi mafakitale ku AU adalengeza kuti Benin ilowa mu AU.



English : The commissioner said, ¨We haven´t yet agreed on rules of origin and tariff con[c]essions, but the framework we have is enough to start trading on July 1, 2020¨.

Nyanja : A Komishona adati, "Sitidagwirizanepo pa malamulo akomwe kukuchokera katundu ndiponso mitengo yamsonkho, koma ndondomeko imene ilipo ndiyokwanira kuti tiyambe malonda pa 1 Julayi 2020."



English : The station maintained its attitude, despite the loss of a gyroscope earlier in the space station mission, until the end of the spacewalk.

Nyanja : Siteshoniyo idasungabe malingaliro ake, ngakhale adataya gyroscope koyambirira kwa ulendo wawo pamalo osungira katundu mpaka kumapeto kwa ulendo wawo.



English : Chiao and Sharipov reported being a safe distance from the attitude adjustment thrusters.

Nyanja : Chiao ndi Sharipov adaoneka kuti adali mtunda wautali bwino kuchokera ku zochitika zosintha zama attitude thruster.



English : Russian ground control activated the jets and normal attitude of the station was regained.

Nyanja : Kuwongolera kwapansi ku Russia kunayendetsa ma jet ndipo maonekedwe abwinobwino amasiteshoni anabweleranso.



English : The case was prosecuted in Virginia because it is the home to the leading internet service provider AOL, the company who instigated the charges.

Nyanja : Mulandu umeneyu umayimbidwira ku Virginia kamba kakuti ndikomwe kampani yotsogola yopanga za intaneti ya AOL idachokera, kampani imene idayambitsa milanduyi.



English : This is the first time a conviction has been gained using the legislation enacted in 2003 to curb bulk e-mail, aka spam, from unsolicited distribution into users mailboxes.

Nyanja : Aka nkoyamba kuti chigamulo chipelekedwe pogwiritsa lamulo limene linakhazikitsidwa mu chaka cha 2003 kuletsa ma email ochuluka komanso a chisawawa omwe anthu ena amatumizila ena popanda kupemphedwa kutelo.



English : 21-year-old Jesus joined Manchester City last year in January 2017 from Brazilian club Palmeiras for a reported fee of £27 million.

Nyanja : Yesu wazaka 21 adapita ku Manchester City mu Januwale 2017 chaka chatha kuchokera ku timu yaku Brazil yotchedwa Palmeiras pamtengo wa 27 miliyoni paundi.



English : Since then, the Brazilian has featured in 53 matches for the club in all competitions and has scored 24 goals.

Nyanja : Kuchokela pamenepo, munthu wa ku Brazil anasewela masewero 53 a timu yake mumipikisano yonse ndipo anagoletsa zigoli 24.



English : Dr. Lee also expressed his concern about reports that children in Turkey have now become infected with the A(H5N1) avian influenza virus without becoming ill.

Nyanja : Dr. Lee anafotokozanso kudandaula kwawo pankhani zomwe zinamveka kuti ana ku dziko la Turkey tsopano ali ndi A (H5N1) virus ya fuluwenza koma osadwala.



English : Some studies suggest that the disease must become less lethal before it can cause a global epidemic, he noted.

Nyanja : Kafukufuku wina akuwonetsa kuti matendawa akuyenera kukhala osawopsa zisanafike muyezo oti mkukhala chiopsezo choyambitsa mliri wapadziko lonse, adatero.



English : There is concern that patients may continue to infect more people by going through their daily routines if the flu symptoms remain mild.

Nyanja : Pali nkhawa kuti odwala atha kupitiliza kufalitsa matenda kwa anthu ambiri pamene akugwira ntchito zawo zamasiku onse ngati zizindikiro zachimfine zikhalebe zochepa.



English : Leslie Aun, a spokesperson for the Komen Foundation, said the organization adopted a new rule that does not allow grants or funding to be awarded to organizations that are under legal investigation.

Nyanja : Mneneri wa bungwe la Komen Foundation, a Leslie Aun, ati bungwe lawo lavomereza lamulo latsopano loti lisamapereke thandizo lazachuma ku mabungwe omwe akufufuzidwa pa pankhani zophwanya malamulo.



[Day12]

English : Komen´s policy disqualified Planned Parenthood due to a pending investigation on how Planned Parenthood spends and reports its money that is being conducted by Representative Cliff Stearns.

Nyanja : Ndondomeko ya a Komeni idaletsa Planned Parenthood chifukwa panali kafukufuku amene amafufuza mmene a Planned Parenthood amagwiritsa ntchito ndikupanga report ya ndalama imene a Representative Cliff Stearns amapanga.



English : Stearns is investigating whether taxes are used to fund abortions through Planned Parenthood in his role as chairman of the Oversight and Investigations Subcommittee, which is under the umbrella of the House Energy and Commerce Committee.

Nyanja : A Stearns omwe ndi wapampando wa Komiti yaying´ono ya Oversight and Investigation, lomwe lili pansi pa Komiti ya House Energy ndi Commerce ati akufufuza kuti misonkho imathandiza kutaya mimba podzera ku Planned Parenthood.



English : Former Massachusetts governor Mitt Romney won the Florida Republican Party presidential primary election on Tuesday with over 46 percent of the vote.

Nyanja : Kazembe wakale waku Massachusetts a Mitt Romney anawina masankho oyambilira awu puresident wa Florida Republican Party Lachiwiri ndi mavoti opitilira 46 % amavoti onse.



English : Former U.S. Speaker of the House Newt Gingrich came in second with 32 percent.

Nyanja : Sipikala wa nyumba yamalamulo wakale Newt Gingrich waku U.S. anakhala wachiwiri ndi 32 %.



English : As a winner-takes-all state, Florida awarded all fifty of its delegates to Romney, pushing him ahead as the front-runner for the Republican Party nomination.

Nyanja : Monga boma lomwe limapeleka mphanvu zonse kwa wotsogola, Florida inapeleka nthumwi zake zonse makumi asanu kwa Romney, kumpangitsa iye kutsogola pachisankho cha mtsogoleri wa chipani chama Republican.



English : Organisers of the protest said about 100,000 people turned up in German cities such as Berlin, Cologne, Hamburg, and Hanover.

Nyanja : Akonzi a ziwonetsero zotsutsa amati pafupifupi anthu okwana 100,000 anafika m´mizinda ina yaku Germary ngati mizinda ya Berlin, Cologne, Hamburg, ndi Hanover.



English : In Berlin, police estimated 6,500 protestors.

Nyanja : Ku Berlin, apolisi amayelekeza pafupifupi anthu 6,500 aziwonetsero.



English : Protests also took place in Paris, Sofia in Bulgaria, Vilnius in Lithuania, Valetta in Malta, Tallinn in Estonia, and Edinburgh and Glasgow in Scotland.

Nyanja : Ziwonetsero zidalikonso ku Paris, Sofia mdziko la Bulgaria, Vilnius mdziko la Lithuania, Valetta mdziko la Malta, Tallinn mdziko la Estonia, ku Edinburgh komanso ku Glasgow mdziko la Scotland.



English : In London, about 200 people protested outside some major copyright holders´ offices.

Nyanja : Ku London, anthu pafupifupi zikwi ziwiri adachita zionetsero kunja kwa maofesi a akuluakulu a umwini.



English : Last month, there were major protests in Poland when that country signed ACTA, which has led to the Polish government deciding not to ratify the agreement, for now.

Nyanja : Mwezi watha, anthu amachita ziwonetselo zikuluzikulu ku Poland pamene dziko lidasayina ACTA, zimenezi zidapangitsa boma la Poland kuti lisavomereze mgwilizano pakadali pano.



English : Latvia and Slovakia have both delayed the process of joining ACTA.

Nyanja : Latvia ndi Slovakia onse achedwetsa ndondomeko yolowera nawo mu ACTA.



English : Animal Liberation and the Royal Society for the Prevention of Cruelty to Animals (RSPCA) are again calling for the mandatory installation of CCTV cameras in all Australian abattoirs.

Nyanja : Animal Liberation ndi Royal Society for the Prevention of Cruelty to Animals (RSPCS) akuyitanitsanso kwatsopano kukakamiza kuyika makamera a CCTV m´malo onse ophera nyama ku Australia.



English : RSPCA New South Wales chief inspector David O´Shannessy told the ABC that surveillance and inspections of abattoirs should be commonplace in Australia.

Nyanja : Mkulu woyang´anira RSPCA New South West a David O´Shannessy anauza a ABC kuti kuyang´anira ndikuyendera malo opherako nyama kukuyenera kukhala m´malo ambiri ku Australia.



English : ¨The CCTV would certainly send a strong signal to those people working with animals that their welfare is of the highest priority.¨

Nyanja : "Chachidziwikire CCTV izatumiza chizindikiro mwamphamvu kwa anthu omwe akusamalira nyama kuwadziwitsa kuti chisamaliro chawo ndichofunikira kwambiri."



English : The United States Geological Survey international earthquake map showed no earthquakes in Iceland in the week prior.

Nyanja : Mapu adziko lonse wowona zivomerezi anthambi ya United States Geological Survey sadawonetse zivomerezi ku Iceland mu sabata yam´mbuyo.



English : The Icelandic Meteorological Office also reported no earthquake activity in the Hekla area in the past 48 hours.

Nyanja : Ofesi yowona za nyengo yaku Iceland yati kudalibe chivomerezi ku dera la Hekla muma ola 48 apitawo.



English : The significant earthquake activity resulting in the phase change had took place on March 10 on the northeast side of the volcano´s summit caldera.

Nyanja : Chivomerezi chachikulu chomwe chachititsa kusintha mchigawo chidachitika pa 10 Marichi kumpoto cham´mawa pamwamba pamalo pamachitika volcano.



English : Dark clouds unrelated to any volcanic activity were reported at the base of the mountain.

Nyanja : Mitambo yakuda imene siyimagwilizana ndi volcano iliyonse inalengezedwa m´musi mwa phiri.



English : The clouds presented the potential for confusion as to whether an actual eruption had taken place.

Nyanja : Mitambo inapereka kuthekera kwa chisokonezo kuti mwina ngati kuphulika kwenikweni kunachitika.



English : The Luno had 120–160 cubic metres of fuel aboard when it broke down and high winds and waves pushed it into the breakwater.

Nyanja : Luna anali ndi mafuta okwana ma cubic mita 120-160 atanyamulidwa pamene inawonongeka ndipo mphepo yamkuntho ndi mafunde zimakankhila ku gombe.



English : Helicopters rescued the twelve crewmembers and the only injury was a broken nose.

Nyanja : Ma helokopitala anapulumutsa anthu onse khumi ndi awiri ogwira ntchito ndipo bala limene linalipo ndi kuthyoka mphuno.



English : The 100-metre ship was en route to pick up its usual fertiliser cargo and initially officials feared the vessel could spill a load.

Nyanja : Sitima ya m´madzi yotalika mamita 100 inali pa ulendo kukatenga katundu wake wamasiku onse Feteleza ndipo oyang´anira sitimayo poyamba anali ndi mantha kuti sitimayo itha kutaya katundu.



English : The proposed amendment already passed both houses in 2011.

Nyanja : Kusintha kumeneku kunadutsa kale mnyumba zonse ziwiri mu 2011.



English : A change was made this legislative session when the second sentence was deleted first by the House of Representatives and then was passed in a similar form by the Senate Monday.

Nyanja : Nthawi iyi yamsonkhano wazamalamulo kusintha kunapangidwa pamene poyamba chiganizo chachiwiri chidachotsedwa ndi Nyumba Yawoyimilira anthu ndipo chidavomerezedwa munjira yake yomweyo ndi Senate patsiku Lolemba.



English : The failure of the second sentence, which proposes to ban same-sex civil unions, could possibly open the door for civil unions in the future.

Nyanja : Kulephera kwa chigamulo chachiwiri, chomwe chimafuna kuletsa maukwati amuna kapena akazi okhaokha, kutha kutsegula khomo kuti anthu oterowa azikwatirana mtsogolo muno.



[Day13]

English : Following the process, HJR-3 will be reviewed again by the next elected legislature in either 2015 or 2016 to remain in process.

Nyanja : Motsatira njirazo, HJR-3 izawunikidwaso ndi nyumba yamalamulo yomwe isankhidwe mu 2015 kapena 2016 kuti zikhalebe mumndandanda.



English : Vautier´s achievements outside of directing include a hunger strike in 1973 against what he viewed as political censorship.

Nyanja : Zimene Vautier adakwanilitsa kunja kotsogolera zikuphatikiza kukana kudya mu chaka cha 1973 kutsutsana ndi m´mene amawonela ngati kuwunika ndale.



English : French law was changed. His activism went back to age 15 when he joined the French Resistance during World War II.

Nyanja : Lamulo la ku France lidasinthidwa. Zochitika zachilimbikitsozi adayamba ali ndizaka 15 pamene adalowa mu French Resistance nthawi ya Nkhondo ya Dziko Lapansi Yachiwiri.



English : He documented himself in a 1998 book.

Nyanja : Adazilemba yekha mu bukhu lomwe linasindikizidwa mu chaka cha 1998.



English : In the 1960s he headed back to newly-independent Algeria to teach film directing.

Nyanja : Muzaka zam´ma 1960 adabwelera ku Algeria watsopano odziimira payekha kukaphunzitsa kuwongolera kanema.



English : Japanese judoka Hitoshi Saito, winner of two Olympic gold medals, has died at the age of 54.

Nyanja : Nzika yaku Japan yosewera masewero a judo a Hitoshi Saito, wopambana mendulo ziwiri za golide ku Olympic, wamwalira ali ndi zaka zakubadwa 54.



English : The cause of death was announced as intrahepatic bile duct cancer.

Nyanja : Chomwe chidapangitsa imfa chidalengezedwa ngati khansa ya m´matumbo yotchedwa intrahepatic bileduct.



English : He died in Osaka on Tuesday.

Nyanja : Iwo anamwalira lachiwiri mu mzinda wa Osaka.



English : As well as a former Olympic and World champion, Saito was the All Japan Judo Federation training committee chairman at the time of his death.

Nyanja : Saito adali katswiri wakale wa Olimpiki ndi Wadziko Lonse Lapansi, adalinso wapampando wa komiti yowona zamaphunziro mu All Japan Judo Federation pa nthawi yomwe amamwalira.



English : At least 100 people had attended the party, in order to celebrate the first anniversary of a couple whose wedding was held last year.

Nyanja : Anthu osachepera 100 adakhala nawo pa phwando pokondwelera kuti banja lina latha chaka chimodzi chilowere m´banja.



English : A formal anniversary event was scheduled for a later date, officials said.

Nyanja : Zochitika zokhazikika zokumbukira mwambo azisintha tsiku mpaka tsiku lina, akuluakulu adatero.



English : The couple had married in Texas one year ago and came to Buffalo to celebrate with friends and relatives.

Nyanja : Anthuwa adamanga banja lawo ku Texas chaka chatha choncho adabwera ku Buffalo kukasangalala pamodzi ndi abwenzi komanso abale.



English : The 30-year-old husband, who was born in Buffalo, was one of the four killed in the shooting, but his wife was not hurt.

Nyanja : Mwamuna wa zaka makumi atatu, amene adabadwila ku Buffalo, adali m´modzi mwa anthu anayi omwe adaphedwa powombelana, koma akazi ake sanapwetekedwe.



English : Karno is a well-known but controversial English tutor who taught under Modern Education and King´s Glory who claimed to have 9,000 students at the peak of his career.

Nyanja : Karno ndi mphunzitsi wa chingelezi wodziwika bwino komanso wosokoneza amene anaphunzitsapo nthawi ya Modern Education and King´s Glory yemwe amati anali ndi ophunzira 9,000 pachimake pa ntchito yake.



English : In his notes he used words which some parents considered coarse, and he reportedly used profanity in class.

Nyanja : Muzolemba zake zoti ana azikawerenga amagwiritsa ntchito mawu wosakhala bwino malingana ndikuwona kwa makolo, ndipo akutiso amatukwana mkalasi.



English : Modern Education accused him of printing large advertisements on buses without authorisation and lying by saying that he was the chief English tutor.

Nyanja : Maphunziro Amakono adamudzuzula chifukwa chotsindikiza malembo akuluakulu mumabasi popanda chilolezo komaso ponama kuti anali mphunzitsi wamkulu wa Chingerezi.



English : He has also been accused previously of copyright infringement, but was not charged.

Nyanja : Anadzudzulidwaponso kuti anaphwanya lamulo potenga ntchito ya anthu ena popanda chilolezo koma sanaimbidwe mlandu.



English : A former student said that he ´used slang in class, taught dating skills in notes, and was just like the students´ friend.´

Nyanja : Ophunzira wakale adati 'ankagwiritsa ntchito katchulidwe ka mawu kosaloledwa mkalasi, adaphunzitsa luso lokhalira pa ubwenzi muzolemba, ndipo anali ngati nzawo wa ophunzira.'



English : During the last three decades, despite officially remaining a communist state, China has developed a market economy.

Nyanja : Mzaka makumi atatu zapitazo, ngakhale likadali kudziwika kuti boma la anthu wamba, China watukula chuma chamisika.



English : The first economic reforms were made under the leadership of Deng Xiaoping.

Nyanja : Kusintha koyamba kokhuza zachuma kudapangidwa muwutsogoleri wa a Deng Xiaoping.



English : Since then, China´s economic size has grown by 90 times.

Nyanja : Kuyambira pamenepo, chuma cha dziko la China chakula ndi maulendo okwana 90.



English : For the first time, last year China exported more cars than Germany and surpassed the United States as the biggest market for this industry.

Nyanja : Kwa nthawi yoyamba, chaka chatha China idagulitsa magalimoto ambiri kuposa dziko la Germany komanso kuposa dziko la United States ngati msika waukulu kwambiri.



English : China´s GDP could be larger than the United States within two decades.

Nyanja : GDP yaku China itha kukhala yayikulu kuposa yaku America muzaka makumi awiri.



English : Tropical Storm Danielle, fourth named storm of the 2010 Atlantic hurricane season, has formed in the eastern Atlantic Ocean.

Nyanja : Mvula yoononga ya Danielle, mvula yachinai yoteleyi munyengo ya mvula yoononga ya Atlantic mu chaka cha 2010, yayamba kum´mawa kwa nyanja ya mchere ya Atlantic.



English : The storm, located approximately 3,000 miles from Miami, Florida, has maximum sustained winds of 40 mph (64 kph).

Nyanja : Mphepo ya mkuntho, yomwe ili pamtunda wa mamayilosi 3,000 kuchokera ku Miami, Frorida, ili ndi kuthekera kobweretsa mphepo yamphamvu ya 40 mph (64 kph).



[Day14]

English : Scientists at the National Hurricane Center predict that Danielle will strengthen to a hurricane by Wednesday.

Nyanja : A sayansi a ku National Hurricane Central alosera kuti Danielle alimbikitsa mphepo yamkuntho pofika Lachinayi.



English : As the storm is far from landfall, it remains difficult to assess potential impact to the United States or Caribbean.

Nyanja : Pamene mphepo yamkuntho ili kutali ndi malo okugwa, zimakhalabe zovuta kuyesa kuthekera m´mene zingakhuzire ku United States kapena ku Caribbean.



English : Born in the Croatian capital, Zagreb, Bobek gained fame while playing for Partizan Belgrade.

Nyanja : Bobek yemwe adabadwira kulikulu la dziko la Croatia, Zagreb adatchuka pamene amasewera timu ya Partizan Belgrade.



English : He joined them in 1945 and stayed until 1958.

Nyanja : Adalowa nawo mu chaka cha 1945 mpaka 1958.



English : During his time with the team, he scored 403 goals in 468 appearances.

Nyanja : Kuyambira nthawi imene anali mu timuyi adagoletsa zigoli 403 pamene anasewera masewero 468.



English : No one else has ever made more appearances or scored more goals for the club than Bobek.

Nyanja : Palibe winanso amene adasewera masewero ambiri kapena adagoletsa zigoli zambiri za kilabu kuposa Bobek.



English : In 1995 he was voted the best player in Partizan´s history.

Nyanja : Mu 1995 adamuvotera wosewera wabwino mu mbiri ya Partizan.



English : The celebrations started with a special show by the world-renowned group Cirque du Soleil.

Nyanja : Zisangalalo zidayamba ndi chiwonetsero chapadera ndi gulu la Cirquel du SoleiL.



English : It was followed by the Istanbul State Symphony Orchestra, a Janissary band, and the singers Fatih Erkoç and Müslüm Gürses.

Nyanja : Kenako kunabwera Istanbul State Symphony Orchestra, gulu la Janissary, kenako oyimba ake Fatih Erkoç komanso Müslüm Gürses.



English : Then Whirling Dervishes took to the stage.

Nyanja : Kenako gulu la Whirling Dervish lidalowa m´bwalo.



English : Turkish diva Sezen Aksu performed with the Italian tenor Alessandro Safina and Greek singer Haris Alexiou.

Nyanja : Woyimba otchuka waku Turkey a Sezen Aksu adayimba ndi woyimba wa ku Italy a Alessandro Safina ndi woyimba waku Greece a Haris Alexiou.



English : To finish, Turkish dance group Fire of Anatolia performed the show ¨Troy¨.

Nyanja : Pomaliza, gulu lovina la Fire of Anatolia , la kuTurkey adavina mavinidwe a "Troy"



English : Peter Lenz, a 13-year-old motorcycle racer, has died after being involved in a crash at the Indianapolis Motor Speedway.

Nyanja : Peter Lenz, amene akhala zaka 13 kuthamangitsa njinga zamoto, amwalira atachita ngozi pa Indianapolis Motor Speedway.



English : While on his warm-up lap, Lenz fell off his bike, and was then struck by fellow racer Xavier Zayat.

Nyanja : Pamene adali kukonzekera kuti akhale pamzere, Lenz adagwa panjinga yake, ndipo adagundidwa ndi wopikisana nawo wina a Xavier Zayat.



English : He was immediately attended to by the on-track medical staff and transported to a local hospital where he later died.

Nyanja : Pompopompo adathangatidwa ndi achipatala amene adali panseu pompo komanso adapita naye ku chipatala chakonko kumene adakamwalira.



English : Zayat was unhurt in the accident.

Nyanja : Zayati sanavulale pa ngoziyi.



English : Regarding the global financial situation, Zapatero continued by saying that ¨the financial system is a part of the economy, a crucial part.

Nyanja : Malingana ndim´mene zachuma zikuyendera padziko lonse, a Zapatero adapitiliza kunena kuti "dongosolo la ndalama ndilo gawo la zachuma, mbali yofunika kwambiri.



English : We have a year-long financial crisis, which has had its most acute moment in the past two months, and I think now the financial markets are beginning to recover.¨

Nyanja : Tili ndimavuto azachuma chaka chonsechi, omwe adafika kovuta kwambiri miyezi iwiri yapitayo, ndipo ndikuganiza kuti pano misika ya zachuma ayamba kubwelera mwakale."



English : Last week, Naked News announced that it would dramatically increase its international language mandate to news reporting, with three new broadcasts.

Nyanja : Sabata yatha, Naked News idalengeza kuti iwonjezera zilankhulo zambiri zakunja pa zolengeza nkhani zake, ndimawayilesi awiri atsopano.



English : Already reporting in English and Japanese, the global organization is launching Spanish, Italian, and Korean-language programs, for television, the web, and mobile devices.

Nyanja : Tsopano Global organisation likulengeza mu chingerezi ndimuchi Japan komabe likuyambanso kulengeza mzilankhulo za chisipanishi, Chitaliana ndi Chikorea pa kanema, tsamba la intaneti ndi matelefoni am´manja.



English : ¨Luckily nothing happened to me, but I saw a macabre scene, as people tried to break windows in order to get out.

Nyanja : Mwamwayi palibe chimene chinandichitikira, koma ndinawona zochitika zoopsa, pamene anthu amayesetsa kuphwanya mawindo kuti atuluke.



English : People were hitting the panes with chairs, but the windows were unbreakable.

Nyanja : Anthu anali kalikiliki kumenya mawindo ndi mipando, kuti aswe mawindo komano sadasweke.



English : One of the panes finally broke, and they started to get out by the window,¨ said survivor Franciszek Kowal.

Nyanja : "Chimodzi mwadzotsekera chidatsekuka ndipo adayamba kutuluka", adatero m´modzi mwa wopulumuka a Franciszek Kowal.



English : Stars give off light and heat because of the energy made when hydrogen atoms are merged (or fused) together to form heavier elements.

Nyanja : Nyenyezi zimapereka kuwala komanso kutentha kamba ka mphamvu yomwe yimapangidwa pamene ma atom a mpweya wa hydrogen akaphatikizana (mwinaso kusakanikirana) limodzi kuti zithe kupanga zinthu zolemera zedi.



English : Scientists are working to create a reactor that can make energy in the same way.

Nyanja : A katswiri a sayansi ali kalikiliki kupanga reactor imene itha kupanga mphanvu munjira yomweyo.



[Day15]

English : This, however, is a very hard problem to solve and will take many years before we see useful fusion reactors built.

Nyanja : Izi choncho ndizovuta kwambiri kuti zikonzedwe ndipo zizatenga zaka zambiri tisanaone kupangidwa kwa ma fusion reactor.



English : The steel needle floats on top of the water because of surface tension.

Nyanja : Singano amayandama pamwamba pa madzi chifukwa cha surface tension.



English : Surface tension happens because the water molecules at the surface of the water are strongly attracted to each other more than they are to the air molecules above them.

Nyanja : Surface tension imapangidwa pamene ma molecule amadzi pamwamba amagwirana kwambiri kusiyana ndim´mene ndima molecule amulengalenga.



English : The water molecules make an invisible skin on the water's surface that allows things like the needle to float on top of the water.

Nyanja : Ma molecule amadzi amapanga khungu losawoneka pamwamba pamadzi zomwe zimapangisa zinthu zina kuyandama monga zingano.



English : The blade on a modern ice skate has a double edge with a concave hollow between them. The two edges allow for a better grasp of the ice, even when tilted.

Nyanja : Chipalawe cha ma skate amakono am´madzi owuma ali ndimbali ziwiri zakuthwa ndi m´bowo wopindikira mkati pakati pawo. Mbali ziwirizi zimapangisa kuti zizigwira bwino madzi oumawo, ngakhale zitapendekeka.



English : Because the bottom of the blade is slightly curved, as the blade tilts to one side or the other, the edge which is in contact with the ice also curves.

Nyanja : Chifukwa pansi pake pamakhala pokhota , pamene tsambalo lakhota , kumapetonso kwatsambalo komwe kwakhudzana ndi madzi wowuma kumakhota.



English : This causes the skater to turn. If the skates tilt to the right, the skater turns right, if the skates tilt to the left, the skater turns left.

Nyanja : Izi zimapangitsa wosewera pa madzi wowuma kupendama. Wosewerayu akatembenukira kumanja amakhotera kumanja ndipo akatembenukira kumanzere amakhotera kumanzere.



English : To return to their previous energy level, they must get rid of the extra energy they got from the light.

Nyanja : Kuti abwerere ku mphamvu zawo zakale, iwo akuyenera kuchotsa mphamvu yowonjezera yomwe anayipeza kuchokera ku kuwala.



English : They do this by emitting a tiny particle of light called a ¨photon¨.

Nyanja : Amachita izi potulutsa tizinthu tochepa totchedwa "Photon".



English : Scientists call this process ¨stimulated emission of radiation¨ because the atoms are stimulated by the bright light, causing the emission of a photon of light, and light is a type of radiation.

Nyanja : Akatswiri Asayansi amatchula njira imeneyi kuti "kulimbikitsa kutulutsa radiation" kamba kakuti ma atom amalimbikitsidwa ndi kuwala kochuluka, zimene zimachititsa kutulutsa ma photon owala, komanso kuwala ndi mtundu wa radiation.



English : The next picture shows the atoms emitting photons. Of course, in reality photons are a lot smaller than those in the picture.

Nyanja : Chithunzi chotsatila chikuonetsa ma atom akutulutsa ma photon. Inde, pachilungamo chake ma photon ndiochepa kwambiri kusiyana ndi zomwe zili pa chithunzi.



English : Photons are even smaller than the stuff that makes up atoms!

Nyanja : Ma photon ndi ocheperapo kuposa zinthu zomwe zimapanga ma atom.



English : After hundreds of hours of operation the filament in the bulb eventually burns out and the light bulb no longer works.

Nyanja : Ikagwira ntchito maola mazana, filamenti mubabulo imapsa ndipo babu siliyakaso.



English : The light bulb then needs replacing. It is necessary to be careful in replacing the light bulb.

Nyanja : Babu lowunikira lofunika kulisinthaso. Ndibwino kusamala pobwezeletsa babu.



English : First, the switch for the light fixture needs to be turned off or the cable disconnected.

Nyanja : Poyambilira, choyatsila cha magetsi chikuyenela kukhala chozimitsa kapena kuchotsa chingwe cha magetsi ku moto.



English : This is because electricity flowing into the socket where the metallic part of bulb sits can give you a severe electric shock if you touch the inside of the socket or the metal base of the bulb while it is still partly in the socket.

Nyanja : Kamba koti magetsi oyenda mu socket momwe muli mbali ya chitsulo ya babu lingakupangitseni kumva nyesi yamphamvu yochuluka pamene mwagwira mkati mwa socket kapena chitsulo chapansi pa babu pamene babulo linali mu socket.



English : The major organ of the circulatory system is the heart, which pumps the blood.

Nyanja : Mtima ndi chiwalo chachikulu cha momwe amayendera magazi, umene umapopa magazi.



English : Blood goes away from the heart in tubes called arteries and comes back to the heart in tubes called veins. The smallest tubes are called capillaries.

Nyanja : Magazi amayenda mutimathyubu totchedwa ma arteries ndipo amabwelera kupita ku mtima podzera mtimathyubu totchedwa ma veins. Timathyubu tochepa kwambiri timatchedwa ma capillaries.



English : A triceratops´ teeth would have been able to crush not only leaves but even very tough branches and roots.

Nyanja : Mano a triceratop adakakhala othekera kutafuna osati masamba basi komanso nthambi zokhwima zedi kuphatikizapo mizu.



English : Some scientists think Triceratops ate cycads, which are a type of plant that was common in the Cretaceous.

Nyanja : Akatswiri ena asayansi akuganiza kuti ma Triceratop adadya ma cycad, amene ndi mtundu wachomera chimene chimapezeka kwambiri munthawi yama Cretaceous.



English : These plants look like a small palm tree with a crown of sharp, spiky leaves.

Nyanja : Zomelazi zikuoneka ngati kamtengo ka kanjedza kakang´ono kamene kali ndi korona wa masamba akuthwa, onunkhira.



English : A Triceratops could have used its strong beak to strip off the leaves before eating the trunk.

Nyanja : Nyama ya maonekedwe a nyanga zitatu ikanatha kugwiritsa ntchito mulomo wake wamphamvu kugwetsa masamba asanadye mtengo wonse.



English : Other scientists argue that these plants are very poisonous so it is unlikely that any dinosaur ate them, even though today the sloth and other animals like the parrot (a descendant of the dinosaurs) can eat poisonous leaves or fruit.

Nyanja : Asayansi ena amati zomelazi ndizokupha ndipo ma dinosaur sakanadya ngakhale kuti pakali pano sloth ndi nyama zina monga mbalame ya Parrot (imene inachokela kuma dinosaur) amadya masamba ndi zipatso zokupha.



English : How would Io´s gravity pull on me? If you stood on the surface of Io, you would weigh less than you do on Earth.

Nyanja : Kodi mphamvu ya lo ingandikoke ine bwanji? Mukayima pansi pa lo, mumalemera mocheperako kusiyana ndi m´mene zimakhalira padziko lapansi.



English : A person who weighs 200 pounds (90kg) on Earth would weigh about 36 pounds (16kg) on Io. So the gravity, of course, pulls less on you.

Nyanja : Munthu amene akulemera mapaundi 200 (90kg) pa Dziko akhonza kulemera pafupifupi ma paundi 36 (16kg) pa lo.Moti mphamvu yokoka, ndiye kuti, imakoka pang´ono pa iwe.



[Day16]

English : The Sun doesn´t have a crust like the Earth that you can stand on. The whole Sun is made out of gases, fire, and plasma.

Nyanja : Dzuwa lilibe kutumphuka ngati Dziko lapansi lomwe mutha kuyimapo. Dzuwa lonse limapangidwa ndi mpweya, moto, ndi plasma.



English : The gas becomes thinner as you go farther from the center of the Sun.

Nyanja : Mpweyawo umayamba kuchepa ndithu pamene mukupita patali kuchokera pakatikati pa Dzuwalo.



English : The outer-part we see when we look at the Sun is called the photosphere, which means ¨ball of light¨.

Nyanja : Chimene timaona chakunja kwa Dzuwa chimatchedwa Photosphere, kumene kuli kutanthauza kuti "mpira wowala".



English : About three thousand years later, in 1610, Italian astronomer Galileo Galilei used a telescope to observe that Venus has phases, just as the moon does.

Nyanja : Pafupifupi zaka zikwi zitatu zitadutsa, muchaka cha 1610, katswiri waku Italy wowona zakuthambo, a Galileo Galilei adagwiritsa ntchito makina a telescope kuti awone ngati Venus ali ndi magawo ngati m´mene mwezi ulili.



English : Phases happen because only the side of Venus (or of the Moon) facing the Sun is lighted. The phases of Venus supported the theory of Copernicus that the planets go around the Sun.

Nyanja : Zigawo zimachitika kamba ka mbali imodzi imene ndiya Venus (komanso ya Mwezi) yoyang´anizana ndi Dzuwa ndi imene imawala. Zigawo za Venus zidathandiza maganizo a Copernicus akuti ma pulaneti amazungulira Dzuwa.



English : Then, a few years later in 1639, an English astronomer named Jeremiah Horrocks observed a transit of Venus.

Nyanja : Pambuyo pake, patadutsa zaka zochepa mu 1639, katswiri wamlengalenga wochokera ku Mangalande a Jeremiah Horrocks adawona njira yopita ku Venus.



English : England had experienced a long period of peace after the reconquest of the Danelaw.

Nyanja : England idakhala pamtendere kwa nthawi yayitali atagonjetsanso Danelaw.



English : However in 991 Ethelred was faced with a Viking fleet larger than any since Guthrum´s a century earlier.

Nyanja : Choncho mu 991 Ethelred adakomana ndi zombo za Viking zokula kuposa zonse kuyambira zaka zana limodzi zakumbuyo za Guthrum.



English : This fleet was led by Olaf Trygvasson, a Norwegian with ambitions to reclaim his country from Danish domination.

Nyanja : Ndipitiyu linatsogozedwa ndi a Olaf Trygvasson, aku Norway amene amafunanso kuchotsa dziko lao mu ulamulilo wa chi Danish.



English : After initial military setbacks, Ethelred was able to agree to terms with Olaf, who returned to Norway to try to gain his kingdom with mixed success.

Nyanja : Pachiyambi chifukwa chobwelera m´mbuyo paza nkhondo, Ethelred adavomera zomwe amafuna a Olaf, yemwe adabwelera ku Norway kukayesa kutenga ufumu wake zimene zinatheka koma movutirapo.



English : Hangeul is the only purposely invented alphabet in popular daily use. The alphabet was invented in 1444 during the reign of King Sejong (1418 – 1450).

Nyanja : Hangeul ndi zilembo zopangidwa zomwe zimagwiritsidwa tsiku ndi tsiku. Zilembozi zinakonzedwa mchaka cha 1444 pa nthawi ya ulamuliro wa mfumu Sejong (1418-1450).



English : King Sejong was the fourth king of the Joseon Dynasty and is one of the most highly regarded.

Nyanja : Mfumu Sejong idali mfumu yachinayi ya Dynasty ya Joseon ndipo ndi imodzi mwamafumu omwe imapatsidwa ulemu kwambiri.



English : He originally named the Hangeul alphabet Hunmin Jeongeum, which means ¨the correct sounds for the instruction of the people¨.

Nyanja : Pachiyambi adazipatsa dzina zilembo za Hangeul kuti ndi Hunmin Jeongeum, kumene kuli kusonyeza kuti "kamvekedwe kolondola kophunzitsira anthu".



English : There are many theories to how Sanskrit came into existence. One of them is about an Aryan migration from the west into India who brought their language with them.

Nyanja : Pali maganizo ambiri omwe amanena zamomwe Sanskrit adabwelera. Amodzi mwamaganizowo ndiwokhuza a Aryan womwe adachokera kumadzulo kupita ku India womwe adabweretsa chilankhulo chawo.



English : Sanskrit is an ancient language and is comparable to the Latin language spoken in Europe.

Nyanja : Sanskrit ndi chiyankhulo chakale ndipo chimafanizidwa ndi Chilatini chomwe chimayankhulidwa ku Ulaya.



English : The earliest known book in the world was written in Sanskrit. After the compilation of Upanishads, Sanskrit just faded due to hierarchy.

Nyanja : Buko lakale koposa onse linalembedwa mu chilankhulo cha Sanskrit. Pambuyo posonkhanista chilankhulo cha Upanishads, chi Sanskrit chidatha chifukwa cha kuchepa mphanvu.



English : Sanskrit is a very complex and rich language, which has served to be the source for many modern Indian languages, just like Latin is the source for European languages like French and Spanish.

Nyanja : Sanskrit ndi chiyankhulo chovuta komanso cholemela, chimene chakhala chiyambi cha zilankhulo zambiri zamakono zaku India, ngati m´mene ilili Latin ndi gwero la zilankhulo zaku Ulaya monga ngati France ndi Spain.



English : With the battle for France over, Germany began to get ready to invade the island of Britain.

Nyanja : Itatha nkhondo yolimbana ndi dziko la France, dziko la German lidayamba kukonzekera kuti likalande chilumba cha Britain.



English : Germany code-named the attack "Operation Sealion". Most of the British Army´s heavy weapons and supplies had been lost when it evacuated from Dunkirk, so the army was fairly weak.

Nyanja : Mchilankhulo chachinsisi chachi German lidatcha chiwembucho "operation sealion". Zambiri mwa zida za nkhondo zolemera za Britain komanso katundu wofunikira adasowa pamene adachoka ku Dunkirk, ndipo asilikali ankhondo adaliko ofooka.



English : But the Royal Navy was still much stronger than the German Navy ("Kriegsmarine") and could have destroyed any invasion fleet sent across the English Channel.

Nyanja : Royal Navy inali ili ndi mphavube zambiri kusiyana ndi German Navy ("Kriegsmarine") ndipo ikanatha kuononga sitima ya nkhondo ili yonse yomwe ikanatumizidwa kuti ikaononge podzera mu English Channel.



English : However, very few Royal Navy ships were based near the likely invasion routes as the admirals were afraid they would be sunk by German air attack.

Nyanja : Choncho, sitima za m´madzi zankhondo zochepa zedi za Royal Navy zomwe zinali kukhala pafupi ndimalo omwe panali njira zoti akanachitiridwa chiwembu, izi zinali choncho chifukwa woyang´anira amaopa kuti zingamizidwe m´madzi ndi asilikali ankhondo am´mwamba aku German.



English : Let´s start with an explanation about Italy´s plans. Italy was mainly the ¨little brother¨ of Germany and Japan.

Nyanja : Tiyeni tiyambe ndi kufotokozera zamalingaliro a dziko la Italy. Italy anali "pa uchimwene" ndi maiko a Germany ndi Japan.



English : It had a weaker army and a weaker navy, although they had just built four new ships right before the beginning of the war.

Nyanja : Anali ndi gulu lankhondo lapantunda komanso lankhondo lapamadzi lofooka, ngakhale anali atangopanga zombo zinayi zatsopano nkhondo isadayambe.



English : Italy´s main goals were African countries. To capture those countries, they would need to have a troop launching pad, so as troops could sail across the Mediterranean Sea and invade Africa.

Nyanja : Dziko la Italy zolinga zake zinali mayiko aku Africa. Kuti alande mayikowo, amafunika kukhala ndi malo okhazikika a asilikali, kuti asilikali azitha kuwoloka nyanja ya mediterranean ndi kulowa mu Africa.



English : For that, they had to get rid of British bases and ships in Egypt. Besides those actions, Italy´s battleships were not supposed to do anything else.

Nyanja : Pachifukwachi, amayenera kuchotsa malo asilikali aku Britain ndi masitima awo mu Egypt. Kupatula izi, masitima ankhondo aku Italy samayenera kupanga chinachilichonse.



[Day17]

English : Now for Japan. Japan was an island country, just like Britain.

Nyanja : Tsopano ngati Japan. Japan linali dziko lachilumba, monganso Britain.



English : Submarines are ships designed to travel underwater, and remain there for an extended amount of time.

Nyanja : Ma Submarine ndi sitima zomwe zidapangidwa kuti ziziyenda pansi pa madzi, ndikukhala mom´mo kwa nthawi yaitali.



English : Submarines were used in World War I and World War II. Back then they were very slow and had a very limited shooting range.

Nyanja : Ma sitima oyenda pansi pamadzi anamenya nkhondo Yoyamba ndi Yachiwiri yapa Dziko Lonse Lapansi. Panthawiyi anali oyenda pang´onopang´ono komanso ankaombera pafupi.



English : In the beginning of the war they mostly travelled on top of the sea, but as radar began developing and becoming more accurate the submarines were forced to go under water to avoid being seen.

Nyanja : Kumayambiliro ankhondo, anali kuyenda pa mwamba pamadzi koma kutabwela upangiri wa radar ma submarines anayamba kuyenda pansi pamadzi kuti asaonedwe.



English : German submarines were called U-Boats. The Germans were very good at navigating and operating their submarines.

Nyanja : Sitima za pansi pamadzi zaku German zinkatchedwa ma U-Boats. Ma German anapambana kwambiri poyendetsa sitimazi.



English : Because of their success with submarines, after the war Germans aren´t trusted to have many of them.

Nyanja : Chifukwa chakupambana kwawo pamodzi ndi oyenda pansi pamadzi, nkhondo itatha anthu aku German sakukhulupilidwa kuti ali nawo ambiri.



English : Yes! King Tutankhamun, sometimes referred to as ¨King Tut¨ or ¨The Boy King¨, is one of the most well known ancient Egyptian kings in modern times.

Nyanja : Zoona! Mfumu Tutankhamun nthawi zina amatchulidwa kuti "´Mfumu Tut´ kapena "" Mfumu ya Chinyamata´", ndi m´modzi mwa mafumu akale aku Egypt omwe akudziwika nthawi zino.



English : Interestingly, he was not considered to be very important in ancient times and was not recorded on most ancient king lists.

Nyanja : Chosangalatsa ndichakuti sadaganizire kuti adali wofunikira mu nthawi ya kale ndipo sadamulembe mu mndandanda wamafumu.



English : However, the discovery of his tomb in 1922 made him a celebrity. While many tombs of the past were robbed, this tomb was left virtually undisturbed.

Nyanja : Choncho, kupezeka kwa mandawo mu chaka cha 1922 zinapangitsa iye kukhala wotchuka. Pamene manda ochuluka akale anabedwa, manda amenewa anasiyidwa osawonongedwa.



English : Most of the items buried with Tutankhamun have been well preserved, including thousands of artefacts made from precious metals and rare stones.

Nyanja : Zinthu zambiri zomwe zinakwililidwa ndi Tutankhamun zidasungidwa bwino zedi, kuonjezerapo zinthu zikwizikwi zakale amagwilitsa ntchito zopangidwa ndi zitsulo za mtengo wapatali ndi miyala yosowa.



English : The invention of spoke wheels made Assyrian chariots lighter, faster, and better prepared to outrun soldiers and other chariots.

Nyanja : Kupangidwa kwa mateyala okhala ndi maspoko kudapangitsa magaleta ama Asiryan akhale opeouka, achangu ndiponso okhala okonzeka bwino kuthamangitsa asilikali ndi magaleta ena.



English : Arrows from their deadly crossbows could penetrate the armor of rival soldiers. About 1000 B.C., the Assyrians introduced the first cavalry.

Nyanja : Mauta awo owopsa wochokera pa maularo awo amatheka kulowa pachishango cha mdani, mu zaka za 1000 BC, anthu aku Syria anayambitsa kavali yoyamba.



English : A cavalry is an army that fights on horseback. The saddle had not yet been invented, so the Assyrian cavalry fought on the bare backs of their horses.

Nyanja : Gulu la ankhondo la asilikali lokwera pamahachi ndi limene limamenya nkhondo lili pahachi. Chishalo chinali chisanapangidwe, kotero asilikali apakavalo a ku Asirya anamenya nkhondo opanda kumbuyo kwa akavalo awo.



English : We know many Greek politicians, scientists, and artists. Possibly the most known person of this culture is Homer, the legendary blind poet, who composed two masterpieces of Greek literature: the poems Iliad and Odyssey.

Nyanja : Tikudziwa andale ambiri achi Greek, asayansi, ndi wopanga ntchito za manja. Mwina mwake munthu wodziwika kwambiri pachikhalidwe ndi Homer, wakhungu, wolemba ndakatulo yemwe analemba ziwiri zapamwamba kwambiri zachi Greek, ndakatulo Iliad ndi Odyssey.



English : Sophocles and Aristophanes are still popular playwrights and their plays are considered to be among the greatest works of world literature.

Nyanja : Sophocles ndi Aristophanes ndiakaswiri olemba zamasewero ndipo zolemba zawo zamasewero ndi zodziwika padziko lotse lapansi.



English : Another famous Greek is a mathematician Pythagoras, mostly known for his famous theorem about relations of the sides of right triangles.

Nyanja : Wina wotchuka ku Greece adali wamasamu Pythagoras, amene adadziwika ndi njira yake yofotokoza ubale wa mbali zofanana za triangle.



English : There are varying estimates for how many people speak Hindi. It is estimated to be between the second and fourth most commonly spoken language in the world.

Nyanja : Pali kuyerekezera kosiyanasiyana pa anthu omwe amalankhula Chihindi. Akuyerekeza kuti chihindi ndi chilankhulo chachiwiri kapena chachinayi chomwe chimalankhulidwa kwambiri padziko lapansi.



English : The number of native speakers varies depending on whether or not very closely related dialects are counted.

Nyanja : Chiwerengero cha mbadwa zomwe zimalankhula chilankhulo chobadwa nacho chimasintha kamba kakuti zilankhulo zapafupi zomwe ndizofananira zimawerengedwa nawo kapena ayi.



English : Estimates range from 340 million to 500 million speakers, and as many as 800 million people can understand the language.

Nyanja : Mulingo woyerekeza wa anthu omwe akulankhula chilankhulochi chikuyambira mamiliyoni 340 mpaka mamiliyoni 500 , komanso anthu pafupifupi mamiliyoni 800 amatha kuchimva chilankhulochi.



English : Hindi and Urdu are similar in vocabulary but different in script; in everyday conversations, speakers of both languages can usually understand each other.

Nyanja : Zilankhulo za Chihindi ndi Urdu ndi zofanana m´mawu koma zimasiyana ndi zilembo; muzokambirana za tsiku ndi tsiku, oyankhula a zilankhulo zonse ziwiri akhoza kumvana wina ndi nzake.



English : Around the 15th century, northern Estonia was under great cultural influence of Germany.

Nyanja : Mzaka za ma 1400 kumpoto kwa Estonia kunatengela kwambiri chikhalidwe cha ku Gelemani.



English : Some German monks wanted to bring God closer to the native people, so they invented the Estonian literal language.

Nyanja : Asembe ena ku Germany amafuna kubweretsa mulungu pafupi kwa anthu akuderaro, ndiye adayambitsa chiyakhulo chaku Estonia.



English : It was based on the German alphabet and one character ¨Õ/õ¨ was added.

Nyanja : Zinatengera pa zilembo za Chijeremani ndipo chilembo chimodzi "Õ/õ" chinawonjezeredwa.



English : As time passed, many words that were borrowed from German coalesced. This was the beginning of enlightenment.

Nyanja : Nthawi itadutsa, mawu ambiri amene adabwelekedwa kuchokera ku German adaphatikizidwa. Ichi chidali chiyambi cha kuwunikilidwa.



English : Traditionally, the heir to the throne would go straight into the military after finishing school.

Nyanja : Mwachikhalidwe, amene amayembekezela kukalowa ufumu ankalowa usilikali akangomaliza sukulu.



[Day18]

English : However, Charles went to university at Trinity College, Cambridge where he studied Anthropology and Archaeology, and later History, earning a 2:2 (a lower second class degree).

Nyanja : Choncho, Charles anapita ku sukulu ya ukachenjede ya Trinity College, ku Cambridge komwe adakaphunzira Anthropology ndi Archaeology, kenako History, ndikupeza 2:2 (Digiri kalasi yachiwiri yapansi).



English : Charles was the first member of the British Royal Family to be awarded a degree.

Nyanja : Charles anali membala oyamba wa Banja la chifumu ku Britain kuti apatsidwe digiri.



English : European Turkey (eastern Thrace or Rumelia in the Balkan peninsula) includes 3% of the country.

Nyanja : Turkey wa ku Ulaya (kum´mawa kwa Thrace kapena Rumelia ku Chisumbu cha Balkan) ndi magawo atatu pa zana la dzikolo.



English : The territory of Turkey is more than 1,600 kilometres (1,000 mi) long and 800 km (500 mi) wide, with a roughly rectangular shape.

Nyanja : Dera la Turkey ndilokula ndi makilomita 1600 mulitali (mamayilosi 1,000) ndipo makilomita 800 mulifupi (mamayilosi 500), ngati mokhala mwa ngodya zinayi ndithu.



English : Turkey´s area, including lakes, occupies 783,562 square kilometres (300,948 sq mi), of which 755,688 square kilometres (291,773 sq mi) are in south west Asia and 23,764 square kilometres (9,174 sq mi) in Europe.

Nyanja : Kukula kwa dziko la Turkey, kuyikaponso nyanja, ndilokwana masikweya makilomita 783,562 (300,948 sq mi), pamene masikweya makilomita 755,688 (291,773 sq mi) ndi akumwera chakumadzulo ku Asia komanso masikweya makilomita 23,764 (9,174 sq mi) ali ku Ulaya.



English : Turkey´s area makes it the world´s 37th-largest country, and is about the size of Metropolitan France and the United Kingdom combined.

Nyanja : Kukula kwamalo a dziko la Turkey likuipanga kukhala dziko lanambala 37 padziko lonse lapansi, ndipo ndilalikulu ngati mayiko awiri a Metropolitan France ndi United Kingdom kuwaphatikiza pamodzi.



English : Turkey is encircled by seas on three sides: the Aegean Sea to the west, the Black Sea to the north and the Mediterranean Sea to the south.

Nyanja : Zigawo zitatu za dziko la Turkey zidazunguliridwa ndi nyanja: Nyanja ya Aegean kumadzulo, Nyanja ya Black kumpoto komanso nyanja ya Mediterranean kumwera.



English : Luxembourg has a long history but its independence dates from 1839.

Nyanja : Dziko la Luxembourg lili ndi mbiri yakale kwambiri koma linadzipezela ufulu mchaka cha 1839.



English : Present-day parts of Belgium were part of Luxembourg in the past but became Belgian after the 1830s Belgian Revolution.

Nyanja : Kufikira lero magawo ena a Belgium anali gawo la Luxemburg m´mbuyomu koma adakhala Belgium patatha zaka za m´ma 1830 chifukwa cha Belgian Revolution.



English : Luxembourg has always tried to remain a neutral country but it was occupied in both World War I and World War II by Germany.

Nyanja : Luxembourg lakhala likuyesera kukhala dziko losalowelera zaeniake ngakhale lidatengedwapo ndi dziko la German munthawi zankhondo zonse ziwiri zadziko lapansi, Nkhondo Yoyamba komaso Nkhondo Yachiwiri.



English : In 1957 Luxembourg became a founding member of the organization which is today known as the European Union.

Nyanja : Mu chaka cha 1957 dziko la Luxembourg lidakhala membala woyambitsa nawo bungwe lomwe lero likutchedwa European Union.



English : The Drukgyal Dzong is a ruined fortress and Buddhist monastery in the upper part of the Paro District (in Phondey Village).

Nyanja : Drukgyal Dzong ndi linga lomwe lidaphwasulidwa komanso ndimalo omwe kuli manyumba ama Monk achipembedzo chama Buddha m´chigawo chakumtunda chaboma la Paro (kumudzi wotchedwa Phondey).



English : It is said that in 1649, Zhabdrung Ngawang Namgyel created the fortress to commemorate his victory against the Tibetan-Mongol forces.

Nyanja : Zikumveka kuti muchaka cha 1649, Zhabdrung Ngawang Namgyel adamanga linga la chitetezo ngati chikumbutso pakupambana kumene kunachitika pomwe ankamenyana ndi asilikali aku Tibetan-Mongol.



English : In 1951, a fire caused for only some of the relics of the Drukgyal Dzong to remain, such as the image of Zhabdrung Ngawang Namgyal.

Nyanja : Mchaka cha 1951 moto unapangitsa kuti zinthu zofunika zochepa zokha za Drukgyal Dzong zitsale monga chithunzi cha Zhabdrung Ngawang Namgyal.



English : After the fire, the fortress was preserved and protected, remaining to be one of Bhutan´s most sensational attractions.

Nyanja : Motowo utazima, linga linalimbitsidwa ndikutetezedwa, ndikukhalabe ngati chimodzi mwa zithu zopatsa chidwi ku Bhutan.



English : During the 18th century Cambodia found itself squeezed between two powerful neighbors, Thailand and Vietnam.

Nyanja : Munthawi yazaka zamazana 18 Cambodia idadzipeza kuti inafinyidwa pakati pa mayiko awiri ogundizana nawo amphamvu, Thailand ndi Vietnam.



English : The Thais invaded Cambodia several times in the 18th century and in 1772 they destroyed Phnom Phen.

Nyanja : Thailand idalowako kuka Cambodia kwa nthawi zambiri mzaka za m´mazana khumi ndi chisanu ndi chitatu ndipo mu chaka cha 1772 adawononga Phnom Phen.



English : In the last years of the 18th century the Vietnamese also invaded Cambodia.

Nyanja : Muzaka zomaliza zam´mazana khumi ndi mphambu zisanu ndi zitatu anthu aku Viyetinamu adalandaso dziko la Kambodya pa nkhondo.



English : Eighteen percent of Venezuelans are unemployed, and most of those who are employed work in the informal economy.

Nyanja : 18 % ya anthu aku Venezuela sali pantchito, ndipo ambiri amene ali pantchito amagwira yazachuma.



English : Two thirds of Venezuelans who work do so in the service sector, nearly a quarter work in industry and a fifth work in agriculture.

Nyanja : Mwa anthu awiri mwa atatu aku Venezuela omwe amagwira ntchito amagwira ku gawo lopereka chithandizo, pafupifupi kota limagwira mu gawo la zamalonda ndipo a chisanu amagwira mu zamalilidwe.



English : An important industry for Venezuelans is oil, where the country is a net exporter, even though only one percent work in the oil industry.

Nyanja : Makampani ofunikira ku Venezuela ndi amafuta, ndi dziko lomwe limagulitsa kwambiri mafuta kunja kusiyana ndiwolowa mdzikomo, ngakhale ndiwogwira ntchito wochepa kwambiri wokwana gawo limodzi womwe amagwira ntchito m´makampani amafuta.



English : Early in the nation´s independence, Singapore Botanic Gardens´ expertise helped to transform the island into a tropical Garden City.

Nyanja : Masiku amenewo atangolandila ufulu wozilamulira wokha ku Singapore, akatswiri azomera a Singapore Botanic Garden adathandiza chilumbachi kuti chikhale ngati mzinda wotchedwa Garden City.



English : In 1981, Vanda Miss Joaquim, an orchid hybrid, was chosen as the nation´s national flower.

Nyanja : Mu chaka cha 1981 Vanda Miss Joaquim, mtundu wa maluwa a orchid, lidasankhidwa kukhala duwa la dziko.



English : Every year around October nearly 1.5 million herbivores travel towards the southern plains, crossing the Mara River, from the northern hills for the rains.

Nyanja : Chaka chilichonse chamu Okutobala pafupifupi mamiliyoni 1.5 herbivores zimayenda kupita ku malo akumwera, kuwoloka mtsinje wa Mara, kuchokera ku mapiri a kumpoto.



English : And then back to the north through the west, once again crossing the Mara river, after the rains in around April.

Nyanja : Kenako kubwerera kumpoto kudzera kumadzulo, kuwolokanso mtsinje wa Mara, mvula itagwa mu Epulo.



[Day19]

English : The Serengeti region contains the Serengeti National Park, the Ngorongoro Conservation Area and Maswa Game Reserve in Tanzania and the Maasai Mara National Reserve in Kenya.

Nyanja : Dera la Serengeti, lili ndi malo nyama lotchedwa Serenget National Park, Ngorongoro Conservation Area ndi Maswa Game Reserve ku Tanzania komanso Maasai Mara National Reserver ku Kenya.



English : Learning to create interactive media requires conventional and traditional skills, as well as tools mastered in interactive classes (storyboarding, audio and video editing, story telling, etc.)

Nyanja : Kuphunzira kupanga ntchito zofalitsa mauthenga molumizikana pamafunika maluso akagwiridwe kabwino ka ntchito komanso a zachikhalidwe, komanso zida zodziwika bwino m´magulu olumikizirana (kuwerengera nkhani, kusintha kwamawu ndi makanema, kufotokozera nkhani, ndi zina zambiri).



English : Interactive design requires that you re-assess your assumptions about media production and learn to think in a non-linear ways.

Nyanja : Gawo lamaphunziro othandizira kuwunikiranso malingaliro anu pakufalitsa nkhani ndikuphunzira kuganiza njira zosiyana ndi zina.



English : Interactive design requires that components of a project connect to each other, but also make sense as a separate entity.

Nyanja : Momwe ntchito yidzagwilikire , zimayenera kuti zigawo zazojambula zantchito zizilumikizana, komanso zizitha kuima pazokha.



English : The disadvantage of zoom lenses is that the focal complexity and number of lens elements required to achieve a range of focal lengths is much greater than for prime lenses.

Nyanja : Kuyipa kwa ma Zoom lens ndiko kuti kuvuta kulunjika komaso kuchuluka kwa ma lens omwe amafunika kuti ulunjike mtunda wautali kusiyana ndi ma lens a prime.



English : This is becoming less of an issue as lens manufacturers achieve higher standards in lens production.

Nyanja : Vuto ili likunka lichepa popeza opanga ma lens amafikira mulingo wovomerezeka wapamwaba popanga ma lens.



English : This has allowed zoom lenses to produce pictures of a quality comparable to that achieved by lenses with fixed focal length.

Nyanja : Izi zapangitsa kuti ma lens okuza atole zithunzi zabwino kuyelekeza ndi ma lens osakuza zithunzi.



English : Another disadvantage of zoom lenses is that the maximum aperture (the speed) of the lens is usually lower.

Nyanja : Kuyipa kwina kwa ma lens ndikokuti nthawi imene kuwala kukufika (kuthamanga) pa lens kumakhala kochepa.



English : This makes inexpensive zoom lenses hard to use in low-light conditions without a flash.

Nyanja : Izi zimapangitsa ma len okulitsa zinthu wotsika mtengo akhale wovuta kugwiritsa ntchito m´malo momwe simowala kwambiri pamene simunagwiritse nyali yapakamera.



English : One of the most common problems when trying to convert a movie to DVD format is the overscan.

Nyanja : Vuto limodzi lodziwika kwambiri pofuna kusintha kanema kupita ku DVD ndikupanga scan mopitilira muyezo.



English : Most televisions are made in a way to please the general public.

Nyanja : Mawayilesi ambiri akanema amakonzedwa mnjira yoti azisangalatsa anthu onse.



English : For that reason, everything you see on the TV had the borders cut, top, bottom and sides.

Nyanja : Chifukwa chazimenezi, zilizonse mumaona pa TV zimakhala kuti zadulidwa mbali, pamwamba, pansi ndiponso m´mbali.



English : This is made to ensure that the image covers the whole screen. That is called overscan.

Nyanja : Izi zimachitika pofuna kuti chithunzi chikwanire galasi lonse. Izi zimatchedwa overscan.



English : Unfortunately, when you make a DVD, it´s borders will most likely be cut too, and if the video had subtitles too close to the bottom, they won´t be fully shown.

Nyanja : Tsoka ilo ukamapanga DVD, m´malire ake muzadulidwaso, ndipo ngati kanema anali ndi mau ena kufupi ndikupansi, mauwonso samaoneka.



English : The traditional medieval castle has long inspired the imagination, conjuring up images of jousts, banquets and Arthurian chivalry.

Nyanja : Nyumba zachifumu zakale zidalimbikitsa malingaliro, zithunzi za nkhondo, maphwando ndi chikhalidwe chachi Arthurian.



English : Even standing amidst thousand year-old ruins it is easy to bring to mind the sounds and smells of battles long gone, to almost hear the clatter of hooves on the cobbles and to smell the fear rising from the dungeon pits.

Nyanja : Mukaima pa nyumba zakale ndi zotheka kumamva fungo komanso maphokoso ankhondo omwe anachitika kalelo, mutha kumamva ndithu zipondelo ndi mantha pa maenje akhondowo.



English : But is our imagination based on reality? Why were castles built in the first place? How were they designed and built?

Nyanja : Koma kodi kuganiza kwathu kukuchokera pa zinthu zenizeni? Poyamba, Nchifukwa chiyani nyumba zachifumu zidamangidwa? Ndipo zidapangidwa ndikumangidwa bwanji?



English : Typical for the period, Kirby Muxloe Castle is more of a fortified house than a true castle.

Nyanja : Malingana ndi nthawi imeneyo, Kirby Muxloe Castle idali nyumba yotetezedwa kwambiri kuposa castle yeniyeni.



English : Its large glazed windows and thin walls would not have been able to resist a determined attack for long.

Nyanja : Mazenela akuluakulu komanso makoma owonda sadakalimba ndi nkhondo ya adani kwanthawi yaitali.



English : In the 1480s, when its construction was begun by Lord Hastings, the country was relatively peaceful and defense was only required against small bands of roving marauders.

Nyanja : Mu chaka cha 1480, pamene adayamba kumanga ndi Lord Hastings, dzikolo lidaliko la mtendere ndipo chitetezo chimafunikira mu timagulu toyendayenda tochepa ta upandu.



English : The balance of power was a system in which European nations sought to maintain the national sovereignty of all European states.

Nyanja : Kuona kuti dziko lililonse lili ndi mphamvu zofanana, ndiyo ndondomeko yomwe mayiko aku Ulaya adafuna kuti dziko lililonse likhale ndi umwini ndi ulamuliro wake m´mayiko onse aku Ulaya.



English : The concept was that all European nations had to seek to prevent one nation from becoming powerful, and thus national governments often changed their alliances in order to maintain the balance.

Nyanja : Chiganizo chinali choti mayiko aku Ulaya adayenera kuona kuti pasakhale dziko limodzi lamphamvu kuposa anzake, choncho maboma aku Ulayawo amasintha mgwirizano wawo kuti mayiko onse akhale ofanana.



English : The War of Spanish Succession marked the first war whose central issue was the balance of power.

Nyanja : Nkhondo yaku Spain yolimbirana utsogoleri idali yoyamba yomwe nkhani yayikulu inali kulimbirana mphamvu zautsogoleri.



English : This marked an important change, as European powers would no longer have the pretext of being religious wars. Thus, the Thirty Years´ War would be the last war to be labeled a religious war.

Nyanja : Ichi chinali chizindikiro cha kusintha kofunikira, pamene mphamvu za ku Ulaya sizikhalanso ndi chifukwa chokhalira ndi nkhondo za chipembedzo. Ndiye kuti, Nkhondo ya zaka Makumi Atatu izakhala nkhondo yomaliza kutchedwa ya chipembedzo.



English : The temple of Artemis at Ephesus was destroyed on July 21, 356 BCE in an act of arson committed by Herostratus.

Nyanja : Kachisi wa Artenis ku Ephesus anagumulidwa pa 21 Julayi mchaka cha 356 BCE pamene Herostratus analiotcha.



[Day20]

English : According to the story, his motivation was fame at any cost. The Ephesians, outraged, announced that Herostratus´ name never be recorded.

Nyanja : Potengera ndi nkhaniyi, chidwi chake chinali kutchuka munjira iliyonseyo.Anthu aku Aefeso, mokwiya, analengeza kuti dzina la Herostratus lisadzalembedwenso.



English : The Greek historian Strabo later noted the name, which is how we know today. The temple was destroyed on the same night that Alexander the Great was born.

Nyanja : Wodziwa za mbiri ya kale wa chi Greek a Strabo analemba dzina, nchifukwa chake lero tidziwa. Kachisi anaonongedwa tsiku lomwe Alexander anabadwa.



English : Alexander, as king, offered to pay to rebuild the temple, but his offer was denied. Later, after Alexander died, the temple was rebuilt in 323 BCE.

Nyanja : Mfumu Alexander anapempha kuti amangenso kachisiyo koma pempholo linakanidwa. Pambuyo pake atamwalira kachisiyo anamangidwanso mchaka cha 323 BCE.



English : Make sure your hand is as relaxed as possible while still hitting all the notes correctly - also try not to make much extraneous motion with your fingers.

Nyanja : Onetsetsani kuti dzanja lanu ndi lotakasuka momwe mukamenya manotsi onse moyenera -komanso onetsetsani kuti musayendetse kwambiri zala zanu.



English : This way, you will tire yourself out as little as possible. Remember there´s no need to hit the keys with a lot of force for extra volume like on the piano.

Nyanja : Pochita zimenezi, muzatopa pang´onopang´o. Kumbukirani sikoyenera kugunda mabatani mwamphamvu zochuluka powonjezera voliyumu ngati m´mene muchitira ndi piyano.



English : On the accordion, to get extra volume, you use the bellows with more pressure or speed.

Nyanja : Kuti mukweze volume pa accordion, umagwiritsa ntchito bellows ndi mphamvu ndithu kapena changu.



English : Mysticism is the pursuit of communion with, identity with, or conscious awareness of an ultimate reality, divinity, spiritual truth, or God.

Nyanja : Kukhala wa kuuzimu ndiko kusakasaka chigwilizano ndi, kudziwika ndi, komanso kuzindikira chowona chenicheni, umulungu, chowona chauzimu, komanso Mulungu.



English : The believer seeks a direct experience, intuition, or insight into divine reality/the deity or dieties.

Nyanja : Awo wokhulupilira akufuna umo zidachitikira, kudziwitsidwa, maganizidwe, azipembedzo/mulungu kapena timilungo.



English : Followers pursue certain ways of living, or practices that are intended to nurture those experiences.

Nyanja : Otsatira amatenga njira zina zakakhalidwe kapena kupanga zina zomwe zili ndi zolinga zopititsa patsogolo zomwe amazidziwa.



English : Mysticism can be distinguished from other forms of religious belief and worship by its emphasis on the direct personal experience of a unique state of consciousness, particularly those of a peaceful, insightful, blissful, or even ecstatic character.

Nyanja : Chikhulupiliro cha mysticism chimasiyana ndi zikhulupiliro zina ndi kupembeza chifukwa amakhazikika pa munthu kuzindikilitsidwa makamaka ntendere, kuunikilidwa, kuupeza ngakhale ku sangalala.



English : Sikhism is a religion from the Indian sub-continent. It originated in the Punjab region during the 15th century from a sectarian split within the Hindu tradition.

Nyanja : Chi Sikh ndi chipembedzo chochokera ku sub-continent ya India. Chidachokera mdera la Punjab muzaka zam´mazana 15 kugulu lomwe ligalukira miyambo ya chi Hindu.



English : Sikhs consider their faith to be a separate religion from Hinduism though they acknowledge its Hindu roots and traditions.

Nyanja : Ma Sikh amakhulupilira kuti chipembedzo chawo ndichosiyana ndi chi Hindu ngakhale amavomereza kuti chidachokera kuchipembedzo ndi miyambo ya ma Hindu.



English : Sikhs call their religion Gurmat, which is Punjabi for ¨way of the guru¨. The guru is a fundamental aspect of all Indian religions but in Sikhism has taken on an importance that forms the core of Sikh beliefs.

Nyanja : Anthu a chi Sikhs amatcha chipembedzo chawo Gurmat, chomwe ndi Chipunjabi cha "njira ya guru". Guru ndi gawo lofunikira pazipembedzo zonse zaku India koma mu Sikhism yatenga kufunikira komwe kumakhala maziko azikhulupiriro zachi Sikh.



English : The religion was founded in the 15th century by Guru Nanak (1469–1539). There followed in succession a further nine gurus.

Nyanja : Chipembedzochi chinayamba zaka mazana 15 ndi Guru Nanak (1469-1539). Patsogolo panabwera ma Guru ena okwana asanu ndi anayi motsatizana.



English : However, in June 1956, Krushchev´s promises were put to the test when riots in Poland, where workers were protesting against food shortages and wage cuts, turned into a general protest against Communism.

Nyanja : Komabe, mu Juni 1956, malonjezo a Krushchev anayesedwa pamene zipolowe ku Poland, komwe ogwira ntchito amatsutsa kusowa kwa chakudya komanso kudulidwa kwa malipiro, zinadzakhala ngati zotsutsa chi Communism.



English : Although in the end, Krushchev sent in tanks to restore order, he did give way to some economic demands and agreed to appoint the popular Wladyslaw Gomulka as the new prime minister.

Nyanja : Pamapeto pake ngakhale a Krushchev adatumiza akasinja kuti akakhazikitse bata, adavomereza zofuna zina zachuma ndiponso adavomera kusankha a Wladyslaw Gomulka omwe adali wotchuka kukhala Nduna yaikulu yatsopano.



English : The Indus Valley Civilization was a Bronze Age civilisation in the northwest Indian subcontinent encompassing most of modern-day Pakistan and some regions in northwest India and northeast Afghanistan.

Nyanja : Chitukuko chaku Indus Valley chinali chamunthawi ya chitukuko chamu nthawi ya Bronze Age chakumpoto kumadzulo kwa subcontinent ya India kuphatikizapo Pakistan watsopano komaso zigawo zina zakumpoto chakumadzulo kwa India ndi kumpoto chakum´mawa kwa Afghanistan.



English : The civilisation flourished in the basins of the Indus River wherefore it derives its name.

Nyanja : Chitukuko chidasefukira mphepete mwa mtsinje wa Indus kumene dzina la mtsinjeli lidachoka.



English : Although some scholars speculate that since the civilisation also existed in the basins of the now dried up Sarasvati River, it should be aptly called the Indus-Sarasvati Civilization, while some call it the Harappan Civilization after Harappa, the first of its sites to be excavated in the 1920s.

Nyanja : Pamene akatswiri ophunzira ena amaganiza kuti chitukuko chidaliponso muchithiba cha Mtsinje wa Sarasvati umene pano udawuma, chiyenera kutchulidwa kuti Indus-Sarasvati Civilization, pamene ena amati Harappan Civilization kamba ka Harappa, ndi malo oyamba kufukulidwa mzaka zam´ma 1920.



English : The militaristic nature of the Roman empire aided in the development of medical advances.

Nyanja : Nkhondo ya maufumu aku Rome inathandizira chitukuko cha zamankhwala.



English : Doctors began to be recruited by Emperor Augustus and even formed the first Roman Medical Corps for use in the aftermath of battles.

Nyanja : Madokotala adayamba kulembedwa ntchito ndi Mfumu Augustus ndipo adayambitsaso gulu loyamba la Roman Medical Corps lomwe limagwira ntchito pakachitika nkhondo kusamala ovulala.



English : Surgeons had knowledge of various sedatives including morphine from extracts of poppy seeds and scopolamine from herbane seeds.

Nyanja : Madotolo ochita opaleshoni anali ndi chidziwitso cha mankhwala kuphatikiza morphine kuchokera ku mbewu ya poppy ndi scopolamine kuchokera ku mbewu ya herbane.



English : They became proficient at amputation to save patients from gangrene as well as tourniquets and arterial clamps to stem blood flow.

Nyanja : Adali ndi aluso pochotsa ziwalo kuti apulumutse odwala kumatenda opha ziwalo komanso, zipangizo zoletsa kuyenda kwa magazi m´mitsempha ndi kuwuma kwa mitsempha kuletsa kuyenda kwa magazi.



English : Over multiple centuries, the Roman empire led to great gains in the field of medicine and formed much of the knowledge we know today.

Nyanja : Kwa zaka mazana ambiri, ufumu wa Roma udatsogolera kubweretsa zopata zochuluka mu gulu la zoona za mankhwala ndi kupanga kwakulu kwa kuzindikira komwe tikukudziwa lero.



English : Pureland origami is origami with the restriction that only one fold may be done at a time, more complex folds like reverse folds are not allowed, and all folds have straightforward locations.

Nyanja : Pureland origami ndi origami yoletsa kupinda kambiri pakamodzi, kupinda kovuta kwambiri kapena kupinda cham´mbuyo sikololedwa, ndipo zopinda zonse zili malo awo osavuta.



[Day21]

English : It was developed by John Smith in the 1970s to help inexperienced folders or those with limited motor skills.

Nyanja : Inapangidwa ndi John Smith muzaka zam´ma 1970 kuthandiza anthu amene luso lawo popinda mapepala mwaluso ndilochepa komanso amene sangakwanitse kuchita zambili ndi manja yao kapena olemala.



English : Children develop an awareness of race and racial stereotypes quite young and these racial stereotypes affect behavior.

Nyanja : Ana amakhala akudziwa za mtundu ndinso kusankhidwa kwamtundu akadali achichepere ndithu ndipo kusankhidwa kamba ka mtundu zimasokoneza khalidwe lawo.



English : For instance, children who identify with a racial minority that is stereotyped as not doing well in school tend to not do well in school once they learn about the stereotype associated with their race.

Nyanja : Mwachitsanzo, ana amene amadziwika ndi mtundu waung´ono omwe amayikidwa zizindikiro zokuti sachita bwino ku sukulu sachitadi bwino akazindikila kuti mtundu wawo umadziwika ndi kusachita bwino.



English : MySpace is the third most popular website used in the United States and has 54 million profiles currently.

Nyanja : MySpace ndi tsamba lapa intaneti lachitatu lotchuka kwambiri limene limagwiritsidwa ntchito ku dziko la United States ndipo ili ndi mbiri za anthu zokwana mamiliyoni 54 pakadali pano.



English : These websites have gotten a lot of attention, especially in the education setting.

Nyanja : Masamba apa intaneti apeza chikoka kwambiri makamaka pa maphunziro.



English : There are positive aspects to these websites, which include, being able to easily setup a class page which can include blogs, videos, photos, and other features.

Nyanja : Pali magawo abwino pamasamba a intanetiwa, monga ngati, kuthekera kukhazikitsa tsamba la kalasi lomwe lingaphatikizepo ma blogs, makanema, ndi zina zotero.



English : This page can easily be accessed by providing just one web address, which makes it easy to remember and easy to type in for students who may have trouble using the keyboard or with spelling.

Nyanja : Mutha kupeza tsambali mosavuta popereka keyala ya tsamba limodzi lokha basi, zomwe zimapangitsa kukumbukira mosavuta komanso kulemba mosavuta kwa ophunzira omwe angapeze mavuto kugwiritsa ntchito keyboard kapena ndi kulemba mawu.



English : It can be customized to make it easy to read and also with as much or little color as desired.

Nyanja : Mutha kupanga momwe mufunira kuti zikhale zosavuta kuwerenga komaso ndi utoto wambiri kapena wochepa malingana ndim´mene mufunira.



English : Attention Deficit Disorder ¨is a neurological syndrome whose classic defining triad of symptoms including impulsivity, distractibility, and hyperactivity or excess energy¨.

Nyanja : Matenda a attention deficit disorder "ndi matenda amitsempha odziwika kuti ali ndi zizindikiro zophatikiza kusowa chidwi, kusachita bwino, kapena kukhala ndi mphamvu zochulukirapo"



English : It is not a learning disability, it is a learning disorder; it ¨affects 3 to 5 percent of all children, perhaps as many as 2 million American children¨.

Nyanja : Siulumali wa kusaphunzira koma vuto la kuphunzira; "imakhudza ma pelesenti atatu mpakana asanu a ana onse, mwina ochuluka kukwanila mamiliyoni awiri a ana aku America".



English : Children with ADD have a hard time focusing on things like school work, but they can concentrate on things they enjoy doing like playing games or watching their favorite cartoons or writing sentences without punctuation.

Nyanja : Ana amene ali ndi vuto la ADD amavutika kulimbikila maphunziro koma amatha kulimbikila zinthu zimene amasangalala nazo bwinobwino monga masewela , kuonela ma kanema komanso kulemba ziganizo zopanda zopumira.



English : These children tend to get into a lot of trouble, because they ¨engage in risky behaviors, get into fights, and challenge authority¨ in order to stimulate their brain, since their brain can not be stimulated by normal methods.

Nyanja : Ana amenewa amakhala m´mavuto ambiri, chifukwa "amachita makhalidwe owopsa, ndewu, kutsutsana ndi ulamuliro" kuti alimbikitse ubongo wawo, popeza ubongo wawo sungalimbikitsidwe ndi njira zabwino.



English : ADD affects relationships with other peers because other children can not understand why they act the way that they do or why they spell they way they do or that their maturity level is different.

Nyanja : Vuto la ADD limakhuza maubale ndi anzake chifukwa ana ena sadziwa chifukwa chimene chimapangitsa khalidwe lawina kapena chifukwa chimene amapangila ma sipelo kapena kuti kukhwima kwake munzeru nkosiyana.



English : As the ability to obtain knowledge and to learn changed in such a way as mentioned above the base rate at which knowledge was obtained changed.

Nyanja : Monga m´mene kuthekera kodziwa zinthu ndi kuphunzira kunasithira m´mene anenera pamwambapa pamusi pamene chidziwitsochi chinatengedwa chinasinthidwa.



English : The approach to obtaining information was different. No longer did pressure reside within individual recall, but the ability to recall text became more of a focus.

Nyanja : Njira zopezera zinthu ndi zosiyana. Sukhalaso okakamizidwa kuti ukumbukire, koma kuthekera kokumbukira mawu kudakhala kolunjika pa mfundo.



English : In essence, the Renaissance made a significant change in the approach to learning and the dissemination of knowledge.

Nyanja : Zoona zake, Chiyambi chamaluso ndi maphunziro zidayambitsa kusintha kwakukulu munjira zophunzilira komaso kugawa nzeru.



English : Unlike other primates, hominids no longer use their hands in locomotion or bearing weight or swinging through the trees.

Nyanja : Kusiyana ndi anyani anzawo ena, ma hominid sagwilitsanso ntchito manja poyenda kapena potchinjiliza kulemela kwa nthupi lawo kapenanso poyenda m´mitengo.



English : The chimpanzee´s hand and foot are similar in size and length, reflecting the hand´s use for bearing weight in knuckle walking.

Nyanja : Dzanja ndi phazi la chimpanzee ndilofanana kukula ndi kutalika kwake, kuwonetsa magwiritsidwe ntchito a dzanja pothandiza kunyamula kwa thupi lake lolemera akamayenda.



English : The human hand is shorter than the foot, with straighter phalanges.

Nyanja : Dzanja la munthu ndilofupika kuposa phazi pamene ma phalanges ali owongoka.



English : Fossil hand bones two million to three million years old reveal this shift in specialization of the hand from locomotion to manipulation.

Nyanja : Zotsalira za mafupa am´manja azaka zokwana ma miliyoni awiri mpaka atatu zawonetsa kusintha kwa ukadaulo wa manja kuchokera posuntha poyendera mpaka kusinthidwa kwake.



English : Some people believe that experiencing many artificially induced lucid dreams often enough can be very exhausting.

Nyanja : Anthu ena amakhulupirira kuti kukhala ndi maloto ambiri ochita kuwapangisa mwadala nthawi zambiri zimakhala zotopesa.



English : The main reason for this phenomenon is the result of the lucid dreams expanding the length of time between REM states.

Nyanja : Ichichi ndichifukwa chomwe chozizwachi chinachitika kamba ka maloto wosadziwika bwino kupangitsa kuti nthawi yitalike pakati pa REM states.



English : With fewer REMs per night, this state in which you experience actual sleep and your body recovers becomes infrequent enough to become a problem.

Nyanja : Ndi ma REM ochepa usiku, munthawi yomwe mumagona kwenikweni ndipo thupi lanu limabwelera mwakale sizichitika kawirikawiri kuti mkukhala vuto.



English : This is just as exhausting as if you were to wake up every twenty or thirty minutes and watch TV.

Nyanja : Izi ndizotopetsa ngati uzidzuka kuwonera TV mphindi makumi awiri kapena mphindi makumi atatu aliwonse.



English : The effect is dependent on how often your brain attempts to lucidly dream per night.

Nyanja : Zotsatira zake zikutengera ndi m´mene ubongo wanu ukuyeselere kulota mwanzeru usiku uliwonse.



[Day22]

English : Things did not go well for the Italians in North Africa almost from the start. Within a week of Italy´s declaration of war on June 10, 1940, the British 11th Hussars had seized Fort Capuzzo in Libya.

Nyanja : Pafupifupi kuyambira pa chiyambi zinthu sizinayende bwino kwa anthu aku Italy ku Mpoto kwa Africa. Mkati mwa sabata yomwe Italy idalengeza za nkhondo pa 10 Juni 1940, ma Hussar 11 aku Britain adalanda Fort Cappuzo ku Libya.



English : In an ambush east of Bardia, the British captured the Italian Tenth Army´s Engineer-in-Chief, General Lastucci.

Nyanja : Paupandu anapanga ku m´mawa kwa Bardia, asilikakali aku Britain adagwira Injiniya, General Lastucci, wa gulu la nkhondo la ku Italy lotchedwa Tenth Army.



English : On June 28, Marshal Italo Balbo, the Governor-General of Libya and apparent heir to Mussolini, was killed by friendly fire while landing in Tobruk.

Nyanja : Pa 28 Juni, a Marshal Italo Balbo, Nkulu woyang´anira Libya komanso wotsatira pa utsogoleri kwa a Mussolini, anaphedwa ndi agulu lawo lomwe pamene amafika ku Tobruk.



English : The modern sport of fencing is played at many levels, from students learning at a university to professional and Olympic competition.

Nyanja : Masewero amakono a fencing amaseweledwa m´magulu osiyanasiyana kuyambila ana a sukulu kumasukulu aukachenjede kufukila anthu ogwira ntchito ya masewelo komanso mipikisano ku Olympic.



English : The sport is primarily played in a duel format, one fencer dueling another.

Nyanja : Masewerawa choyambilira amaseweredwa pamene pali awiriawiri, gulu lina awiri lotchinga kugulu linaso la awiri.



English : Golf is a game in which players use clubs to hit balls into holes.

Nyanja : Masewero a Golf ndi masewero amene wosewera ake amakhala ndi ndodo ngati chibonga imene amagwiritsa ntchito pomenya mipira kuti ilowe m´mabowo.



English : Eighteen holes are played during a regular round, with players usually starting on the first hole on the course and finishing on the eighteenth.

Nyanja : Ma bowo khumi ndi asanu ndi atatu amaseweledwa nthawi zambiri, osewela amayamba bowo loyamba nkumalizila bowo la khumi ndi asanu ndi atatu.



English : The player who takes the fewest strokes, or swings of the club, to complete the course wins.

Nyanja : Wosewera amene wakankha mpira mochepa kwambiri, kapena kusuntha kwa chibonga, kuti amalize ndi amene amapambana.



English : The game is played on grass, and the grass around the hole is mown shorter and called the green.

Nyanja : Masewelawa amaseweledwa pa kapinga ndipo kapinga wozungulira dzenje amaumweta kuti afupike ndipo amatchulidwa kuti wobiriwira.



English : Perhaps the most common type of tourism is what most people associate with traveling: Recreation tourism.

Nyanja : Mwina mwake mtundu wodziwika kwambiri wazokopa alendo ndi womwe anthu ambiri amawuganizira kuti umakhuza kuyenda: Maulendo wopuma.



English : This is when people go to a place that is very different from their regular day-to-day life to relax and have fun.

Nyanja : Apa ndi pamene anthu amapita kumalo omwe ndiwosiyana kwambiri ndi malo omwe amapita nthawi zonse kukapuma komaso kukasangalala.



English : Beaches, theme parks and camp grounds are often the most common places frequented by recreational tourists.

Nyanja : Magombe, malo osewelera ana ndi malo amisasa ya alendo ndi malo omwe amakondedwa ndi alendo okonda kusangalala.



English : If the objective of one's visit to a particular place is to get to know its history and culture then this type of tourism is known as cultural tourism.

Nyanja : Ngati cholinga chofika kudera linalake ndikudziŵa mbiri yake ndi chikhalidwe chawo, mtundu wazokopa alendo umenewu umatchedwa kuti wachikhalidwe.



English : Tourists may visit different landmarks of a particular country or they may simply opt to focus on just one area.

Nyanja : Alendo angathe kupita malo angapo osiyanasiyana otchuka kapena atha kusankhapo kuona dera limodzi lokha.



English : The Colonists, seeing this activity, had also called for reinforcements.

Nyanja : Atsamunda ataona zochitikazi anaitanitsa thandizo.



English : Troops reinforcing the forward positions included the 1st and 3rd New Hampshire regiments of 200 men, under Colonels John Stark and James Reed (both later became generals).

Nyanja : Asilikali omwe amapita chitsogolo adali a gulu Loyamba ndi Lachitatu, magulu asilikali okhala ndi asilikali 200 aku New Hampshire, omwe adatsogozedwa ndi ma Colonel John Stark ndi James Reed (ndipo onse adazakhala akulu ankhondo).



English : Stark´s men took positions along the fence on the north end of the Colonist´s position.

Nyanja : Amuna a gulu la Stark anayandikira pafupi ndi mpanda chakumpoto kwa Colonist.



English : When low tide opened a gap along the Mystic River along the northeast of the peninsula, they quickly extended the fence with a short stone wall to the north ending at the water´s edge on a small beach.

Nyanja : Pamene mafunde otsika adatsegula mpata m´mbalim´mbali mwamtsinje wa Mystic kumpoto chakum´mawa kwa ndomoyo, mwamsangamsanga adaonjezera kukulitsa mpanda ndikhoma lalifupi la miyala kumpoto kwake kumalizira mphepete mwamadzi pagombe laling´ono.



English : Gridley or Stark placed a stake about 100 feet (30 m) in front of the fence and ordered that no one fire until the regulars passed it.

Nyanja : A Gridley kapena a Stark adayika mtengo wamphamvu pafupi mafiti 100 (mamitala 30) kutsogolo kwa mpanda ndikulamula kuti aliyense asawombere mpaka anthuwa wamba atadutsa.



English : The American plan relied on launching coordinated attacks from three different directions.

Nyanja : Malingana ndi dongosolo la America, linadalira kuyambitsa kuombera mogwirizana kuchokera mbali zitatu zosiyana.



English : General John Cadwalder would launch a diversionary attack against the British garrison at Bordentown, in order to block off any reinforcements.

Nyanja : General John Cadwalder ankathila nkhondo asilikali Achingelezi ku Bordentown ndi cholinga chowasokoneza kuti kusafikae chithandizo cha nkhondo.



English : General James Ewing would take 700 militia across the river at Trenton Ferry, seize the bridge over the Assunpink Creek and prevent any enemy troops from escaping.

Nyanja : Mkulu wankhondo a James Ewing amatenga asilikali 700 kudutsa nawo pa mtsinje ku Trenton Ferry, kulanda mlatho umene umapita ku Assunpink Creek ndikulepheretsa asilikali agulu la adani kuti asathawe.



English : The main assault force of 2,400 men would cross the river nine miles north of Trenton, and then split into two groups, one under Greene and one under Sullivan, in order to launch a pre-dawn attack.

Nyanja : Gulu lalikulu lowopsa la nkhondo la amuna 2,400 limadutsa mtsinje mamayilosi asanu ndi anayi kumpoto kwa Trenton, kenako mkuligawa gulili kuti akhale awiri, lina mtsogoleri wake a Greene pomwe lina mtsogoleri wake a Sullivan, pokonzekera kuthira nkhondo yam´bandakucha.



English : With the change from the quarter to the half mile run, speed becomes of much less importance and endurance becomes an absolute necessity.

Nyanja : Ndikusintha kothamanga kuchokera pa kota mayilosi mpaka theka la mayilo, liwiro silimakhala lofunikira kwambiri koma kupilira ndiko kumafunika kwenikweni.



English : Of course a first-class half-miler, a man who can beat two minutes, must be possessed of a fair amount of speed, but endurance must be cultivated at all hazards.

Nyanja : Ndichoncho wothamanga wa gawo loyamba wothamanga theka la mayilosi, munthu yemwe amakwanitsa osapitilira mphindi ziwiri, ayenera kukhala ndi liwiro labwino, koma akhale wopilira kunyengo zonse.



[Day23]

English : Some cross country running during the winter, combined with gymnasium work for the upper part of the body, is the best preparation for the running season.

Nyanja : Masewera othamanga mitunda italiitali kasanu kuphatikizilapo masewero olimbitsa thupi amalimbitsa kuntunda kwathupi ndipo amakonzekeletsa bwino munthu nthawi yothamanga.



English : Proper nutritional practices alone cannot generate elite performances, but they can significantly affect young athletes´ overall wellness.

Nyanja : Kudya moyenela kokha sikungazetse kuchita masewelo mopambana koma zitha kuthandizila kwambiri osewela achinyamata kukhala angwiro.



English : Maintaining a healthy energy balance, practicing effective hydration habits, and understanding the various aspects of supplementation practices can help athletes improve their performance and increase their enjoyment of the sport.

Nyanja : Kuti ukhalebe wa thanzi lamphamvu, kugwiritsa ntchito makhalidwe abwino othanirana ndi ludzu, ndi kumvetsetsa magawo osiyanasiyana ophatikizirapo zochita akhoza kuthandiza othamanga kusintha kukonza magwiridwe awo ndi kuonjezera kusangalatsidwa kwawo ndi masewera.



English : Middle distance running is a relatively inexpensive sport; however, there are many misconceptions regarding the few pieces of equipment required to participate.

Nyanja : Kuthamanga kwa ntunda wofupikilapo ndi masewela otsika ntengo; komabe pali kunsanvetsa pa zida zofunikila kuti munthu achitile masewerawa.



English : Products can be purchased as needed, but most will have little or no real impact on performance.

Nyanja : Zogulitsa zikhoza kugulidwa ngati zingafunike, koma zambiri zidzakhudza pang´ono kapena osakhudza kwenikweni magwiridwe a ntchito.



English : Athletes may feel that they prefer a product even when it provides no real benefits.

Nyanja : Ochita masewera olimbitsa thupi amatha kumamva kufuna chinthu ngakhale chinthucho sichipindulitsa kwenikweni.



English : The atom can be considered to be one of the fundamental building blocks of all matter.

Nyanja : Atom itha kutengedwa ngati chinthu chimodzi chofunikira kuti china chilichonse chipangidwe.



English : Its a very complex entity which consists, according to a simplified Bohr model, of a central nucleus orbited by electrons, somewhat similar to planets orbiting the sun - see Figure 1.1.

Nyanja : Ndichigawo china chovuta zedi, zomwe kutengera ndi maganizidwe a Bohr, pakati pa nucleus mozungulilidwa ndima electron, zimafanana ndima planet kuzungulira dzuwa- wonani chithuzi 1.1.



English : The nucleus consists of two particles - neutrons and protons.

Nyanja : Nucleus ili ndizinthu ziwiri - ma neutron ndi ma proton.



English : Protons have a positive electric charge while neutrons have no charge. The electrons have a negative electric charge.

Nyanja : Maproton ali ndi mphamvu ya magetsi ambiri pomwe ma neutron alibe mphamvu ya magetsi. Ma electron ali ndi vuto la magetsi.



English : To Check the victim, you must first survey the scene to ensure your safety.

Nyanja : Kuti muone wovulala mukuyenera kuona kaye pamalopo.



English : You need to notice the victim´s position as you approach him or her and any automatic red flags.

Nyanja : Muyenera kuzindikira momwe wofuna thandizo m´mene wakhalira pamene mukumuyandikira komaso ngati pali zina zosokoneza zachikhalire.



English : If you get hurt trying to help, you may only serve to make matters worse.

Nyanja : Ngati mwapwetekedwa pamene mukuthandiza, mutha kuthandiza kuti zinthu zikhale zosokonekera kwambiri.



English : The study found that depression, fear and catastrophising mediated the relationship between pain and disability in lower back pain sufferers.

Nyanja : Kafukufukuyu anapeza kuti kukhumudwa, mantha komanso kuganizila mavuto kumathandizila ubale pakati pa ululu ndi ulumali kwa anthu amakhala ndi vuto la ululu kumusi kwa nsana.



English : Only the effects of catastrophizing, not depression and fear was conditional of regular weekly structured PA sessions.

Nyanja : Zokhazokha zokhuza zotsatira zakuwonongedwa, osati kukhumudwa ndi mantha zinali zovomerezeka pa zochitika za sabata la maphunziro a PA.



English : Those participating in regular activity required more support in terms of negative perception of pain distinguishing the differences of chronic pain and discomfort feel from normal physical movement.

Nyanja : Omwe amatenga nawo mbali nzochitika zamasiku onse ayenera kuthandizidwa moyenera makamaka pa nkhani yamaganizilidwe olakwika pa ululu posiyanisa kumva ululu kwamasiku onse ndi kusapeza bwino kamba koyenda.



English : Vision, or the ability to see depends on visual system sensory organs or eyes.

Nyanja : Masomphenya, ndi kuthekera kuwona kumadalira ziwalo zamaganizidwe ndiponso maso.



English : There are many different constructions of eyes, ranging in complexity depending on the requirements of the organism.

Nyanja : Pali mawonekedwe amaso osiyanasiyana, maonekedwe osiyana potengera ndi zofunikira za thupi.



English : The different constructions have different capabilities, are sensitive to different wave-lengths and have differing degrees of acuity, also they require different processing to make sense of the input and different numbers to work optimally.

Nyanja : Zomangamanga zosiyanasiyanazi zili ndikuthekera kosiyana ndithu, kuthekera kuzindikira kutalika kwa mafunde osiyasiyana ndipo zimakhala ndi macuity osiyanasiyana, zimafunikanso kukonza kosiyanasiyana kuti zolowa zimveka ndi manambala osiyanasiyana kuti agwire ntchito moyenera.



English : A population is the collection of organisms of a particular species within a given geographic area.

Nyanja : Chiwerengero cha zinthu ndiye kuti kutolela zamoyo zamtundu umodzi kudera linalake lomwe mwapatsidwa.



English : When all individuals in a population are identical with regard to a particular phenotypic trait they are known as monomorphic.

Nyanja : Pamene zinthu zonse pagulu mzofanana malingana ndi mtundu wake zimadziwika ndi dzina loti monomorphic.



English : When the individuals show several variants of a particular trait they are polymorphic.

Nyanja : Pamene anthu asonyeza mitundu ingapo ya makhalidwe ndiye kuti ali polymorphic.



English : Army ant colonies march and nest in different phases as well.

Nyanja : Nyerere zotchedwa zankhondo zimayenda ndikupanga chisa mzigawo zoyisanasiyanaso.



English : In the nomadic phase, army ants march at night and stop to camp during the day.

Nyanja : Mkatikati mwa maulendo oyendayenda, nyerere zankhondo zimayenda nthawi ya usiku ndipo zimayima kumanga msasa nthawi ya masana.



English : The colony begins a nomadic phase when available food has decreased. During this phase, the colony makes temporary nests that are changed everyday.

Nyanja : Pamene chakudya chatsika nyerere zimanka ziyenda kufuna chakudya. Munthawi imeneyi zimapanga zitsa zoyembekezera za tsiku ndi tsiku.



[Day24]

English : Each of these nomadic rampages or marches lasts for approximately 17 days.

Nyanja : Ina iliyonse yamayendedwe oterewa kapena mayendedwe omatenga pafupifupi masiku 17.



English : What is a cell? The word cell comes from the Latin word ¨cella¨, meaning ¨small room¨, and it was first coined by a microscopist observing the structure of cork.

Nyanja : Kodi cell ndi chani? Liwu loti cell limachokera ku liwu la Latin "cella", kuthandauza "chipinda chaching´ono" ndipo inapangidwa ndi microscopist atayang´ana mawonekedwe a chotsekera.



English : The cell is the basic unit of all living things, and all organisms are composed of one or more cells.

Nyanja : Cell ndicho chinthu chomwe chilichonse chamoyo chili nacho, ndipo zamoyo zonse zimapangidwa kuchokera ku cell kapena ma cell ambiri.



English : Cells are so basic and critical to the study of life, in fact, that they are often referred to as ¨the building blocks of life¨.

Nyanja : Ma cell ndi tating´ono koma tofunikira pamaphunziro okhuza moyo, tchutchutchu lake ndikuti, amatchedwa "zida zomangira moyo".



English : The Nervous System maintains homeostasis by sending nerve impulses through out the body to keep the flow of blood going as well as undisturbed.

Nyanja : Nervous System imatumiza mauthenga a misempha kuthupi lonse kuti magazi aziyendabe mosasokonezedwa.



English : These nerve impulses can be sent so quickly throughout the body which helps keep the body safe from any potential threat.

Nyanja : Nyesi zimenezi za mitsempha zimatumizidwa mwachangu mthupi lonse, zimenezi zimapangitsa kuti thupi likhale la chitetezo ku zoopsa zomwe zingabwere.



English : Tornadoes strike a small area compared to other violent storms, but they can destroy everything in their path.

Nyanja : Mphepo zamkuntho zimachitika kudera laling´ono poyerekeza ndi mphepo zina koma zitha kuononga chilichonse mu njira yake.



English : Tornadoes uproot trees, rip boards from buildings, and fling cars up into the sky. The most violent two percent of tornadoes last more than three hours.

Nyanja : Mphepo ya nkuntho imazula mitengo kuononga nyumba kugwetsa galimoto. Mphepo yankuntho yokwana maperesenti awiri yoononga kwambiri imaomba koposela maola atatu.



English : These monster storms have winds up to 480 km/h (133 m/s; 300 mph).

Nyanja : Mphepo zowopsa zamkunthozi zimakhala ndimphepo zothamanga mpaka 480 km / h (133 m / s; 300 mph).



English : Humans have been making and using lenses for magnification for thousands and thousands of years.

Nyanja : Anthu akhala akupanga ndikugwiritsa ntchito magalasi wopangisa kuti zinthu zizioneka zikuluzikulu kwa zaka zikwi zikwi.



English : However, the first true telescopes were made in Europe in the late 16th century.

Nyanja : Komabe ma telesikopu woyamba adapangidwa ku Ulaya nzaka zam´ma zana 16.



English : These telescopes used a combination of two lenses to make distant objects appear both nearer and larger.

Nyanja : Ma telescope amenewa amagwilitsa ntchito ma lens awiri kuti zinthu zakutali zioneke pafupi komanzo zikuzidwe.



English : Greed and selfishness will always be with us and it is the nature of cooperation that when the majority benefit there will always be more to gain in the short term by acting selfishly

Nyanja : Dyera ndi kuzikonda kudzakhala pakati panthu mpaka kalekale ndipo ndim´mene zimakhalira kuti ngati anthu ambiri apindula pamakhala mwai opindula koposa pochita zinthu modzikonda.



English : Hopefully, most people will realise that their long term best option is to work together with others.

Nyanja : Mwachiyembekezo, anthu ambiri azadzindikira kuti kwa nthawi yayitali apange chisankho chabwino chogwira ntchito limodzi ndi ena.



English : Many people dream of the day when humans can travel to another star and explore other worlds, some people wonder what´s out there some belive that aliens or other life may live on another plant.

Nyanja : Anthu ambili amalota tsiku lomwe anthu adzapite ku nyenyezi ina ndi kuonako malo ena, ena amadabwa kuti kunjaku kuli chani, ena amakhulupilira kuti kuli alendo kapena moyo muzomera kuma planet ena.



English : But, if this ever does happen probably won´t happen for a very long time. The stars are so spread out that there are trillions of miles between stars that are ¨neighbors¨.

Nyanja : Ngati zimenezi sizinachitike, zimatenga nthawi kuti zichitike.Nyenyezi zimakhala patalipatali ndipo zimakhala kutalitu, koposa zoyandikana nazo.



English : Maybe one day, your great grandchildren will be standing atop an alien world wondering about their ancient ancestors?

Nyanja : Kapena tsiku lina, zidzukulu zanu zikuluzikulu zidzayima pachulu mdziko lachilendo kuganizira makolo awo akalekale?



English : Animals are made of many cells. They eat things and digest them inside. Most animals can move.

Nyanja : Nyama zimapangidwa ndima cell ambiri. Zimadya zinthu ndikuzinyenya nkati ndipo nyama zambiri zimayenda.



English : Only animals have brains (though not even all animals do; jellyfish, for example, do not have brains).

Nyanja : Ndinyama zokha zomwe zimakhala ndi ubongo (ngakhale sinyama zonse zili nawo; mwachitsanzo jellyfish zilibe ubongo).



English : Animals are found all over the earth. They dig in the ground, swim in the oceans, and fly in the sky.

Nyanja : Nyamazi zimapezeka padziko lonse lapansi. Zimakumba munthaka, kusambira mu nyanja, komanso kuwuluka mumlengalenga.



English : A cell is the smallest structural and functional unit of a living (things) organism.

Nyanja : Cell ndi gawo lochepetsetsa loima ndi kugwira ntchito pa chinthu cha moyo.



English : Cell comes from the Latin word cella which means small room.

Nyanja : Cell lidachokera ku mawu achilatini otchedwa cella omwe amatanthauza kuti kachipinda kakang´ono.



English : If you look at living things under a microscope, you will see that they are made of small squares or balls.

Nyanja : Ngati mukuyang´ana zinthu zamoyo kudzera pamakina otchedwa mayikurosikopu, muzaona kuti zinthuzi zapangidwa ndi tinthu ting´onoting´ono towoneka ngati timabokosi kapena mipira.



English : Robert Hooke, a biologist from England, saw small squares in cork with a microscope.

Nyanja : Robert Hooke, katswiri wasayansi waku England, adawona tinthu ting´onoting´ono mu cork pogwilitsa ntchito makina otchedwa maikulosikopu.



English : They looked like rooms. He was the first person to observe dead cells

Nyanja : Zidawoneka ngati zipinda. Adali munthu woyamba kuwona ma cello wokufa.



[Day25]

English : Elements and compounds can move from one state to another and not change.

Nyanja : Zipangizo ndi zopangira zikhoza kuchoka mu mtundu wina kupita kwina ndipo osasintha.



English : Nitrogen as a gas still has the same properties as liquid nitrogen. The liquid state is denser but the molecules are still the same.

Nyanja : Mpweya wa Nitrogen uli ndi zizindikiro ngati za Nitrogen wamadzi. Wamadzi ndi olimba koma ma molecule ndi ofanana.



English : Water is another example. The compound water is made up of two hydrogen atoms and one oxygen atom.

Nyanja : Chitsanzo china ndi Madzi. Madzi amapangidwa ndi ma atom awiri a hydrogen ndi atom imodzi ya oxygen.



English : It has the same molecular structure whether it is a gas, liquid, or solid.

Nyanja : Ili ndi ma molecule ofanana kaya itakhale ngati mpweya, madzi, kapena chitsulo.



English : Although its physical state may change, its chemical state remains the same.

Nyanja : Ngakhale mawonekedwe ake akhoza kusintha, koma chemical yake imakhala yomweyo.



English : Time is something that is all around us, and affects everything we do, yet is difficult to understand.

Nyanja : Nthawi ndi chinthu chimene chili pakati pathu, motero yimakhudza zonse zomwe timachita, ngakhale ndiyovuta kuyimvetsetsa.



English : Time has been studied by religious, philosophical, and scientific scholars for thousands of years.

Nyanja : Nthawi yakhala ikuphunziridwa ndi zipembedzo, anthu anzeru, komanso azasayansi kwazaka zikwizikwi.



English : We experience time as a series of events passing from the future through the present to the past.

Nyanja : Timainva nthawi ngati ndondomeko ya zochitika kuchokela mtsogolo kufika lero mpaka m´mbuyo.



English : Time is also how we compare the duration (length) of events.

Nyanja : Nthawi ndi momwenso timafanizira matalikidwe (kutalika) a zochitika.



English : You can mark the passing of time yourself by observing the repetition of a cyclical event. A cyclical event is something that happens again and again regularly.

Nyanja : Muntha kuwona m´mene nthawi yapitira panokha poyang´ana kabwerezedwe ka chinthu chochitika mozungulira.Chinthu chochitika mozungulira ndi chinthu chomwe chimachitikachitika mobwerezabwereza.



English : Computers today are used to manipulate pictures and videos.

Nyanja : Pano makompuyuta akugwiritsidwa ntchito yokonzera zithunzi komaso makanema.



English : Sophisticated animations can be constructed on computers, and this kind of animation is increasingly being used in television and films.

Nyanja : Luso lapamwamba lopanga zinthu zosayenda kuoneka ngati zikuyenda mumakanema zimatha kuchitikira pamakina akompuyuta, ndipo mtundu wa ntchito ngati imeneyi ikuchulukira kugwiritsidwa ntchito mumakanema apawayilesi komaso makanema ena.



English : Music is often recorded using sophisticated computers to process and mix sounds together.

Nyanja : Nthawi zambiri nyimbozi zimajambulidwa pogwiritsa ntchito makompuyuta amakono kwambiri kuti anthe kuphatikiza mawu pamodzi.



English : For a long time during the nineteenth and twentieth centuries, it was believed the first inhabitants of New Zealand were the Maori people, who hunted giant birds called moas.

Nyanja : Kwa nthawi yaitali muzaka zama 1700 ndi 1800, kunkakhulupililidwa kuti anthu woyamba kukhala ku New Zealand anali a chi Maori amene ankasaka zimbalame zazikuluzikulu zotchedwa moas.



English : The theory then established the idea that the Maori people migrated from Polynesia in a Great Fleet and took New Zealand from the Moriori, establishing an agricultural society.

Nyanja : Chiphunzitsochi chimatsindikiza maganizo woti anthu achi Maori adachoka ku Polynesia ku Great Fleet komanso adalanda New Zealand kwa a Moriori, ndikuyambitsa ulimi pakati pawo.



English : However, new evidence suggests that the Moriori were a group of mainland Maori who migrated from New Zealand to the Chatham Islands, developing their own distinctive, peaceful culture.

Nyanja : Choncho, umboni watsopano ukunena zoti a Moriori adali gulu la Maori wochokera ku China amene adachoka ku New Zealand kulowera ku zilumba za Chatham, ndikukhala ndi chikhalidwe chawochawo chamtendere.



English : There was also another tribe on the Chatham islands these were Maori who migrated away from New Zealand.

Nyanja : Panalinso ntundu wina pa zilumba za Chatham amene anali a Maori amene anachoka ku New Zealand.



English : They called themselves the Moriori there were a few skirmishes and in the end, the Moriori were wiped out

Nyanja : Eni ake amadzitcha okha kuti a Moriori, panali kusagwirizana kochepa ndipo pa mapeto ake, a Moriori adaphedwa wonse.



English : Individuals who had been involved for several decades helped us appreciate our strengths and passions while candidly assessing difficulties and even failures.

Nyanja : Anthu amene adatenga nawo mbali kwa zaka zochuluk adathangatira kudziwa mphamvu ndi zimene timakonda komanso kuyang´ana zovuta ndiponso zolephera zathu.



English : While listening to individuals share their individual, family, and organizational stories, we gained valuable insight into the past and some of the personalities who influenced for good or ill the culture of the organization.

Nyanja : Pamene tikumvetsera kwa anthu omwe akutigayira nkhani zawo zokhuza, zam´mabanja awo, komaso nkhani zokhuza bungwe, timapezako zofunikira zina zakale ndiponso timadziwanso anthu ena omwe anapangitsa chikhalidwe chabwino ndi choyipa pa bungweli.



English : While understanding one's history does not assume understanding of culture, it does at least help people gain a sense of where they fall within the history of the organization.

Nyanja : Pamene tikumvetsa mbiri ya munthu tisaganizenso kuti tamvetsanso chikhalidwe, zimathandiza anthu kuzindikila mbali imene ali pa mbiri ya bungwe.



English : While assessing the successes and becoming aware of failures, individuals and the whole of the participating persons discover more deeply the values, mission, and driving forces of the organization.

Nyanja : Pamene tikuwunika zopambana komaso kudziwa kulephera kwathu, aliyense pamodzi ndi wonse wotenga nawo mbali amapeza zikhalidwe zozama, cholinga, ndiponso mphamvu zomwe zikuyendetsera bungwe.



English : In this instance, recalling previous instances of entrepreneurial behavior and resulting successes helped people to be open to new changes and new direction for the local church.

Nyanja : Munyengo ngati izi, kukumbukira zochitika zakale zamabizinesi ndi zotsatira zabwino kunathandizira anthu kumasuka kuzinthu zatsopano ndikutenga njira yatsopano kutchalichi kwawoko.



English : Such success stories lessened the fears of change, while creating positive inclinations toward change in the future.

Nyanja : Nkhani zachipambano zoterezi zidachepetsa mantha pakufuna kusintha zinthu, ndikukhala ndi maganizo abwino ofuna kusintha mtsogolo.



English : Convergent thinking patterns are problem solving techniques that unite different ideas or fields to find a solution.

Nyanja : Kachitidwe kam´mene mayankho amaperekedwera kumafunso mosavuto ndizo njira zopezera mayankho zomwe zimagwirizana ndi maganizo osiyana kapena magawo kuti mupeze yankho.



[Day26]

English : The focus of this mindset is speed, logic and accuracy, also identification of facts, reapplying existing techniques, gathering information.

Nyanja : Maganizidwewa cholinga chake ndi changu, kuganiza moyenera ndiponso kupanga zinthu molondola, komaso kutha kuzindikira mfundo, kugwiritsanso njira zokhazikika, kutolela zambiri.



English : The most important factor of this mindset is: there is only one correct answer. You only think of two answers, namely right or wrong.

Nyanja : Chinthu chofunika kwambiri nkaganizidwe aka nachi; pali yankho limodzi lokha lolondola. Pali mayankho awiri okha lolondola ndi lolakwika.



English : This type of thinking is associated with certain science or standard procedures.

Nyanja : Kaganizide aka nkogwilizana ndi kaganizidwe ka anthu ena a sayansi kapena kapangidwe kao ka zinthu.



English : People with this type of thinking have logical thinking, are able to memorize patterns, solve problems and work on scientific tests.

Nyanja : Anthu oganiza chonchi ali ndi maganizo ozama, amatha kuloweza zakachitikidwe ka zinthu, kuthana ndi zovuta ndi kugwira ntchito pa zakuyesera za sayansi.



English : Humans are by far the most talented species in reading the minds of others.

Nyanja : Anthu ndi mtundu womwe wuli ndi luso powelenga maganizo ayena.



English : That means we are able to successfully predict what other humans perceive, intend, believe, know or desire.

Nyanja : Ndiye zikutanthauza kuti tingathe kulosera bwino zomwe anthu ena amaganiza, amafuna, amakhulupilira, kudziwa kapena kulakalaka.



English : Among these abilities, understanding the intention of others is crucial. It allows us to resolve possible ambiguities of physical actions.

Nyanja : Zina zakuthekera kwazimenezi, kumvetsetsa cholinga cha ena ndikofunikira kwambiri. Zimatilola kuthetsa kusiyana kwa zochitika mthupi.



English : For example, if you were to see someone breaking a car window, you would probably assume he was trying to steal a stranger's car.

Nyanja : Mwachitsanzo mutawona wina akuswa zenera la galimoto mutha kuyesa akufuna kuba galimoto ya wina.



English : He would need to be judged differently if he had lost his car keys and it was his own car that he was trying to break into.

Nyanja : Akuyenera kuweluzidwa mosiyana makamaka kuti galimoto amayesa kutsegura ndiyake chifukwa chakuti makiyi ake anatayika.



English : MRI is based on a physics phenomenon called nuclear magnetic resonance (NMR), which was discovered in the 1930s by Felix Bloch (working at Stanford University) and Edward Purcell (from Harvard University).

Nyanja : MRI imachokela ku gawo la sayansi lotchedwa Nuclear Magnetic Resonance (NMR), limene linapezedwa mzaka za ma 1930 ndi a Felix Bloch (Aku Stanford Universtity) ndi a Edward Purcel (Aku Havard).



English : In this resonance, magnetic field and radio waves cause atoms to give off tiny radio signals.

Nyanja : M´malo oterewa, maginito komanso ma radio wave amapangitsa kuti ma atom apereke mauthenga wocheperako.



English : In the year 1970, Raymond Damadian, a medical doctor and research scientist, discovered the basis for using magnetic resonance imaging as a tool for medical diagnosis.

Nyanja : Muchaka cha 1970, Raymond Damadian, dotolo owona za mankhwala komanso wofufuza za sayansi, anapeza maziko ogwiritsa ntchito kulingalira kwa maginito ngati chida chothandizira kupeza vuto kuzipatala.



English : Four years later a patent was granted, which was the world´s first patent issued in the field of MRI.

Nyanja : Patapita zaka zinayi patent idaperekedwa, imene idali patent yoyamba padziko lapansi kupekedwa yokhudza MRI.



English : In 1977, Dr. Damadian completed the construction of the first "whole-body" MRI scanner, which he called the "Indomitable".

Nyanja : Mu chaka 1997, Dr. Damadian anamaliza kumanga chomwe amati ndi "thupi lonse" pa MRI scanner, imene adayitchula "Indomitable".



English : Asynchronous communication encourages time for reflection and reaction to others.

Nyanja : Kuyakhula motsindika kumathandiza kupeleka nthawi yachikumbu mtima ndikuti ena achitepo kanthu.



English : It allows students the ability to work at their own pace and control the pace of instructional information.

Nyanja : Amalola ophunzira kuti azitha kugwira ntchito momwe angafunire komanso kuongolera kayendetsedwe ka zidziwitso za ma maphunzilo monga iwo afunira.



English : In addition, there are fewer time restrictions with the possibility of flexible working hours. (Bremer, 1998)

Nyanja : Kuonjezerapo, pali nthawi zoletsa zochepa ndizokuthekera kosintha maola ogwirira ntchito (Bremer, 1998).



English : The use of the Internet and the World Wide Web allows learners to have access to information at all times.

Nyanja : Kugwilitsa ntchito intaneti ndi matsamba a intaneti zimathandiza awo akupanga sukulu kuti azikhala ndimwayi wodziwa zambiri nthawi iliyonse.



English : Students can also submit questions to instructors at any time of day and expect reasonably quick responses, rather than waiting until the next face-to-face meeting.

Nyanja : Ophunzira athanso kupereka mafunso kwa mphunzitsi nthawi ina iliyonse ya patsiku ndipo ayembekezere kulandira mayankho mwachangu, kusiyana ndikuti azidikira kuti akomaneso maso ndi maso.



English : The postmodern approach to learning offers the freedom from absolutes. There is no one good way to learn.

Nyanja : Njira zomwe akugwilitsa ntchito makono zimapereka ufulu ndithu. Palibenso njira ina yabwino yophunzirapo.



English : In fact, there is not one good thing to learn.Learning takes place in the experience between the learner and the knowledge presented.

Nyanja : Mwatchutchu, palibe chabwino choti muphunzire. Kuphunzira kumatenga malo pakati pa ophunzira ndiponso pakupereka zomwe waphunzirazo.



English : Our current experience with all the do-it-yourself and information presenting, learning-based television shows illustrates this point.

Nyanja : Zimene taziziwa zonse zokhuzana ndi njira yoti uzipanga wekha ndikuwonetsa zambiri, ziwonetsero za pakanema ophunzilira zikusonyeza mfundo imeneyi.



English : So many of us find ourselves watching a television show that informs us of a process or experience in which we will never participate or apply that knowledge.

Nyanja : Ambiri a ife timapezeka tikuwonera wayilesi ya kanema imene imatidziwitsa njira zina koma zomwe sititenga nawo mbali kapena kugwiritsa ntchito zomwe tadziwazo.



English : We will never overhaul a car, build a fountain in our backyard, travel to Peru to examine ancient ruins, or remodel our neighbour´s house.

Nyanja : Sitingamasule galimoto, kumanga fountain kumpanda, kuyenda kupita ku Peru kukaona nyumba zakale kapena kukonza nyumba ya omwe tawandikana nawo.



English : Thanks to undersea fiber optic cable links to Europe and broadband satellite, Greenland is well connected with 93% of the population having internet access.

Nyanja : Ndayamika chingwe cha optic fiber cholowera pansi pa nyanja cholumikiza ku Ulaya ndi satellite, Greeland ndiyolumikizana bwino ndi 93% ya anthu omwe ali ndi intaneti.



[Day27]

English : Your hotel or hosts (if staying in a guesthouse or private home) will likely have wifi or an internet connected PC, and all settlements have an internet cafe or some location with public wifi.

Nyanja : Malo ogona omwe muli kapena eni malo mukugona (ngati mukukhala mnyumba ya alendo kapena nyumba yaeni) atha kukhala ndi wifi kapena intaneti yolumikizidwa ku PC, ndipo midzi yonse ili malo amalonda wopangirako intaneti kapena malo ena a wifi ya aliyense.



English : As mentioned above, though the word ¨Eskimo¨ remains acceptable in the United States, it is considered pejorative by many non-U.S. Arctic peoples, especially in Canada.

Nyanja : Monga tanenela pamwambapa ngakhale kuti mau oti "Esikimo" ali ovomelezedwa ku America anthu ambiri akwina monga Arctic makamaka ku dziko la Canada amawatenga kuti mauwa ndi onyogodola.



English : While you may hear the word used by Greenlandic Natives, its use should be avoided by foreigners.

Nyanja : Pamene mukumva mawuwa akugwiritsidwa ntchito ndi mbadwa zaku Greenland, magwiritsidwe ake a ntchito ayenera kupewedwa ndi anthu ochokera kunja kwadzikolo.



English : The native inhabitants of Greenland call themselves Inuit in Canada and Kalaalleq (plural Kalaallit), a Greenlander, in Greenland.

Nyanja : Mbadwa zochokera ku Greenland zimadzitchula kuti ndima Inuit pamene aliku Canada ndiponso Kalaalleq (kuchuluka Kalaallit), ma Greenlander, ku Greenland.



English : Crime, and ill-will toward foreigners in general, is virtually unknown in Greenland. Even in the towns, there are no ¨rough areas.¨

Nyanja : Upandu ndi nkhanza , kwa obwera sizidziwika ku Greenland.Ngakhale mtawuni mulibe malo ovuta.



English : Cold weather is perhaps the only real danger the unprepared will face.

Nyanja : Nyengo yozizira ndiye chiopsezo chenicheni chomwe chimapeza osakonzekera.



English : If you visit Greenland during cold seasons (considering that the further north you go, the colder it will be), it is essential to bring warm enough clothing.

Nyanja : Ngati mukupita ku Greenland nthawi yozizira (poganizira kuti pamene ukupita kumpoto kwambiri mpamene kumazizira kwambiri), ndikoyenera kutenga zovala zotenthera zokwanira.



English : The very long days in the summer can lead to problems getting sufficient sleep and associated health issues.

Nyanja : Masiku ataliatali nthawi yotentha amapangitsa kubweletsa mavuto ovutika kugona ndikubweletsa zina zovuta pamoyo wamunthu.



English : During the summer, also watch out for the Nordic mosquitoes. Although they do not transmit any diseases, they can be irritating.

Nyanja : Munyengo yotentha khalani tcheru ndi udzudzu waku Nordic. Ngakhale suyambitsa matenda, koma umasowetsa mtendere.



English : While San Francisco´s economy is linked to it being a world-class tourist attraction, its economy is diversified.

Nyanja : Pamene nkhani zachuma zaku San Francisco zikulumikizana ndi kukopa alendo kochititsa chidwi padziko lonse lapansi, chuma chake chimachokera m´magawo osiyanasiyana.



English : The largest employment sectors are professional services, government, finance, trade, and tourism.

Nyanja : Anthu ambiri wogwira ntchito ndi amene ali akadaulo, aboma, zandalama, malonda ndi zokopa alendo.



English : Its frequent portrayal in music, films, literature and popular culture has helped make the city and its landmarks known throughout the world.

Nyanja : Mukuonetsedwa mwawo makamaka munyimbo, makanema, zolemba komanso chikhalidwe zodziwika zathandiza kupanga mzindawu ndiponso zochitika zake kudziwika padziko lonse.



English : San Francisco has developed a large tourist infrastructure with numerous hotels, restaurants, and top-notch convention facilities.

Nyanja : San Francisco yamanga malo akuluakulu okopa alendo omwe ali malo ogona ambiri, malo odyera ambiri komaso malo ena apamwamba.



English : San Francisco is also one of the best places in the nation for other Asian cuisine: Korean, Thai, Indian, and Japanese.

Nyanja : San Francisco ndi malo amodzi amalo omwe ali abwino mdziko pa nkhani ya zakudya zina zaku Asia: zaku Korea, zaku Thailand, zaku India komaso zaku Japan.



English : Traveling to Walt Disney World represents a major pilgrimage for many American families.

Nyanja : Kupita ku Walt Disney World zimaonetsa kuti ulendo wofunikira kwambiri kwa mabanja ambiri ku America.



English : The ¨typical¨ visit involves flying into Orlando International Airport, busing to an on-site Disney hotel, spending about a week without leaving Disney property, and returning home.

Nyanja : Ulendo "wamba" umakhudza kukwera ndege kupita kubwalo lalikulu la ndege la Orlando International, ndikukwera basi pamalo owogona a Disney, mkukhalako pafupifupi sabata imodzi osasiya katundu wa Disney, ndikubwelera kwawo.



English : There are infinite variations possible, but this remains what most people mean when they talk of ¨going to Disney World¨.

Nyanja : Pali kuthekera kosiyana ndithu kosatha, koma izi ndi zokhazikika zomwe anthu ambiri amatanthauza akamanena zokhudza "kupita ku Disney World".



English : Many tickets sold online through auction websites such as eBay or Craigslist are partially used multi-day park-hopper tickets.

Nyanja : Matikiti ambiri omwe amagulitsidwa pa matsamba a intaneti monga eBay kapena Craigslist amakhala kuti ndi matikiti oti mutha kugwiritsa ntchito kumalo ambiri komaso amakhala agwirapo ntchito kale pang´ono.



English : While this is a very common activity, it is prohibited by Disney: the tickets are non-transferable.

Nyanja : Ngakhale izi zimachitikachitika zimaletsedwa ndi a Disney: ndipo matiketi sapatsidwa kwa wina.



English : Any camping below the rim in Grand Canyon requires a backcountry permit.

Nyanja : Kumanga masasa pansi kunja kwa Grand Canyon kumafunika chilolezo choti muzabwelera ku dziko lanu.



English : Permits are limited to protect the canyon, and become available on the 1st day of the month, four months prior to the start month.

Nyanja : Zilolezo sizimaperekedwa zambiri zokhuza kuteteza canyon, choncho zimapezeka tsiku loyamba la mwezi, miyezi inayi usanayambe mwezi woyambirawo.



English : Thus, a backcountry permit for any start date in May becomes available on 1 Jan.

Nyanja : Chifukwa, chilolezo chobwelera chimayamba tsiku loyamba mu Meyi.



English : Space for the most popular areas, such as the Bright Angel Campground adjacent to Phantom Ranch, generally fill up by the requests received on first date they are opened to reservations.

Nyanja : Malo ku malo otchuka kwambiri monga Bright Angle Campground moyandikana ndi Phanto Ranch kumadzadza tsiku lomwelo loyamba kuti anthu asungitse malo.



English : There are a limited number permits reserved for walk-in requests available on a first come, first served basis.

Nyanja : Pamakhala zilolezo zochepa zomwe zimasungiridwa kwa ongobwera kudzafunsa potengera kuti woyamba kufika, ndi amene amayambirira kuthandizidwa.



English : Entering Southern Africa by car is an amazing way to see all the region´s beauty as well as to get to places off the normal tourist routes.

Nyanja : Kulowa Kumwera kwa Africa pa galimoto ndi njira yabwino yoonera kukongora kwa derali komanso kufikila malo amene samatchulidwa njira zodutsa alendo.



[Day28]

English : This can be done in a normal car with careful planning but a 4x4 is highly advised and many locations are only accessible with a high wheel base 4x4.

Nyanja : Izi zitha kuchitika mgalimoto zathu zamasiku onse ngati pali dongosolo labwino ngakhale ma 4x4 ndi amene aliwoyenera ndipo malo ambiri amafikidwa ndimagalimoto am´mwamba a 4X4 basi.



English : Keep in mind while planning that although Southern Africa is stable not all neighboring countries are.

Nyanja : Dzindikirani kuti pomwe mukukonzekera kuti kumwera kwa Africa ndikwabata koma osati mayiko onse oyandikana ali pamtendere.



English : Visa requirements and costs vary from nation to nation and are affected by the country you come from.

Nyanja : Zofunikira pa Visa pamodzi ndi mitengo yake zimakhala zosiyanasiyana kutengera dziko lomwe ukuchokera.



English : Each country also has unique laws requiring what emergency items need to be in the car.

Nyanja : Dziko lilonse lili ndimalamulo ake azinthu zomwe zimafunikira galimoto itapanga ngozi.



English : Victoria Falls is a town in the western portion of Zimbabwe, across the border from Livingstone, Zambia, and near Botswana.

Nyanja : Victoria Falls ndi kamzinda kakang´ono kakumadzulo kwa dziko la Zimbabwe, kudutsa ku malire kuchokera ku Livingstone, Zambia, ndiponso kufupi ndi dziko la Botswana.



English : The town lies immediately next to the falls, and they are the major attraction, but this popular tourist destination offers both adventure seekers and sightseers plenty of opportunities for a longer stay.

Nyanja : Mzindawu uli pafupi ndi mathithi, ndipo ndi amene amakopa kwambiri, ndipo malo osililikawa amapatsa onse okonda zochitika ndi ofuna kukawona malo mwayi wawukulu wokhala nthawi yayitali.



English : In the rainy season (November to March), the water volume will be higher and the Falls will be more dramatic.

Nyanja : Munyengo ya mvula (Novembala mpaka Marichi), kuchuluka kwa madzi kumakhala kokwera ndi Mathithi amakhala wosangalatsa.



English : You are guaranteed to get wet if you cross the bridge or walk along the trails winding near the Falls.

Nyanja : Nzodziwikilatu kuti munyowa ngati muyenda njira yooloka mulatho kapena tinjira tam´mbali mwa mathithi.



English : On the other hand, it is precisely because the volume of water is so high that your viewing of the actual Falls will be obscured—by all the water!

Nyanja : Pena, nchifukwa chakuti madziwo ndi ambiri moti simudzatha kuona mathithio bwino- chifukwa cha kuchuluka madzi.



English : Tomb of Tutankhamun (KV62). KV62 may be the most famous of the tombs in the Valley, the scene of Howard Carter´s 1922 discovery of the almost intact royal burial of the young king.

Nyanja : Manda a Tutankhamun (KV62).KV62 akhoza kukhala manda odziwika m´chigwa, pomwe Howard Carter mu 1922 anatulukira kuti anali manda pafupifupi osawonongeka a mfumu yaying´ono.



English : Compared to most of the other royal tombs, however, the tomb of Tutankhamun is barely worth visiting, being much smaller and with limited decoration.

Nyanja : Kufanizira ndi manda ena achifumu, ngakhale zili choncho manda a Tutankhamun ndiwoyenerabe kumawayendera, pakuti ndi wochepa ndiponso sanawakongoletsedwe kwambiri.



English : Anyone interested in seeing evidence of the damage to the mummy done during attempts to remove it from the coffin will be disappointed as only the head and shoulders are visible.

Nyanja : Aliyense wofuna umboni wa kuonongeka kwa ntembo pamene amafunira kuuchotsa mu bokosi azakhumudwa poti mutu ndi khosi ndi zomwe zili zoonekela.



English : The fabulous riches of the tomb are no longer in it, but have been removed to the Egyptian Museum in Cairo.

Nyanja : Chuma chambiri cha m´manda sichilinso m´mandamo, koma chinachotsedwa kupita ku Egyptian Museum ku Cairo.



English : Visitors with limited time would be best to spend their time elsewhere.

Nyanja : Alendo amene alibe nthawi yambiri nkwabwino kuti akataye nthawiyo ku malo ena.



English : Phnom Krom, 12 km southwest of Siem Reap. This hilltop temple was built at the end of the 9th century, during the reign of King Yasovarman.

Nyanja : Phnom Krom, makilomita khumi ndi awiri kumwela kwa chaku madzulo kwa Siem Reap. Kachisi wapa phiri ili anamangidwa pokutha pa zaka za ma 800 panthawi ya ulamuliro wa mfumu Yasovarman.



English : The gloomy atmosphere of the temple and the view over the Tonle Sap lake make the climb to the hill worthwhile.

Nyanja : Maonekedwe a mdima amukachisi ndi mawonekedwe a nyanja yotchedwa Tonle Sap amapangitsa kukwela phiri kukhala koyenela.



English : A visit to the site can be conveniently combined with a boat trip to the lake.

Nyanja : Ulendo wokaona kumaloko utha kuphatikizidwa ndi ndi ulendo wapa ngalawa wopita ku nyanja.



English : The Angkor Pass is needed to enter the temple so do not forget to bring your passport along when heading to Tonle Sap.

Nyanja : Angkor Pass imafunika kuti ulowe mu kachisi choncho musayiwale kubweletsa ziphaso zanu zolowela ndi kutulukila m´dziko mukamapita ku Tonle Sap.



English : Jerusalem is the capital and largest city of Israel, though most other countries and the United Nations do not recognize it as Israel´s capital.

Nyanja : Yerusalemu ndi likulu komaso mzinda waukulu wa dziko la Israel ngakhale mayiko ambiri kuphatikizapo United Nations sivomereza kuti mzindawu ndi likulu la dzikolo.



English : The ancient city in the Judean Hills has a fascinating history spanning thousands of years.

Nyanja : Mzinda wakale mumapiri a Yudea uli ndi mbiri yochititsa kaso ya zaka zikwizikwi zochulukirapo.



English : The city is holy to the three monotheistic religions - Judaism, Christianity and Islam, and serves as a spiritual, religious, and cultural center.

Nyanja : Mzinda umenewu ndiwoyera kuzipembedzo zitatu zokhudza Mulungu m´modzi - Chiyuda, Chikhristu ndi Chisilamu, komanso umagwiritsidwa nchito ngati malo auzimu, chipembedzo, ndiponso ngati chikhalidwe.



English : Due to the religious significance of the city, and in particular the many sites of the Old City area, Jerusalem is one of the main tourist destinations in Israel.

Nyanja : Chifukwa cha kufunika kwachipembedzo kwa mzindawu, makamaka malo ambiri ndiamumzinda wakalekale, Yerusalemu ndi amodzi amalo omwe kumapitako alendo ambiri mdziko la Israeli.



English : Jerusalem has many historic, archeological and cultural sites, along with vibrant and crowded shopping centers, cafés, and restaurants.

Nyanja : Yerusalemu ili ndi malo odziwika ndi ofunika ambiri, azinthu zakale komanso malo achikhalidwe, pamodzi ndi malo okongola ndi owunjikana anthu ogulitsirako, khofi komanso malo odyerako.



English : Ecuador requires that Cuban citizens receive an invitation letter prior to entering Ecuador through international airports or frontier admission points.

Nyanja : Ecuador imafuna kuti nzika zaku Cuba zizikhala ndi kalata zosonyeza kuti zayitanidwa kuti zilowe mdzikolo zisanalowe mu Ecuador podzera m´mabwalo andege akuluakulu kapena malo am´malire adzikolo.



English : This letter must be legalized by the Ecuadorian Ministry of Foreign Affairs, and comply with certain requirements.

Nyanja : Kalatayi ikuyenera kuvomelezedwa ndi malamulo ndi Unduna wa Zakunja ku Ecuador, komanso kukwaniritsa zina zofunifira.



[Day29]

English : These requirements are designed to provide an organized migratory flow between both countries.

Nyanja : Zofunikirazi zidakhazikitsidwa kamba kofuna kuti mayendedwe olowa ndi kutuluka mdziko akhale olongosoka pakati pa mayiko awiri.



English : Cuban citizens who are US green card holders should visit an Ecuadorian Consulate to obtain an exemption to this requirement.

Nyanja : Nzika zaku Cuba zomwe zili ndi makadi a green card aku US ayenera kufika ku ofesi ya oyimilira kazembe waku Ecuador kuti akatenge chilolezo choti zimenezi iwo zisawakhuze.



English : Your passport must be valid for at least 6 months beyond your travel dates. A round/onward trip ticket is needed to prove the length of your stay.

Nyanja : Chiphaso chanu cha ulendo chikuyenera kukhala chovomerezeka kwa miyezi isanu ndi umodzi kupitilira masiku anu aulendo. Tiketi yanu kaya yobwelera/ yopitilira imafunika kutsikimizira kutalika kwa nthawi yomwe mukhale.



English : Tours are cheaper for larger groups, so if you´re by yourself or with just one friend, try to meet other people and form a group of four to six for a better per-person rate.

Nyanja : Maulendo ndiotsika mtengo m´magulu akulu, chifukwa chake ngati muli nokha kapena ndi nzanu m´modzi, yesani kukumana ndi anthu ena ndikupanga gulu la anayi mpaka asanu kuti mulandire mtengo wabwino.



English : However, this shouldn´t really be off your concern, because often tourists are shuffled around to fill the cars.

Nyanja : Choncho, zimenezi siziyenera kukupatsani nkhawa, chifukwa kawirikawiri alendo amapachiridwa ndicholinga choti adzaze m´magalimoto.



English : It seems actually to be more a way of tricking people into believing they have to pay more.

Nyanja : Ndi njira chabe yowapusitsa anthu kuti mwina adziwapatsa ndalama yambiri.



English : Towering above the north end of Machu Picchu is this steep mountain, often the backdrop to many photos of the ruins.

Nyanja : Kudutsa pamwamba pa kumpota kwa Machu Picchu ndi phiri lalitali, limakhala chithunzi chamabwinja ambiri a zinthu zakale.



English : It looks a bit daunting from below, and it is a steep and difficult ascent, but most reasonably fit persons should be able to make it in about 45 minutes.

Nyanja : Zikuoneka kuti ndizovutilako kuchokera pansi, ndi mtsetse wovuta kukwera, koma anthu omwe matupi awo ali amphamvu amatha kukwera potenga mphindi 45.



English : Stone steps are laid along most of the path, and in the steeper sections steel cables provide a supporting handrail.

Nyanja : Masitepe amiyalaya adaikidwa munjira zambiri, malo wotsetsereka kwambiri muli zingwe zazitsulo zomwe anthu amazigwira pothandizira kupereka mphamvu zoti asagwe.



English : That said, expect to be out of breath, and take care in the steeper portions, especially when wet, as it can become dangerous quickly.

Nyanja : Zili choncho, yembekezerani kuti mubanika, ndipo samalani magawo otsetseleka makamaka kukanyowa poti kumakhala koopsya.



English : There´s a tiny cave near the top that must be passed through, it is quite low and a rather tight squeeze.

Nyanja : Pafupi ndi pamwamba pali kaphanga kamene kayenera kudutsidwa, kali m´musi kwambiri, ndipo ndikothina ndithu.



English : Seeing the sites and wildlife of the Galapagos is best done by boat, just as Charles Darwin did it in 1835.

Nyanja : Kuwona malo ndi nyama zamtchire zaku Galapagos zimafunika kugwilitsa ntchito ngalawa ngati m´mene adapangira Charles Darwin mu chaka cha 1835.



English : Over 60 cruise ships ply the Galapagos waters - ranging in size from 8 to 100 passengers.

Nyanja : Sitima zam´madzi zopitilira 60 zimadutsa m´madzi a Galapagos-Zonyamula anthu 8 kulekeza 100.



English : Most people book their place well in advance (as the boats are usually full during the high season).

Nyanja : Anthu ambiri amasungitsa malo awo lisanafike tsiku la ulendo (pachifukwa chakuti maboti amakhala odzaza nthawi yokondedwa yayitali).



English : Be sure the agent through whom you book is a Galapagos specialist with a good knowledge of a wide variety of ships.

Nyanja : Onetsetsani kuti mkhala pakati amene adakuthandizani akhale katswiri wapa Galapagos ndiwodziwa bwino mitundu yochuluka ya sitima zam´madzi.



English : This will ensure that your particular interests and/or constraints are matched with the ship most suitable to them.

Nyanja : Zimenezi zizawonetsa makamaka zofuna zanu ndi/kapena zosowa zanu zagwirizana ndi sitima yoyenera bwino kwa iwo.



English : Before the Spanish arrived in the 16th century, northern Chile was under Inca rule while the indigenous Araucanians (Mapuche) inhabited central and southern Chile.

Nyanja : Nthawi imene anthu aku Spain asadafike muzaka zamazana 16, kumpoto kwa Chile amalamuliridwa ndi Inca pamene nkhalakale zachi Araucania (Mapuche) amakhala pakati komanso kumwera kwa Chile.



English : The Mapuche were also one of the last independent American indigenous groups, that were not fully absorbed into Spanish-speaking rule until after Chile´s independence.

Nyanja : A Mapuche anali gulu limodzi loyima palokha lakumudzi ku America omwe sadatengereko zoyankhula zaku Spain ndi ulamuliro mpakana Chile atayamba kudzilamulira.



English : Although Chile declared independence in 1810 (amid the Napoleonic wars that left Spain without a functioning central government for a couple of years), decisive victory over the Spanish was not achieved until 1818.

Nyanja : Ngakhale dziko la Chile linalengeza za ufulu wodziyimilira mu 1810 (mkatikati mwa nkhondo ya Napoleon imene inasiya dziko la Spain kukhala ndi boma losagwira ntchito kwa zaka zambiri), kupambana kwakukulu ku dziko la Spain sikunakwaniritsidwe mpaka mu 1818.



English : The Dominican Republic (Spanish: República Dominicana) is a Caribbean country that occupies the eastern half of the island of Hispaniola, which it shares with Haiti

Nyanja : Dominican Republic (Spanish: Rupública Dominicana) ndi dziko la Caribbean limene linatenga theka la malo a chigawo chakumanja a chilumba cha Hispaniola, chimene imagawana ndi Haiti.



English : Besides white sand beaches and mountain landscapes, the country is home to the oldest European city in the Americas, now part of Santo Domingo.

Nyanja : Kupatula magombe a mchenga oyela ndi mapiri, dzikoli lili ndi mzinda wakale kwambiri wa anthu a ku Ulaya kumwela kwa America, kumene pano ndi mbali ya Santo Domingo.



English : The island was first inhabited by the Taínos and Caribes. The Caribes were an Arawakan-speaking people who had arrived around 10,000 BCE.

Nyanja : Chilumbachi chidayamba kukhalidwamo ndi anthu achi Taínos komanso ma Caribes. Ma Caribes ankalankhula Arawakan ndipo adafika pafupifupi 10,000 BCE.



English : Within a few short years following the arrival of European explorers, the population of Tainos had significantly been reduced by the Spanish conquerors

Nyanja : M´zaka zochepa kuchokera pamene ofufuza aku Ulaya anafika, anthu a ku Tainos anali atachepepa kwambiri chifukwa cha kugonja ndi Spain.



English : Based on Fray Bartolomé de las Casas (Tratado de las Indias) between 1492 and 1498 the Spanish conquerors killed around 100,000 Taínos.

Nyanja : Malingana ndi a Fray Bartolomé de las Casas (Tratado de las Indias) pakati pazaka zam´ma 1492 komanso 1498 asilikali wochokera ku Spain adapha ma Taíno ngati 100,000.



English : Jardín de la Unión. This space was built as the atrium for a 17th-century convent, of which the Templo de San Diego is the sole surviving building.

Nyanja : Jardín de la Unión. Malo amenewa adamangidwa ngati atrium ya nyumba ya zaka mazana 17, Templo de Sa Diego ndi nyumba yokhayo imene idatsala.



[Day30]

English : It now functions as the central plaza, and always has a lot of things going on, day and night.

Nyanja : Ili ngati malo apakati , ndipo zinthu zambiri zimachitika , m´mawa ndi madzulo.



English : There are a number of restaurants surrounding the garden, and in the afternoons and evening there free concerts are often given from the central gazebo.

Nyanja : Pali malo ambiri odyera ozungulira mundawo, madzulo komaso usiku pamakhala zoyimbayimba zaulere zomwe zimachitikira pakati pa gazebo.



English : Callejon del Beso (Alley of the Kiss). Two balconies separated by only 69 centimeters is home of an old love legend.

Nyanja : Callejon del Beso (Alley of the kiss). Makonde awili omwe anasiyana ndi ma sentimita 69 ndi malo akalekale achikondi.



English : For a few pennies some children will tell you the story.

Nyanja : Ndi ndalama yochepa kwambiri ana ena atha kukuwuzani nkhani.



English : Bowen Island is a popular day trip or weekend excursion offering kayaking, hiking, shops, restaurants, and more.

Nyanja : Chilumba cha Bowen ndi chodziwika ndi ulendo wapatsiku kapena mathelo asabata, kumene kumapezeka kayaking, kuyenda, masitolo, malo odyera, ndi zina.



English : This authentic community is located in Howe Sound just off Vancouver, and is easily accessed via scheduled water taxis departing Granville Island in downtown Vancouver.

Nyanja : Malo ovomerezekawa ali ku Howe Sound kungodutsa Vancouver, amapezeka mosavuta kudzera pama taxi m´madzi ochokera ku Chilumba cha Granville kumusi kwa Vancouver.



English : For those who enjoy outdoor activities, a trek up the Sea to Sky corridor is essential.

Nyanja : Kwa amene amakonda zochitika panja , ulendo wochoka ku Sea to Sky ndi ofunika.



English : Whistler (1.5 hour drive from Vancouver) is expensive but well-known because of the 2010 Winter Olympics.

Nyanja : Whistler (komwe ndikoyenda maola 1.5 kuchokera ku Vancouver), ndikodula zinthu koma ndi kodziwika chifukwa chamasewelo a 2010 Winter Olympic.



English : In the winter, enjoy some of the best skiing in North America, and in the summer try some authentic mountain biking.

Nyanja : Munyengo yozizila pitani mukasangalale ndi masewela a skiing kumpoto kwa America mu chilimwe pitani mukakwele njinga m´mapiri.



English : Permits must be reserved in advance. You must have a permit to stay overnight at Sirena.

Nyanja : Muyenera kusungitsiratu Zilolezo. Muyenera kukhala ndichilolezo kuti mugone ku Sirena.



English : Sirena is the only ranger station that offers dormitory lodging and hot meals in addition to camping. La Leona, San Pedrillo, and Los Patos offer only camping with no food service.

Nyanja : Sirena ndimalo okhawo a alenje kumene alendo amagona ngati gulu, kumapezeka chakudya chotentha kuphatikizapo misasa. Pamene La Leona, San Pedrillo, ndi Los Patos amapereka misasa yokha basi popanda chakudya.



English : It is possible to secure park permits directly from the Ranger Station in Puerto Jiménez, but they do not accept credit cards

Nyanja : Ku Ranger Station imene ili ku Puerto Jiménez, kumeneku mutha kukapeza ziphaso zolowera ku paki , choncho samalora kulipira ndi makadi a credit card.



English : The Park Service (MINAE) does not issue park permits more than one month in advance of anticipated arrival.

Nyanja : A Park Service (MINAE) samaperekeratu zilolezo za paki kupitilira mwezi umodzi omwe mukuganiza kufika.



English : CafeNet El Sol offers a reservation service for a fee of US$30, or $10 for one-day passes; details on their Corcovado page.

Nyanja : CafeNet El Sol imapanga zosungitsa malo pamtengo wa $30, komanso $10 kwa tsiku limodzi; zambiri zili pa tsamba la Corcovado.



English : The Cook Islands are an island country in free association with New Zealand, located in Polynesia, in the middle of the South Pacific Ocean.

Nyanja : Dziko la Cook ndi la zilumba limene limagwirizana mopanda kukamizidwa ndi dziko la New Zealand, lomwe lili ku Polynesia, pakati pa Nyanja yamchere ya Pacific.



English : It is an archipelago with 15 islands spread out over 2.2 million km2 of ocean.

Nyanja : Ndi gulu la zilumba zokwana 15 zofalikira mtunda wautali okwana mamaliyoni 2.2 km2 pa nyanja.



English : With the same time zone as Hawaii, the islands are sometimes thought of as ¨Hawaii down under¨.

Nyanja : Kamba kakuti ali mu gawo lanthawi yofanana ngati yaku Hawaii, zilumbazi nthawi zina zimaonedwa ngati "Hawaii wapansi".



English : Though smaller, it reminds some elderly visitors of Hawaii before statehood without all the large tourist hotels and other development.

Nyanja : Ngakhale ndizocheperako, zimakumbutsa alendo ena okalamba omwe adafika ku Hawaii lisadakhazikitsidwe boma opanda malo ogonamo akulu onse akulu ndi zitukuko zina.



English : The Cook Islands do not have any cities but are composed of 15 different islands. The main ones are Rarotonga and Aitutaki.

Nyanja : Chilumba Cha Cook chilibe mizinda yiliyonse koma chili ndi zilumba 15 zosiyanasiyana. Zomwe zikululuzikulu ndi Rarotonga ndi Aitutaki.



English : In developed countries today, providing deluxe bed and breakfasts has been raised to a sort of art-form.

Nyanja : M´mayiko otukuka masiku ano, kupereka makama otchedwa deluxe ndi kadzutsa zafika ngati paluso tsopano.



English : At the top end, B&Bs obviously compete mainly on two main things: bedding and breakfast.

Nyanja : Pamwamba pomalizirapo, B&Bs chachidziwikire imapikisana kwambiri pa zinthu ziwiri: Zofunda ndi Kadzutsa.



English : Accordingly, at the finest such establishments one is apt to find the most luxurious bedding, maybe a handmade quilt or an antique bed.

Nyanja : Choncho, m´malo abwino ngati awa mutha kupeza zofunda zabwino kwambiri , mwina chopangidwa ndi manja kapena kama lamasiku adzana.



English : Breakfast may include seasonal delights of the region or the host´s speciality dish.

Nyanja : Chakudya cham´mawa chitha kukhala zakudya zomwe zimabwera mu nyengo zina za mchigawocho kapena chakudya chapaderadera chomwe wakonza mwini nyumba.



English : The setting might be an historic old building with antique furnishings, manicured grounds and a swimming pool.

Nyanja : Malowa atha kukhala a nyumba ya mbiri yakale yokhala ndi ziwiya zakale ma bwalo otchetchedwa bwino komanso dziwe losambira.



English : Getting into your own car and heading off on a long road trip has an intrinsic appeal in its simplicity.

Nyanja : Kukwera mugalimoto yako ndikuyenda ulendo wautali ndizinthu zina zake zosangalatsa.



[Day31]

English : Unlike larger vehicles, you are probably already familiar with driving your car and know its limitations.

Nyanja : Mosayelekeza ndi magalimoto akuluakulu, nkutheka kuti mukudziwa bwino lomwe kuyendetsa galimoto yanu komanso mukudziwa zofooka zake.



English : Setting up a tent on private property or in a town of any size can easily attract unwanted attention.

Nyanja : Kukhoma chihema pamalo anu kapena mumzinda waung´ono uliwonse kungathe kubweletsa chidwi chosafunikira.



English : In short, using your car is a great way to take a road trip but seldom in itself a way to ¨camp¨.

Nyanja : Mwachindunji, kuyenda pa galimoto yanu ndi njira yabwino yoyendera koma sinjira imene imagwiritsidwa nthawi zambiri popita ku "msasa".



English : Car camping is possible if you have a large minivan, SUV, Sedan or Station Wagon with seats that lay down.

Nyanja : Kukhala mugalimoto ndikotheka ngati muli ndi galimoto lokulirapo la minivan, SUV, Sedan kapena Station Wagon ndi mipando yoti itha kugonekedwa.



English : Some hotels have a heritage from the golden age of steam railways and ocean liners; before the Second World War, in the 19th or early 20th centuries.

Nyanja : Malo ena ogona alendo ali ndi mbiri yochokera kunthawi ya golden age yamasitima apamtunda woyendera nthuzi komanso masitima am´madzi akuluakulu otenga anthu; nkhondo yachiwiri isadayambe, mzaka za m´mazana khumi ndi zisanu mchinayi kapena kumayambiliro azaka zam´mazana makumi awiri.



English : These hotels were where the rich and the famous of the day would stay, and often had fine dining and nightlife.

Nyanja : Malo ogonawa kunali kumene anthu olemela ndi otchuka amasiku amenewo amakhala , ndiponso nthawi zambiri amakhala ndi malo abwino odyela komanso chisangalalo chabwino cha usiku.



English : The old fashioned fittings, the lack of the latest amenities, and a certain graceful agedness are also part of their character.

Nyanja : Zovala zachikale, kusowa kwa zinthu zamakonoi, komanso chikale china chokongola ndichimodzi mwazikhalidwe zawo.



English : While they are usually privately owned, they sometimes accommodate visiting heads of state and other dignitaries.

Nyanja : Ngakhale kuti malowa siofikila alendo, nthawi zina atsogoleri a maiko ndi olemekezeka ena amalandilidwa.



English : A traveller with piles of money might consider a round the world flight, broken up with stays in many of these hotels.

Nyanja : Wapaulendo amene ali ndi ndalama zambiri atha kuganiza zozungulira dziko lonse pandege, powugawa pomakhala m´malo ogona ambiriwa.



English : A hospitality exchange network is the organization that connects travelers with locals in the cities they are going to visit.

Nyanja : Kulandila alendo mwamsangala komanso kusithana mauthenga ndi bungwe limene limalumikiza anthu apaulendo ndi anthu akumizinda kumene akupita.



English : Joining such a network usually just requires filling out an online form; although some networks offer or require additional verification.

Nyanja : Kulowa pa netiweki imeneyi kumafunika kulemba fomu yapa intanenti, ngakhale ma netiweki ena amafuna kutsimikiza kowonjezerapo.



English : A listing of available hosts is then provided either in print and/or online, sometimes with references and reviews by other travelers.

Nyanja : Mndandanda wa eni malo omwe alipo udaperekedwa podzera pakutsindikizidwa ndi/ kapena pa intaneti, nthawi zina ndi umboni ndi kuwunikira kwa apaulendo ena.



English : Couchsurfing was founded in January 2004 after computer programmer Casey Fenton found a cheap flight to Iceland but did not have a place to stay.

Nyanja : Couchsurfing idayamba mu Januwale chaka 2004 kamba kakatswiri olemba mapulogalamu apakompuyuta a Casey Fenton adapeza ndege yotsika mtengo yopita ku Iceland koma adalibe malo oti akhaleko kumeneko.



English : He emailed students at the local university and received an overwhelming number of offers for free accommodation.

Nyanja : Anatumiza imelo kwa ophunzira ku yunivesite yakomweko ndipo analandira mwayi wochuluka wopatsidwa mwaulere malo ogona.



English : Hostels cater primarily to young people – a typical guest is in their twenties – but you can often find older travellers there too.

Nyanja : Malo okhala gulu amasunga achinyamata - alendo ambili amakhala ndi zaka zam´ma kumi awiri- koma mutha kupeza akuluakulunso kumeneku nthawi zina.



English : Families with children are a rare sight, but some hostels do allow them in private rooms.

Nyanja : Ndizosowa kuti uwone mabanja omwe ali ndi ana, koma malo ogona chigulu amalola kuti akhale muzipinda zawozawo.



English : The city of Beijing in China will be the host city of the Olympic Winter Games in 2022, which will make it the first city to have hosted both the summer and winter Olympics.

Nyanja : Mzinda wa Beijin ku China ndiwomwe masewera adzachitikire amu nyengo yozizira a Olympic Winter Games mu 2022, zomwe zizapangitse kuti ukhale mzinda woyamba kuchitika masewerowa kawiri amunyengo yotentha komaso yozizira.



English : Beijing will host the opening and closing ceremonies and the indoor ice events.

Nyanja : Ku Beijin ndikomwe kukachitikire mwambo wa zotsegulira ndi zotsekera zamasewera komaso masewero anyumba apadzi owuma.



English : Other skiing events will be at the Taizicheng ski area in Zhangjiakou, about 220 km (140 miles) from Beijing.

Nyanja : Zochitika zina zokhuza masewero a skii, zikachitikira ku malo a Taizicheng ski amene ali mu mzinda wa Zhangjiakou, pafupifupi makilomita 220 (mamayilosi 140) kuchokera ku Beijing.



English : Most of the temples do have an Annual festival starting from November end to Mid of May, which varies according to each temple´s annual calendar.

Nyanja : Zikondwelero zapachaka zamakachisi ambiri zimayamba kumapeto kwa Novembala mpaka pakati pa Meyi, ndipo zimasiyanasiyana malingana ndi kalendala yapachaka ya kachisi.



English : Most of the temple festivals is celebrated as part of temple´s anniversary or presiding deity´s birthday or any other major event associated with the temple.

Nyanja : Zikondwelero zokhudza mu kachisi zimakhala gawo lokondwelera chaka kapena kubadwa kwa timilungu kapena zikondwelero zina zokhudza tchalitchi.



English : Kerala´s temple festivals are very interesting to see, with regular procession of decorated elephants, temple orchestra and other festivities.

Nyanja : Maphwando amu kachisi wa Kerala ndiwopatsa chidwi kuonera, ndi mayendedwe anthawi zonse a njovu zokongoletsedwa, mayimbidwe amukachisi ndi zikondwelero zina.



English : A World´s Fair (commonly called World Exposition, or simply Expo) is large international festival of arts and sciences.

Nyanja : Chiwonetsero cha Padziko lonse (chotchedwa World Exposion, kapena kuti Expo) ndichikondwerero chachikulu chamayiko ambiri omwe amawonetsa zalunso ndi sayansi.



English : Participating countries present artistic and educational displays in national pavilions to showcase world issues or their country´s culture and history.

Nyanja : Mayiko amene akutenga nawo mbali amaonetsa luso ndi zamaphunziro mu dziko lawo kapena kuwonetsa zinthu zokhudza dziko ndi mbiri yamayiko yawo.



English : International Horticultural Expositions are specialised events which showcase floral displays, botanical gardens and anything else to do with plants.

Nyanja : International Horticultural Expositions ndi zochitika zapadera zomwe zimawonetsa maluwa, minda yamaluwa ndi china chilichonse chokhudzana ndi zomera.



[Day32]

English : Although in theory they can take place annually (so long as they are in different countries), in practice they are not.

Nyanja : Ngakhale kuti nkulingalira nkotheka kupangika chaka ndi chaka (bola zichitike maiko osiyanasiyana), koma sizingatheke kutero.



English : These events normally last anywhere between three and six months, and are held on sites no smaller than 50 hectares.

Nyanja : Zochitika izi zimakhalapo kulikonse pakati miyezi yitatu ndi isanu ndi umodzi ndipo zimachitima m´malo osachepera mahekita 50.



English : There are many different film formats that have been used over the years. Standard 35 mm film (36 by 24 mm negative) is much the commonest.

Nyanja : Ilipo mitundu yochuluka yamakanema imene yagwiritsidwa ntchito kwa zaka zochuluka. Kanema wa Standard wa 35 mm (36 ndi 24 mm negative) ndi amene amapezeka ponseponse.



English : It can usually be replenished fairly easily if you run out, and gives resolution roughly comparable to a current DSLR.

Nyanja : Zimatheka kubwenzeletsedwa mosavuta zikati zatha, koma kutapezeka njira yakuti pamenepo ndiyabwinoko ya DSLR.



English : Some medium-format film cameras use a 6 by 6 cm format, more precisely a 56 by 56 mm negative.

Nyanja : Makamela ena a pakatipati amakanema amagwilitsa ntchito filimu ya masentimita 6 ndi 6, ambiri kwenikweni ama negative okula mamilimita 56 ndi 56.



English : This gives resolution almost four times that of a 35 mm negative (3136 mm2 versus 864).

Nyanja : Izi zimapereka mawalidwe pafupifupi kanayi kama 35 mm negative (3136mm2 versus 864).



English : Wildlife is among the most challenging motifs for a photographer, and needs a combination of good luck, patience, experience and good equipment.

Nyanja : Nyama zakuthengo ndizovuta zina kwa amene amajambula zithunzi, choncho kumafunikira mwayi, kupilira, kudziwa bwino komanso zida zoyenera.



English : Wildlife photography is often taken for granted, but like photography in general, a picture is worth a thousand words.

Nyanja : Zithunzi zachilengedwe zakutchire sizimatengedwa ngati zofunikira nthawi zambiri, koma m´mene zojambula zilili, chithunzi ndicholemera mawu zikwi.



English : Wildlife photography often requires a long telephoto lens, though things like a flock of birds or a tiny creature need other lenses.

Nyanja : Kujambula zithunzi za chilengedwe mthengo kunali makamera ama lens ataliatali ngakhale kuti zinthu ngati mbalame ndi zolengedwa zina zing´onozingono zimafuna ma lens amitundu ina.



English : Many exotic animals are hard to find, and parks sometimes have rules about taking photographs for commercial purposes.

Nyanja : Nyama zambili zobwela nzovuta kuzipeza ndipo nthawi zina nkhalango zosungilako nyama zimaika malamulo okhuza kutola zithunzi pa chifukwa chofuna phindu.



English : Wild animals might either be shy or aggressive. The environment might be cold, hot, or otherwise hostile.

Nyanja : Nyama zakuthengo zitha kukhala zamanyazi komanso zolusa. Komwe zimatha kukhala kozizira, kotentha kapenanso osati kwabwino.



English : The world has over 5,000 different languages, including more than twenty with 50 million or more speakers.

Nyanja : Dziko lapansi lili ndi zilankhulo zoposa zikwi zisanu, ndipo zoposa makumi awiri zili ndi olankhula mamiliyoni 50 kapena kuposela apo.



English : Written words are often easier to understand than spoken words, also. This is especially true of addresses, which are often difficult to pronounce intelligibly.

Nyanja : Mawu olembedwa amakhala osavuta kuwamvetsetsa kusiyana ndi mawu oyankhulidwa, nawonso. Izi ndizowona makamaka pama keyala, amene amakhala ovuta kuwatchula momveka bwino.



English : Many entire nations are completely fluent in English, and in even more you can expect a limited knowledge - especially among younger people.

Nyanja : Mayiko ambiri amalankhula bwino Chingerezi kwathunthu, ngakhale kwambiri umayembekezera kuti amadziwa mochepa makamaka pakati pa achinyamata.



English : Imagine, if you will, a Mancunian, Bostonian, Jamaican and Sydneysider sitting around a table having dinner at a restaurant in Toronto.

Nyanja : Tangoganizani, ngati mukufuna munthu waku Mancun, waku Boston, waku Jamaica komaso waku Sydney atakhala kuzungulira tebulo kudya mgonero pamalo odyera ku Toronto.



English : They´re regaling each other with stories from their hometowns, told in their distinct accents and local argot.

Nyanja : Amasangalatsana wina ndi m´zake ndi nkhani zochokera maloawo obadwira, zomwe zimayankhulidwa m´mawu awo omveka bwino komanso gulu la kudelalo.



English : Buying food in supermarkets is usually the cheapest way to get fed. Without cooking opportunities, choices are however limited to ready-made food.

Nyanja : Kugula chakudya mumasitolo akuluakulu ndi njira yopezera chakudya yotsika mtengo kwambiri. Pamene palibe kuthekera kophika, chisankho chimakhala ku zakudya zophika kale.



English : Increasingly supermarkets are getting a more varied section of ready-made food. Some even provide a microwave oven or other means to heat food.

Nyanja : Masitolo akuluakulu ochulukirachulukira akumakhala ndi gawo logulitsa zakudya zokonza kale. Ena akumapereka mpaka microwave kapena njira zina zotenthesera zakudya.



English : In some countries or types of stores there is at least one on-site restaurant, often a rather informal one with affordable prices.

Nyanja : M´mayiko ena kapena mu mitundu ina yamasitolo mumakhala malo odyera pompo, nthawi zambiri malowa sakhala okhazikika koma mitengo yake imakhala yomvelera.



English : Make and carry copies of your policy and your insurer´s contact details with you.

Nyanja : Pangani ndikunyamula zikalata za inshuransi yanu ndipo mukhaleso ndizolumikizirana ndi kampani ya inshuransi yanu.



English : They need to show the insurer´s e-mail address and international phone numbers for advice/authorizations and making claims.

Nyanja : Akuyenela kuonetsa keyala ya imelo ya inshuransi ndi nambala zao zama telefoni ogwira ngakhale kunja kuti alandile chilolezo ndi uphungu komanso chithandizo.



English : Have another copy in your luggage and online (e-mail to yourself with attachment, or stored in the ¨cloud¨).

Nyanja : Muchilankhulo chanu mukuyenera kukhala ndi kope ina komanso pa intaneti (muzitumizire nokha imelo ya uthenga wake, kapena kusungidwa mu "cloud").



English : If traveling with a laptop or tablet, store a copy in its memory or disc (accessible without the internet).

Nyanja : Mukamayenda ndi laputopu kapena kompuyuta yam´manja yotchedwa tablet, muzisunga zina mu memory card kapena disc (zokuti mutha kuzipeza wopanda intaneti).



English : Also give policy/contact copies to traveling companions and relatives or friends back home willing to help.

Nyanja : Apatseniso chikalata cha inshuransi/ zolumikizirana anzanu omwe mukuyenda nawo komaso abale ndi abwenzi omwe ali kumudzi ofuna kuthandiza.



English : Moose (also known as elk) aren´t inherently aggressive, but will defend themselves if they perceive a threat.

Nyanja : Moose (amadziwikanso ndi dzina la elk) sinyama yoopsya koma imadziteteza yokha ngati iopsezedwa.



[Day33]

English : When people don´t see moose as potentially dangerous, they may approach too closely and put themselves at risk.

Nyanja : Pamene anthu amayitenga ngati Mphalapala ndi nyama yosaopsa, amatha kuyiyandikira kwambiri kumene kuli kuziyika pa chiopsezo.



English : Drink alcoholic drinks with moderation. Alcohol affects everyone differently, and knowing your limit is very important.

Nyanja : Kumamwa zakumwa zoledzeletsa moyenelera. Mowa umakhudza anthu mosiyana ndipo kudziwa mulingo wanu ndikofunikira kwambiri.



English : Possible long term health events from excessive drinking can include liver damage and even blindness and death. The potential danger is increased when consuming illegally produced alcohol.

Nyanja : Mavuto amene atha kubwela chifukwa cha uchidakwa akuphatikizila kuonongeka kwa chiwindi, khungu komanso imfa. Vutoli limakula pamene munthu akumwa mowa wopangidwa mosaloledwa.



English : Illegal spirits can contain various dangerous impurities including methanol, which can cause blindness or death even in small doses.

Nyanja : Zakumwa zoledzeletsa zopanda chilolezo zimatha kukhala ndi zoyipa zambiri kuphatikizapo methanol, amene amatha kupangitsa khungu kapena kufa pamene wamwedwa wamulingo wochepa.



English : Eyeglasses can be cheaper in a foreign country, especially in low-income countries where labour costs are lower.

Nyanja : Mandala amakhala otsika ntengo maiko ena makamaka kumaiko okwela kumene ogwira ntchito amalandila ndalama zochepa.



English : Consider getting an eye exam at home, especially if insurance covers it, and bringing the prescription along to be filed elsewhere.

Nyanja : pangani ganizo loti akakuyezeni maso anu muli kunyumba, makamaka pamene ngati insuransi ikukhuzaso zamaso, ndikubweretsa mankhwala omwe anakulemberani ndikuti zikasungidwe bwino lomwe penapake.



English : High-end brand-name frames available in such areas may have two problems; some may be knock-offs, and the real imported ones may be more expensive than at home.

Nyanja : Maferemu apamwamba amayina otchuka amene akupezeka m´malo amenewa atha kukhala ndi mavuto awiri; ena atha kukhala ongofanana koma sienieni, ndipo amene adachokera kunja atha kukhala odula kusiyana ndiwomwe sakuchokera kunja.



English : Coffee is one of the world´s most traded commodities, and you can probably find many types in your home region.

Nyanja : Khofi ndi chinthu chimodzi chogulitsidwa kwambiri padziko lonse ndipo mutha kupeza mitundu yambiri kwanuko.



English : Nevertheless, there are many distinctive ways of drinking coffee around the world that are worth experiencing.

Nyanja : Choncho, pali njira zapaderadera zambiri zomwera khofi padziko lonse zapansi zomwe muyenera kudzidziwa.



English : Canyoning (or: canyoneering) is about going in a bottom of a canyon, which is either dry or full of water.

Nyanja : Kudutsa m´malo othamanga madzi (kapena: kudumphira m´madzi othamanga kwambiri odutsa m´mapiri) ndi ngati kupita pansi pa malo ozama, omwe akhoza kukhala owuma kapena odzadza madzi.



English : Canyoning combines elements from swimming, climbing and jumping--but requires relatively little training or physical shape to get started (compared to rock climbing, scuba diving or alpine skiing, for example).

Nyanja : Kuyenda malo otsika zedi zimaphatikiza zinthu kuchokera kusamba, kukwera ndi kudumpha-- koma zimafunikira maphunziro ocheperako kapena munthu wazitho kuti muyambepo (poyelekeza ndi kukwera miyala, kusambira m´madzi kapena kutsetseleka m´mapiri, mwachitsanzo).



English : Hiking is an outdoor activity which consists of walking in natural environments, often on hiking trails.

Nyanja : Kuyenda wapansi ndi ntchito ya panja yomwe imakhuza kuyenda m´malo azachilengedwe, nthawi zambiri pogwiritsa tinjira toyenderamo.



English : Day hiking involves distances of less than a mile up to longer distances that can be covered in a single day.

Nyanja : Kuyenda masana kumakhala kwa ulendo wochepa wosakwana mayilosi mpaka mitunda italiitali yomwe itha kuyendedwa pa tsiku limodzi.



English : For a day hike along an easy trail little preparations are needed, and any moderately fit person can enjoy them.

Nyanja : Kuyenda kwatsiku limodzi mu njila yosavuta kumafuna kukonzekela pang´ono, komanso ndikofunika, ndipo munthu aliyese wankhongono angathe kukwanitsa.



English : Families with small children may need more preparations, but a day outdoors is easily possible even with babies and pre-school children.

Nyanja : Mabanja omwe ali ndi ana achichepere atha kufuna kukonzekera kwambiri, koma kutuluka kunja patsikulo nkotheka mosavutikira ngakhale ndi makanda omwe ndi ana osayamba sukulu.



English : Internationally, there are nearly 200 running tour organizations. Most of them operate independently.

Nyanja : Pali ma bungwe oposa ma zana awiri pa dziko lonse amene amakonza za maulendo. Ambiri mwa iwo ndi oima paokha.



English : The Global Running Tours successor, Go Running Tours networks dozens of sightrunning providers on four continents.

Nyanja : Mlowa malo wa Global Running Tours, Go Running Tours amalumikizana ndi magulu okonza ma ulendo m´ma Kontinenti anayi.



English : With roots in Barcelona´s Running Tours Barcelona and Copenhagen´s Running Copenhagen, it was quickly joined by Running Tours Prague based in Prague and others.

Nyanja : Poti pali ubale ku Barcelona ndi Running Tours Barcelona komanso ku Copenhagen ndi Running Copenhagen, inapanga ubale ndi Runing Tours Prague yaku Prague.



English : There are many things you have to take into consideration before and when you travel somewhere.

Nyanja : Pamakhala zinthu zochuluka zimene muyenera kuzilingalira musananyamuke mwinaso pamene mukupita malo ena.



English : When you travel, expect things not to be like they are ¨back home¨. Manners, laws, food, traffic, lodging, standards, language and so on will to some extent differ from where you live.

Nyanja : Pamene muli pa ulendo, dziwani kuti zinthu zina sizifanana ngati za "kwanu". Ulemu, malamulo, chakudya, magalimoto, malo ogona, milingo, chilankhulo ndi zinaso sizingafanane ndi kumene mumakhala.



English : This is something you always need to keep in mind, to avoid disappointment or perhaps even distaste over local ways to do things.

Nyanja : Ichi ndi chomwe mukuyenera kukumbukira nthawi zonse, kupewa kukhumudwitsidwa kapena kusokoneza njira zomwe muchitira zinthu.



English : Travel agencies have been around since the 19th century. A travel agent is usually a good option for a journey which extends beyond a traveller´s previous experience of nature, culture, language or low-income countries.

Nyanja : Amkhala pakati amaulendo akhala alipo kuyambira mzaka zamzana khumi ndi chisanu mchinayi. Mkhala pakati waulendo ndiwofunika makamaka pamene ulendo wanu ndiwofuna kuwona zosiyana ndizimene mudakomana nawo wam´mbuyomu pazachilengedwe, chikhalidwe, chilankhulo kapena mayiko omwe chuma chawo chili chotsika.



English : Although most agencies are willing to take on most regular bookings, many agents specialise in particular types of travel, budget ranges or destinations.

Nyanja : Ngakhale mabungwe ochuluka amafunitsitsa kusungitsa malo pafupipafupi, amkhalapakati ambiri anazama pamitundu ina yamaulendo, gawo la zachuma kapena komwe anthu angapite.



English : It can be better to use an agent who frequently books similar trips to yours.

Nyanja : Kutha kukhala koyenera kugwiritsa ntchito mkhalapakati amene kawirikawiri amapeza maulendo ofanana ngati anu.



English : Take a look at what trips the agent is promoting, whether on a website or in a shop window.

Nyanja : Onanai maulendo amene mkhalapakati akulimbikitsa, kaya pa tsamba la intaneti kapena pawindo la shopu.



[Day34]

English : If you want to see the world on the cheap, for necessity, lifestyle or challenge, there are some ways to do that.

Nyanja : Ngati mungafune kuona dziko losadula, zofunikira, makhalidwe ndi zoletsa, pali njira zina zomwe mungapange.



English : Basically, they fall into two categories: Either work while you travel or try and limit your expenses. This article is focused on the latter.

Nyanja : Kwenikweni zimakhala m´magawo awiri: Kugwira ntchito pamene uli koyendako kapena muyese kuchepesa zogulagula. Nkhaniyi ikukamba kwambiri njira yochepetsa zogulagula.



English : For those willing to sacrifice comfort, time and predictability to push expenses down close to zero, see minimum budget travel.

Nyanja : Kwa iwo omwe akufuna kutaya kutakasuka, nthawi, komaso kulosera zam´mene mungachepetsere zogula zanu mpaka pa ziro, wonani ndondomeko ya ndalama yosachepera ya ulendo.



English : The advice assumes that travellers do not steal, trespass, participate in the illegal market, beg, or otherwise exploit other people for their own gain.

Nyanja : Malangizo akuganizila kuti anthu apaulendo samaba, kupita malo aeni opanda chilolezo kapena kutenga mbali pa misika yosaloledwa, kupemphetsa kapenanso kubela anthu ena.



English : An immigration checkpoint is usually the first stop when disembarking from a plane, a ship, or another vehicle.

Nyanja : Malo owona za anthu olowa ndikutuluka ndiwo oyambilira kuyimapo mukatsika ndege, sitima kapena galimoto ina.



English : In some cross-border trains inspections are done on the running train and you should have valid ID with you when boarding one of those trains.

Nyanja : Oyendela mmasitima ena apantunda owoloka amalire a maiko amayendela sitima ikuyenda ndiye muyenela kukhala ndi makalata oyenela a ulendo pokwela.



English : On night sleeper trains, passports may be collected by the conductor so that you do not have your sleep interrupted.

Nyanja : Masitima ogona usiku, ziphaso zoyendera zimatha kutengedwa ndi wochititsa kuti musalore kuti kugona kwanu kusokonezedwe.



English : Registration is an additional requirement for the visa process. In some countries, you must register your presence and address where you are staying with the local authorities.

Nyanja : Kulembetsa ndi china chofunikira zedi popanga chilolezo chokhalira dera lina, m´maiko ena umayenera kulembetsa ndi akulu aboma.



English : This might require filling out a form with the local police or a visit to the immigration offices.

Nyanja : Izi zikhoza kufuna kulemba pa fomu yapolisi yakudera komweko kapena kupita ku ma ofesi owona anthu olowa ndi kutuluka mdziko.



English : In many countries with such a law, local hotels will handle the registration (make sure to ask).

Nyanja : M´mayiko ambiri omwe ali ndi lamulo ngati ili, malo ogonamo amdzikomo amapanga kalembera (muyenera kufusa ndithu).



English : In other cases, only those staying outside of tourist accommodations need to register. However, this makes the law much more obscure, so find out beforehand.

Nyanja : Mu nthawi zambiri zina, omwe amene amakhala kunja kwa malo omwe kuli alendo ayenera kulembetsa. Choncho , izi zimapangitsa kuti lamuloli lisaoneke bwino kwambiri, choncho fufuziranitu.



English : Architecture is concerned with the design and construction of buildings. The architecture of a place is often a tourist attraction in its own right.

Nyanja : Ukadaulo ojambula nyumba umagona pakajambulidwe ndi kamangidwe ka nyumba. Kajambulidwe ka nyumba pamalo pakokha kumakhala kochititsa chidwi kwa alendo.



English : Many buildings are quite beautiful to look at and the view from a tall building or from a cleverly-positioned window can be a beauty to behold.

Nyanja : Manyumba ambiri ndiokongola kwambiri m´maonekedwe ake komanso maonekedwe ochokera nyumba yayitali kapena pazenera lokhala mwaluso akhoza kukhala okongola kuwona.



English : Architecture overlaps considerably with other fields including urban planning, civil engineering, decorative arts, interior design and landscape design.

Nyanja : Ntchito zomangamanga zimakhudzana ndi magawo ena kwambiri kuphatikizirapo mapulani a m´matauni, zomangamanga zaluso, zokongoletsa, kapangidwe kazamkati ndi maonekedwe.



English : Given how remote many of the pueblos are, you won´t be able to find a significant amount of nightlife without traveling to Albuquerque or Santa Fe.

Nyanja : Popeza ma pueblo ambiri amakhala ngati kutali, simungapeze moyo wazochitika wausiku musanapite ku Albuquerque kapena Santa Fe.



English : However, nearly all of the casinos listed above serve drinks, and several of them bring in name-brand entertainment (primarily the large ones immediately surrounding Albuquerque and Santa Fe).

Nyanja : Choncho, pafupifupi makasino onse ali pamndandanda pamwambapo amakhala ndizakumwa, ndipo ambiri ayiwo amabweretsa zisangalaro zotchuka (makamaka zikuluzikulu zongulira madera a Albuquerque ndi Santa Fe).



English : Beware: small-town bars here are not always good places for the out-of-state visitor to hang out.

Nyanja : Chenjezo: malo omwerako mowa opezeka mtimizinda ting´onoting´ono siabwino kuchezako nthawi zonse kwa alendo omwe akuchokera kunja.



English : For one thing, northern New Mexico has significant problems with drunk driving, and the concentration of intoxicated drivers is high close to small-town bars.

Nyanja : Pachifukwa chimodzi, kumpoto kwa New Mexico kuli mavuto akulu oyendetsa galimoto utamwa mowa, ndipo kuchuluka kwa woyendetsa magalimoto ataledzerawa ndi kwakukulu pafupi ndi m´matauni ang´onoang´ono omwerako mowa.



English : Unwanted murals or scribble is known as graffiti.

Nyanja : Zithunzi zopanda pake kapena zojambula ndimanja pa khoma zimatchedwa graffiti.



English : While it´s far from a modern phenomenon, most people probably associate it with youth vandalizing public and private property using spray paint.

Nyanja : Ngakhale zili kutali ndi zochitika masiku ano anthu ambiri amaona kuti ndiyofanana ndi magulu achinyamata owononga katundu wa dziko ndi waeni pogwilitsa ntchito utoto.



English : However, nowadays there are established graffiti artists, graffiti events and ¨legal¨ walls. Graffiti paintings in this context often resemble artworks rather than illegible tags.

Nyanja : Choncho, masiku ano kuli ojambula ovomelezeka, zochitika za zojambula ndiponso "pamakoma ovomelezeka". Zojambula zamtunduwu nthawi zambiri zimafanana ndi maluso zambiri kusiyana ndi ma tag osavomelezeka.



English : Boomerang throwing is a popular skill that many tourists want to acquire.

Nyanja : Kuponya Boomerang ndi luso lomwe alendo ambiri amafuna ataphunzira.



English : If you want to learn throwing a boomerang that comes back to your hand, make sure you have a suitable boomerang for returning.

Nyanja : Ngati mukufuna kudziwa kuponya Chida chomwe chimabweleranso, muyenera kuwonetsetsa kuti muli ndi chinanso chobwelera.



English : Most boomerangs available in Australia are in fact non-returning. It is best for beginners to not try throwing in windy

Nyanja : Ma boomerang ambiri omwe alipo ku Australia kwenikweni ndi osabwerera m´mbuyo. Ndikwabwino kwa omwe ayamba kumene asazitengere kwambiri.



English : A Hangi Meal is cooked in a hot pit in the ground.

Nyanja : Chakudya cha chi Hangi chimaphikidwa mudzenje lotentha pansi pa nthaka.



[Day35]

English : The pit is either heated with hot stones from a fire, or in some places geothermal heat makes areas of ground naturally hot.

Nyanja : Dzenjelo limatentha kamba ka miyala yotentha imene imachokera kumoto, nthawi zima m´malo ena kutentha kwa mphamvu ya chilengedwe kumachititsa kuti madera ena apansi akhale wotentha mwachilengedwe.



English : The hangi is often used to cook a traditional roast style dinner.

Nyanja : Chida cha Hangi kawirikawiri chimagwiritsidwa ntchito pophika chakudya chowotcha chamadzulo.



English : Several places in Rotorua offer geothermal hangi, while other hangi can be sampled in Christchurch, Wellington and elsewhere.

Nyanja : Malo ambiri ku Rotorua amakhala ndi mphamvu ya miyala ya hangi, pamene hangi angathe kupezeka ku Christchurch, Wellington ndi kwina konse.



English : MetroRail has two classes on commuter trains in and around Cape Town: MetroPlus (also called First Class) and Metro (called Third Class).

Nyanja : MetroRail ili ndi magawo awiri mu masitima anjanje omwe amakwera oyenda ndikuzungulira mu Cape Town: MetroPlus (imene imatchedwanso Kalasi Yoyamba) ndi Metro (yotchedwa Kalasi Yachitatu).



English : MetroPlus is more comfortable and less crowded but slightly more expensive, though still cheaper than normal metro tickets in Europe.

Nyanja : MetroPlus ndiyotakasuka komanso simudzadza kwambiri koma mitengo yao ndiyokwelelapo ngakhale ndiyotsika kuposa mametro tikiti ambiri ku Ulaya.



English : Every train has both MetroPlus and Metro coaches; the MetroPlus coaches are always on the end of the train nearest Cape Town.

Nyanja : Sitima iliyonse ili ndi makochi a MetroPlus ndi Metro; ma MetroPlus amakhala chifupi ndi mzinda wa Cape Town.



English : Carrying for others - Never let your bags out of your sight, especially when you are crossing international borders.

Nyanja : Kunyamulira katundu ena- Musayese dala kusiya chikwama chanu pomwe simukutha kuchiona, makamaka pamene mukudutsa malire adziko lina.



English : You could find yourself being used as a drug carrier without your knowledge, which will land you in a great deal of trouble.

Nyanja : Mutha kugwiritsidwa ntchito kunyamula mankhwala ozunguza bongo musakudziwa, zimenezi zizakupezetsani mavuto ochuluka.



English : This includes waiting in line, as drug-sniffing dogs could be used at any time without notice.

Nyanja : Izi zikuphatikizirapo kudikilira pamzere, pamene agalu onukhiza amatha kuwagwiritsa ntchito nthawi iliyonse opanda chenjezo.



English : Some countries have exceedingly draconian punishments even for first time offenses; these can include prison sentences of over 10 years or death.

Nyanja : Mayiko ena ali ndi zilango zokhaulitsa ngakhale kwa omwe alakwitsa koyamba, anthu amawatumiza kundende kwa zaka 10.



English : Unattended bags are a target for theft and can also attract attention from authorities wary of bomb threats.

Nyanja : Zikwama zokhala zokha zimakhala pa chiopsezo chobedwa ndiponso zimapatsa chidwi akuluakulu poganiza kuti mutha kukhala muli bomba.



English : At home, due to this constant exposure to the local germs, odds are very high that you´re already immune to them.

Nyanja : Kunyumba , chifukwa choyandikirana ndi magelemusi , chikhulupiro chilipo kuti uli ndichitetezo chokwera mthupi.



English : But in other parts of the world, where the bacteriological fauna are new to you, you´re far more likely to run into problems.

Nyanja : Madera ena adziko lapansi, kumene nyama za bacteria zili zatsopano kwa inu, mutha kukhala pamavuto wochuluka.



English : Also, in warmer climates bacteria both grow more quickly and survive longer outside the body.

Nyanja : Komanso, mu nyengo yotentha tizilombo ta bakiteriya timakula msanga ndi kupulumuka kwa nthawi yayitali kunja kwa thupi.



English : Thus the scourges of Delhi Belly, the Pharaoh´s Curse, Montezuma´s Revenge, and their many friends.

Nyanja : Ndiye mlili wa Dehli Belly , tembelero la Farao, kubwenzela kwa Montezum ndi anzao ena.



English : As with respiratory problems in colder climates, intestinal problems in hot climates are fairly common and in most cases are distinctly annoying but not really dangerous.

Nyanja : Ndi m´mene zimachitikiraso ndi mavuto akapumidwe kumalo wozizira, kumalo wotentha mavuto am´mimba amachulukirapo choncho nthawi zambiri amasautsa ngakhale siwowopsa.



English : If traveling in a developing country for the first time – or in a new part of the world – don´t underestimate the potential culture shock.

Nyanja : Ngati mupita ku dziko lotukuka kumene koyamba - kapena malo ena a chilendo - musanyalanyaza kuti patha kukhala kusanvetsesana chifukwa chosiyana chikhalidwe.



English : Many a stable, capable traveler has been overcome by the newness of developing world travel, where many little cultural adjustments can add up quickly.

Nyanja : Oyenda ambiri okhazikika, otha kuchita bwino agonjetsedwa ndi zatsopano zapaulendo wapadziko lonse lapansi, komwe kusintha pang´ono kwazikhalidwe zambiri kumatha kuwonjezeka mwachangu.



English : Especially in your initial days, consider splurging on Western-style and -quality hotels, food, and services to help acclimatize.

Nyanja : Makamaka m´masiku anu oyamba, lingalirani za kukhala malo ogona azikhalidwe zaku maiko akumadzulo komanso malo abwino, chakudya, ndi ntchito zina kuti muzolowere.



English : Do not sleep on a mattress or pad on the ground in areas where you do not know the local fauna.

Nyanja : Osagona pa matilesi pansi mdera lomwe zinyama zake simukuzidziwa.



English : If you are going to camp out, bring a camp cot or hammock to keep you away from snakes, scorpions and such.

Nyanja : Pamene mukufuna kokamanga msasa, tengani kama komanso machira kuti musakalumidwe ndi njoka, zinkhanira ndiponso zina zotero.



English : Fill your home with a rich coffee in the morning and some relaxing chamomile tea at night.

Nyanja : Dzadzani nyumba yanu ndi khofi wamtengo wapatali nthawi ya m´mawa ndi tiyi wochotsa nkhawa wa chamomile nthawi ya usiku.



English : When you´re on a staycation, you have the time to treat yourself and take a few extra minutes to brew up something special.

Nyanja : Pamene uli pa tchuthi mdziko mwako mom´mo, umakhala ndi nthawi yambiri yosangalala komaso umakhalaso ndi nthawi yoti nkufulula kenakake kapaderadera.



English : If you´re feeling more adventurous, take the opportunity to juice or blend up some smoothies:

Nyanja : Ngati mukumva kuti mufuna kudziwa zambiri, mwayi ndiwomwewu wopanga juwisi kapena pangani juwisi pogwiritsa ntchito makina otchedwa blender.



English : maybe you´ll discover a simple beverage that you can make for breakfast when you´re back to your daily routine.

Nyanja : Mwina mutha kupeza chakumwa chosavuta kukonza chomwe mungagwiritse ntchito pa chakudya chanu cham´mawa pamene mukubwelera ku ntchito zanu zamasiku onse.



[Day36]

English : If you live in a city with a varied drinking culture, go to bars or pubs in neighborhoods you don´t frequent.

Nyanja : Ngati ukukhala mu mzinda umene uli ndi miyambo yosiyanasiyana ya kamwedwe, pita kumalo omwela mowa amene ali mudela lomwe sufikafikako.



English : For those unfamiliar with medical jargon, the words infectious and contagious have distinct meanings.

Nyanja : Kwa amene sadziwa mawu omwe amagwiritsa ntchito ndi azachipatala, mawu oti kupatsirana matenda pakati pa anthu podzera ku tizirombo kapena ndi anthu okhaokha ndi mawu woti kupatsirana matenda pakati pa anthu okhaokha basi ali ndi matanthauzo awoawo.



English : An infectious disease is one that is caused by a pathogen, such as a virus, bacterium, fungus or other parasites.

Nyanja : Matenda opatsirana ndi amene amayamba chifukwa cha tizilombo, ngati ma vayilasi, bakiteliya, fangasi kapena ena ma parazayiti.



English : A contagious disease is a disease which is easily transmitted by being in the vicinity of an infected person.

Nyanja : Matenda opatsilana ndi matenda amene amapatsilana mosavuta pamene mwayandikana ndi odwalayo.



English : Many governments require visitors entering, or residents leaving, their countries to be vaccinated for a range of diseases.

Nyanja : Maboma ambiri amafuna alendo olowa, kapena eni nthaka ochoka, maiko awo kulandira katemera wamatenda osiyanasiyana.



English : These requirements may often depend on what countries a traveller has visited or intends to visit.

Nyanja : Malamulo amatengera kawirikawiri mayiko omwe muNthu wapita kapena komwe akufuna apite.



English : One of strong points of Charlotte, North Carolina, is that it has an abundance of high-quality options for families.

Nyanja : Chimodzi mwazinthu zamphamvu ku Charlotte, ku North Carolina ndikuchuluka kwa zinthu zapamwamba zoyenera mabanja.



English : Residents from other areas often cite family-friendliness as a primary reason for moving there, and visitors often find the city easy to enjoy with children around.

Nyanja : Anthu okhala madela ena nthawi zambiri amatchula ma ubale am´mabanja ngati chifukwa choyambilira chopitila kumeneko ndipo alendo nthawi zambiri amapeza kuti mzinda suvuta kusangalala ndi ana.



English : In the past 20 years, the amount of child-friendly options in Uptown Charlotte has grown exponentially.

Nyanja : Zaka 20 zapitazo, kupezeka kwambiri kwa zoti musankhe zimene zili zokomera ana ku Uptown Charlotte zakula kwambiri.



English : Taxis are not generally used by families in Charlotte, though they can be of some use in certain circumstances.

Nyanja : Magalimoto amatola samagwiritsidwa ntchito ndi mabanja ku Charlotte, ngakhale akhoza kukhala othandiza munjira zina.



English : There is a surcharge for having more than 2 passengers, so this option might be more expensive than necessary.

Nyanja : Pali kuonjezera malipilidwe anthu awili akakhala pa mpando, choncho izi zimakhala zokwelerapo mtengo.



English : Antarctica is the coldest place on Earth, and surrounds the South Pole.

Nyanja : Kwa Antarctica ndikozizira mopitilira muyezo pa dziko lonse lapansi, komanso lidazungulira South Pole.



English : Tourist visits are costly, demand physical fitness, can only take place in summer Nov-Feb, and are largely limited to the Peninsula, Islands and Ross Sea.

Nyanja : Maulendo azokopa alendo ndiwokwera mtengo, amafuna kukhala olimba mthupi, amatha kuchitika mnyengo yachilimwe kuyambira Novembala-Febuluwale, ndipo amakhala kumalo owerengeka monga ku Chisumbu, Zilumba komaso kunyanja ya Ross.



English : A couple of thousand staff live here in summer in some four dozen bases mostly in those areas; a small number stay over winter.

Nyanja : Anthu ogwira ntchito zikwi amakhala kuno nthawi yotentha mu manyumba makumi anayi, asanu ndi atatu makamaka malo amenewo; anthu ochepa okha amakhala kuno nyengo yozizira.



English : Inland Antarctica is a desolate plateau covered by 2-3 km of ice.

Nyanja : Nkatikati mwa Antartica muli phiri lokutidwa ndi madzi owuma kwa ntunda wautali ngati makilomita 2 mpaka 3.



English : Occasional specialist air tours go inland, for mountaineering or to reach the Pole, which has a large base.

Nyanja : Akadaulo oyenda m´mwamba pena amayenda pamtunda, basi kulizungulira phiri kapena kufika kunsonga kwenikweni kwa dziko koma ndikotakasuka.



English : The South Pole Traverse (or Highway) is a 1600 km trail from McMurdo Station on the Ross Sea to the Pole.

Nyanja : South Pole Traverse (kapena Msewu waukulu) ndi msewu wotalika makilomita 1600 kuchokera ku McMurdo Station ku Ross Sea kupita kumapeto kwa Pole.



English : It´s compacted snow with crevasses filled in and marked by flags. It can only be traveled by specialized tractors, hauling sleds with fuel and supplies.

Nyanja : Ndimadzi ouma ofewa koma othinana omwe ali ndi ming´alu ikuluikulu yomwe ili ndizizindikiro. Kutha kuyendedwa ndi ma thirakitale apadera, magalimoto oyenda pamadzi owuma atanyamula mafuta ndi akatundu ena.



English : These aren´t very nimble so the trail has to take a long swerve around the Transantarctic Mountains to come onto the plateau.

Nyanja : Zimenezi sizotakasuka moyenera choncho njirayo ndiyokhota kwambiri kuti ikazungulire Mapiri a Transantarctic kuti ikafike pa mwamba pa chigwa.



English : The most common cause for accidents in winter is slippery roads, pavements (sidewalks) and especially steps.

Nyanja : Zimene zimayambisa ngozi zambiri munthawi yozizira ndi misewu yotelela, njira zoyendamo (moyenda anthu apasi) komaso masitepe.



English : At a minimum, you need footwear with suitable soles. Summer shoes are usually very slippery on ice and snow, even some winter boots are deficient.

Nyanja : Mosachepera, mukhale ndi nsapato zomwe zazidendene zabwino. Nsapato za nthawi yotentha nthawi zambiri zimakhala zotelera pa madzi wowuma ofewa, ngakhaleso nsapato za nthawi yozizira zimakhala zosakwanira.



English : The pattern should be deep enough, 5 mm (1/5 inch) or more, and the material soft enough in cold temperatures.

Nyanja : Kachitidwe kake kayenera kakhale kokwanira, 5mm (1/5 inchi) mwinanso kuposera apo, komanso zinthuzo ndizofewa malingana ndi kunthawi yozizira.



English : Some boots have studs and there is studded add-on equipment for slippery conditions, suitable for most shoes and boots, for the heels or heels and sole.

Nyanja : Nsapato zitalizitali zina zimakhala toyimilira tambiri tozaza pansi pansapato ponse ndipo palinso zida zina zokhala ndi toyimilirati timene timagwiritsidwa ntchito ngati pansi pakutelera, zoyenera ku nsapato zambiri ndi nsapato zitalizitali, zidendene kapena zidendene ndichapansi cha nsapato.



English : Heels should be low and wide. Sand, gravel or salt (calcium chloride) is often scattered on roads or paths to improve traction.

Nyanja : Zidendene ndi zofunika kuti zikhale zotsika komanso zotambalala. Mchenga, miyala kapena mchere (calcium chloride) kawirikawiri zimakhala zamwazidwa m´misewu mwinanso mnjira pothandiza kuchepesa kutelera.



English : Avalanches are not an abnormality; steep slopes can hold only so much slow, and the excess volumes will come down as avalanches.

Nyanja : Ma avalanche siachilendo; mapiri otsetseleka amatha kuchepa, ndipo kuchuluka kwake kumatsika ngati ma avalanche.



[Day37]

English : The problem is that snow is sticky, so it needs some triggering to come down, and some snow coming down can be the triggering event for the rest.

Nyanja : Vuto ndilakuti Chipale chimamata, choncho chimafunika kusungunura, ndipo chipale china chimatheka kuyambitsa zinthu zinanso zambiri.



English : Sometimes the original trigging event is the sun warming the snow, sometimes some more snowfall, sometimes other natural events, often a human.

Nyanja : Nthawi zina chochititsa choyambirira chimakhala ndi dzuwa kutenthetsa madzi owuma, nthawi zina kugwa madzi owuma owundana wofewa ochulukirapo, nthawi zina zochitika zina za chilengedwe, kawirikawiri munthu.



English : A tornado is a spinning column of very low-pressure air, which sucks the surrounding air inward and upward.

Nyanja : Nkuntho ndi mpweya umene umazungulira umene umakhala wochepa mphanvu ndipo umayamwa mpweya ozungulira kuukokela mkati komanso mokweza.



English : They generate high winds (often 100-200 miles/hour) and can lift heavy objects into the air, carrying them as the tornado moves.

Nyanja : Zimapanga mphepo ya mkuntho (nthawi zambiri mamayilosi 100-200 / ola) ndipo amatha kuwulutsa zinthu zolemera kupita mumlengalenga, ndikuzinyamula komwe tornado akupita.



English : They begin as funnels descending from storm clouds, and become ¨tornadoes¨ when they touch the ground.

Nyanja : Zimayamba ngati ma fanelo kutsika kumitambo ndipo nkukhala "kamvuluvulu" akafika pansi.



English : Personal VPN (virtual private network) providers are an excellent way of circumventing both political censorship and commercial IP-geofiltering.

Nyanja : Anthu omwe ali ndi VPN (Virtual Private Network) ma netiweki achinsinsi ndi njira yabwino yopewa kuthana ndi ndale komanso IP geofiltering.



English : They are superior to web proxies for several reasons: They re-route all Internet traffic, not only http.

Nyanja : Ndiakadaulo pa nkhani ya katumizidwe ka mauthenga pa intaneti pazifukwa zingapo: Amatumiza mauthenga apa intaneti munjira zambiri, osati http yokha.



English : They normally offer higher bandwidth and better quality of service. They are encrypted and thus harder to spy on.

Nyanja : Nthawi zambiri amapereka mphamvu yothamanga yambiri ndiposo ntchito yapamwamba. Zinthu zimatumizidwa mwachinsisi zoti simungathe kuziziwa ndipo zimapangisa kuti zikhale zovuta kwa akazitape.



English : The media companies routinely lie about the purpose of this, claiming that it is to ¨prevent piracy¨.

Nyanja : Makampani wofalitsa nkhani ndichizolowezi chawo kunama pa cholinga chake, ponena kuti "akuteteza chinsinsi".



English : In fact, region codes have absolutely no effect on illegal copying; a bit-for-bit copy of a disk will play just fine on any device where the original will.

Nyanja : Zoona zake, ma code amchigawo alibe zovuta pakukopera mosaloledwa; kukopa kwazonse mu disk ikasewera bwinobwino pachida chilichonse pamene disk yeniyeniyo itha kusewera.



English : The actual purpose is to give those companies more control over their markets; it´s all about money spinning.

Nyanja : Cholinga chenicheni ndichopereka mphamvu kumakampani zoti azitha kuwongolera misika yawo; zonsezi ndinkhani ya ndalama basi.



English : Because calls are routed over the Internet, you do not need to use a phone company located where you live or where you travel.

Nyanja : Kamba kakuti mafoni amayendetsedwa pa intaneti, simukuyenera kugwiritsa ntchio kampani ya mafoni yokhala kumene muli kapena mukupita.



English : There is also no requirement that you obtain a local number from the community in which you live; you can obtain a satellite Internet connection in the wilds of Chicken, Alaska and select a number which claims you´re in sunny Arizona.

Nyanja : Sikuliso kofunikira kuti mupeze nambala yakudera komwe mukukhala; mutha kupeza malumikizidwe a intaneti pozera satellite ku tchire la Nkhuku, Alaska ndipo sankhani nambala yomwe ikukuwuzani kuti muli ku Arizona.



English : Often, you have to buy a global number separately that allows PSTN phones to call you. Where the number is from makes a difference for people calling you.

Nyanja : Kawirikawiri mukufunika kuti mugule nambala yogwira dziko lonse mwapadera imene sikana mafoni a PSTN akakuyimbirani. Kumene nambala ikuchokera kumachititsa kusiyana ndi kumene anthu akuyimbira.



English : Real-time text translator apps – applications that are capable of automatically translating whole segments of text from one language into another.

Nyanja : Mapulogamu omwe amamasulira nthawi yomweyo- ali ndi kuthekera komasulira magawo onse a zolemba kuchokera ku chilankhulo china kupita ku china.



English : Some of the applications in this category can even translate texts in foreign languages on signs or other objects in the real world when the user points the smartphone towards those objects.

Nyanja : Mwazina zomwe zili mugulu ili zitha kutanthauzira zolembedwa muzilankhulo zakunja malingana ndi zizindikiro kapena zinthu zenizeni zina zomwe zaonetsedwa pamene ogwiritsa ntchito akuloza foni yake yam´manja ku zinthuzi.



English : The translation engines have improved dramatically, and now often give more or less correct translations (and more seldom gibberish), but some care is due, as they still may have gotten it all wrong.

Nyanja : Makina omasulira asintha bwino kwambiri, ndipo panopa kawirkawiri amapereka zambiri zomasulira molondola (osati zopanda pake kwenikweni), koma kumafunika kusamala ndithu, chifukwa akhoza kukhala kuti adalakwisa zonse.



English : One of the most prominent apps in this category is Google Translate, which allows offline translation after downloading the desired language data.

Nyanja : Imodzi mwa mapulogalamu odziwika kwambiri m´gululi ndi Google Translate, yomwe imalola kutanthauzira popanda kukhala pa intaneti ngati mwatenga kale kuchokera pa intanenti zofunikira zachilankhulo chomwe mukufuna.



English : Using GPS navigation apps on your smartphone can be the easiest and most convenient way to navigate when out of your home country.

Nyanja : Kugwiritsa ntchito mapulogalamu a GPS mumafoni anu am´manja kutha kukhala kosavuta komaso njira yothandiza kuti musavutike kudziwa m´mene mungayendere kumalo pamene muli kunja kwa dziko lanu.



English : It can save money over buying new maps for a GPS, or a standalone GPS device or renting one from a car rental company.

Nyanja : Zitha kupangisa kuti musaononge ndalama pamene mwagula ma mapu amakono a GPS, mwina chida cha GPS ngakhale kubwereka kumene imodzi ku kampani ya malonda wobwereketsa magalimoto.



English : If you don´t have a data connection for your phone, or when it is out of range, their performance can be limited or unavailable.

Nyanja : Ngati mulibe kulumikizana kwama intaneti pafoni yanu, kapena ikakhala kuti ili kutali ndi netiweki, magwiridwe ake antchito amakhala ochepa kapena ena samayipeza.



English : Every corner store is filled with a confusing array of pre-paid phone cards that can be used from pay phones or ordinary telephones.

Nyanja : Sitolo ina iliyonse imene ili pangodya ikumadzaza ndi makadi a foni omwe akhoza kugwiritsidwa ntchito pama foni olipira kapena matelefoni wamba.



English : While most cards are good for calling anywhere, some specialise in providing favourable call rates to specific groups of countries.

Nyanja : Pamene makhadi ena ndi abwino kuimbira kulikonse, ena umalipira mtengo wina wapadera ku maiko ena.



English : Access to these services is often through a toll-free telephone number that can be called from most phones without charge.

Nyanja : Kufikila kuthandizoli kumakhala kudzela m´matelefoni aulere amene utha kuimbila mafoni ambili osalipila kanthu.



English : Rules regarding regular photography also apply to video recording, possibly even more so.

Nyanja : Malamulo okhudzana ndi zojambula nthawi zonse amagwiritsidwa ntchitonso pojambula kanema, mwinanso kuposera pamenepo.



[Day38]

English : If just taking a photo of something isn´t allowed, then you shouldn´t even think of recording a video of it.

Nyanja : Ngati kujambula chithunzi chilichonse nkosaloledwa, ndiye musayelekeze dala kuganiza zopanga kanema.



English : If using a drone, check well in advance as to what you are allowed to film and what permits or additional licensing are required.

Nyanja : Ngati mukugwilitsa ntchito chowulutsa chotchedwa drone, mukuyenera muoneretu zomwe mukuyenera kujambula kapena chilolezo chapadera ngati chikufunikira.



English : Flying a drone near an airport or over a crowd is almost always a bad idea, even if it´s not illegal in your area.

Nyanja : Kuyendetsa dironi pafupi ndi bwalo la ndege kapena pagulu la anthu nthawi zonse kumakhala kuganiza molakwika, ngakhale ndizololedwa ndi malamulo mdera lanu.



English : Nowadays air travel is only rarely booked directly through the airline without first searching and comparing prices.

Nyanja : Masiku ano maulendo a pandege sakulipidwa ku makampani a ndege popanda munthu kufufuza ndi kufananiza mitengo.



English : Sometimes the same flight can have vastly differing prices at various agregators and it pays to compare search results and to also look at the website of the airline itself before booking.

Nyanja : Masiku ena ndege yomweyo itha kuwonetsa mitengo yosiyana zedi pa ma agregator osiyanaso choncho zimathandiza kuti musiyanitse zomwe munapeza posaka ndiponso kuwona tsamba la intanenti la ndegeyo musanagule.



English : While you may not need a visa for short visits to certain countries as a tourist or for business, going there as an international student generally requires a longer stay than going there just as a casual tourist.

Nyanja : Mwina mutha kusafuna Visa pamaulendo okhala masiku ochepa kumayiko ena pamene mwalowa ngati alendo kapena ochita bizinezi, koma kupita ngati wophunzira wochokera kunja pamafunika kuti mukakhale nthawi yaitali kusiyana ndikupita ngati okacheza.



English : In general, staying in any foreign country for an extended period of time will require you to obtain a visa in advance.

Nyanja : Tingonena kuti kukhala mudziko laweni nthawi yayitali kumafunika zikalata zokuyeneleza kukhalako, zija amati visa.



English : Student visas generally have different requirements and application procedures from normal tourist or business visas.

Nyanja : Chilorezo chokhalira mdziko cha ophunzira ochokera mmaiko ena nthawi zambiri chimakhala ndi zofunikira zambiri komanso ndondomeko zogwiritsila ntchito zosiyana ndi chilorezo cha alendo kapena amalonda.



English : For most countries, you will need an offer letter from the institution you wish to study at, and also evidence of funds to support yourself for at least the first year of your course.

Nyanja : Kwa mayiko ambiri, mudzafunika kalata yopereka kuchokera ku bungwe lomwe mukufuna kukaphunzirira, komanso umboni wa ndalama zodzithandizira zosachepera chaka choyamba chamaphunziro anu.



English : Check with the institution, as well as the immigration department for the country you wish to study in for detailed requirements.

Nyanja : Funsani ku Sukulu, komanso dipatimenti yowona anthu olowa ndi kutuluka mdziko lomwe mukufuna kukaphunzirako kuti mudziwe zofunikira.



English : Unless you are a diplomat, working overseas generally means that you will have to file income tax in the country you are based in.

Nyanja : Pokhapokha mukhale kazembe waboma, kugwira ntchito kunja kwa dziko lanu kukutanthauza kuti muyenera kupereka msonkho pazomwe mukupeza mdziko lomwe mulimo.



English : Income tax is structured differently in different countries, and the tax rates and brackets vary widely from one country to another.

Nyanja : Msonkho umene umaperekedwa pa ndalama zimene anthu apeza umapangidwa mosiyanasiyana m´maiko osiyanaso, ndipo mulingo woperekera umasintha ukachoka dziko lina kupita lina.



English : In some federal countries, such as the United States and Canada, income tax is levied both at the federal level and at the local level, so the rates and brackets can vary from region to region.

Nyanja : M´mayiko ena achitaganya, monga United States ndi Canada, misonkho imatoleledwa kuchitaganya komanso kumaderako, chifukwa chake mitengo imatha kusiyanasiyana kudera ndi dera.



English : While immigration check is usually absent or a formality when you arrive in your homeland, customs control can be a hassle.

Nyanja : Ngakhale chipikisheni cha anthu olowa nthawi zambiri sichichitika kapena zoyenera kuchitika mukafika kwanu, kulongosora miyambo kumatha kukhala kovuta.



English : Make sure you know what you can and cannot bring in and declare anything over the legal limits.

Nyanja : Onetsetsani kuti mukudziwa zomwe muyenera kutenga kapena kusatenga ndipo munene chilichonse chomwe chapitilira mulingo wovomerezeka ndi malamulo.



English : The easiest way to get started in the business of travel writing is to hone your skills on an established travel blog website.

Nyanja : Njira yosavuta kuyamba bizinezi yolemba za maulendo ndi kuphunzila izi patsamba lokhazikika la maulendo.



English : After you become comfortable with formatting and editing on the web, then later, you might create your own website.

Nyanja : Pamene mwakhala omasuka ndi kupanga komanso kusintha pa intaneti, ndiye kenako, mukhoza kupanga tsamba lanu.



English : Volunteering while travelling is a great way to make a difference but it´s not just about giving.

Nyanja : Kudzipereka pamene mukuyenda ndi njira yabwino yothandiza kukhala thandizo koma sizitathauza kuti ndikupeleka kokha.



English : Living and volunteering in a foreign country is a great way to get to know a different culture, meet new people, learn about yourself, get a sense of perspective and even gain new skills.

Nyanja : Kukhala ndi kudzipereka kudziko lina ndi njira yabwino yodziwira chikhalidwe china, kukumana ndi anthu atsopano, kuziphunzira imwe mwini, kukhala ndi malingaliro komanso ngakhale kupeza maluso atsopano.



English : It can also be a good way to stretch a budget to allow a longer stay somewhere since many volunteer jobs provide room and board and a few pay a small salary.

Nyanja : Ithanso kukhala njira yabwino kupanga ndondomeko yazandalama yayikulu kuti mukakhale malo ena chifukwa ntchito zina zongothandiza zimaperaka chipinda ndi mayendedwe ndi malipiro wochepa.



English : Vikings used the Russian waterways to get to the Black Sea and Caspian Sea. Parts of these routes can still be used. Check possible need for special permits, which may be difficult to get.

Nyanja : Ma Vikings ankagwilitsa ntchito njira za m´madzi za ku Russia kupita ku nyanja za Black ndi Caspian. Mbali za njira zimenezi zimatha kugwiritsidwa ntchito. Fufuzani zilolezo zapadela zimene zitha kukhala zovuta kuzipeza.



English : The White Sea–Baltic Canal connects the Arctic Ocean to the Baltic Sea, via Lake Onega, Lake Ladoga and Saint Petersburg, mostly by rivers and lakes.

Nyanja : Nyanja ya Arctic ku Baltic Sea, inalumikizana ndi White Sea- Baltic Canal, podzera pa Nyanja ya Onega, Nyanja ya Ladoga komanso Saint Petersburg, makamaka pa mitsinje ndi nyanja.



English : Lake Onega is also connected to Volga, so coming from the Caspian Sea through Russia is still possible.

Nyanja : Nyanja ya Onega idagundanizananso ndi Volga, choncho ndikotheka kuchoka ku Nyanja ya Caspian kudutsa ku Russia.



English : Be assured that once you hit the marinas everything will be pretty obvious. You will meet other boat hitchhikers and they will share their information with you.

Nyanja : Tsikimizani kuti pamene mwafika pa marinas zonse zikhala zodziwikilatu. Mukumana ndi enanso oyenda pa nyanja amene akudziwitseni zina zomwe amadziwa.



English : Basically you´ll be putting up notices offering your help, pacing the docks, approaching people cleaning their yachts, trying to make contact with sailors in the bar, etc.

Nyanja : Tingonena kuti mudziyika chidziwitso zofuna chithandizo, kufunsa m´madoko, kufunsa anthu omwe akusamala maboti awo, kuyesera kupeza woyendetsa sitima zam´madzi omwe ali m´malo omwera mowa, ndi zina zotero.



[Day39]

English : Try to talk to as many people as possible. After a while everyone will know you and will give you hints as to which boat is looking for someone.

Nyanja : Yesani kuyankhula ndi anthu ambiri kenako pakadutsa nthawi aliyense adzakudziwani ndipo adzakupatsani mwayi wa boti lomwe mukufuna.



English : You should choose your Frequent Flyer airline in an alliance carefully.

Nyanja : Mukuyenera kusankha ndege ngati Frequent Flyer mumgwirizano wanu mosamala.



English : Although you may think it is intuitive to join the airline you fly most, you should be aware that privileges offered are often different and frequent flyer points may be more generous under a different airline in the same alliance.

Nyanja : Pamene mungaganize kuti nkoyenera kupita ku kampani ya ndege yomwe mumakwera kwambiri, mudziwe kuti mwayi woperekedwa ndi wosiyana ndipo ma point amaperekedwa kwa okwera ndege kawirikawiri akhoza kukhala ambiri pansi pa kamapani ina ya ndege mu mgwirizano omwewo.



English : Airlines such as Emirates, Etihad Airways, Qatar Airways & Turkish Airlines have greatly expanded their services to Africa, and offer connections to many major African cities at competitive rates than other European airlines.

Nyanja : Makampani andege monga Emirates, Etihad Airways, Qatar Airways & Turkish Airlines awonjezera kwambiri maulendo awo ku Afirika, ndipo umatha kulumikiza ulendo kupitaso kumizinda ikuluikuya yaku Afirika pamitengo yabwino kuposa makampani ena aku Ulaya.



English : Turkish Airlines flies to 39 destinations in 30 African countries as of 2014.

Nyanja : Kufikira chaka cha 2014, Turkish Airlines imafikira malo 39 m´maiko 30 aku Afirika.



English : If you have additional travel time, check to see how your total fare quote to Africa compares with a round-the-world fare.

Nyanja : Ngati muli ndi nthawi ina paulendo, muone kuti mtengo ndiwotani kufananitsa ndiku Afilika ndi dziko lonse lapansi.



English : Don´t forget to add in the extra costs of additional visas, departure taxes, ground transportation, etc. for all those places outside of Africa.

Nyanja : Musaiwale kuwonjezera ndalama zina zogwiritsa ntchito monga kuwonjezera ma visa, msonkho wonyamukira, zolipira mayendedwe apansi, ndizina zambiri kumalo onse akunja kwa Afirika.



English : If you want to fly around the world completely in the Southern Hemisphere, the choice of flights and destinations is limited due to the lack of transoceanic routes.

Nyanja : Ngati mukufuna kukwera ndege kuzungulira dziko lonse cha kum´mwera kwa dziko lapansi, chisankho cha ndege ndi malo okafikila ndi wochepa chifukwa cha kusowa njira zodutsa pa nyanja.



English : No airline alliance covers all three ocean crossings in the Southern Hemisphere (and SkyTeam covers none of the crossings).

Nyanja : Palibe mgwirizano wa ulendo wapa ndege umene umakhudza kuwoloka nyanja zonse zitatu ku Southern Hemishephere (ndipo SkyTeam siyidutsa nawo kumalowo).



English : However, Star Alliance covers everything except the eastern South Pacific from Santiago de Chile to Tahiti, which is a LATAM Oneworld flight.

Nyanja : Motero, Star Alliance imayenda kwinakulikonse kupatula ku m´mawa chaku mwera kwa nyanja ya Pacific kuchokera ku Santiago de Chile kupita kufika ku Tahiti, yomwe ndi ndege ya LATAM Oneworld.



English : This flight is not the only option if you want to skip the South Pacific and the west coast of South America. (see below)

Nyanja : Ndege imeneyi siyokhayo yomwe mungasankhe ngati mukufuna kusadzera ku South Pacific ndi gombe lakumadzulo kwa South America. (Onani pansipa)



English : In 1994, the ethnically Armenian Nagorno-Karabakh region of Azerbaijan waged war against the Azeris.

Nyanja : Mu chaka cha 1994, chigawo cha mtundu cha Armenian Nagorno-Karabakh ku dziko la Azerbaijan lidamenya nkhondo kulimbana ndi Azeris.



English : With Armenian backing, a new republic was created. However, no established nation - not even Armenia - officially recognizes it.

Nyanja : Mothandizidwa ndi Armenia, lipabuliki yatsopano idakhazikitsidwa. Choncho, palibe dziko lokhazikika- ngakhale dziko la Armenia-lidavomereza za lipabuliki.



English : Diplomatic arguments over the region continue to mar relations between Armenia and Azerbaijan.

Nyanja : Mkangano waukazembe okhuza deralo zikupitilira kuwononga ubale pakati pa Armenia ndi Azerbaijan.



English : The Canal District (Dutch: Grachtengordel) is the famous 17th-century district surrounding the Binnenstad of Amsterdam.

Nyanja : Boma la Canal (chidatchi: Grachtengordel) ndi malo otchuka amzaka za ma 1600 ozungulira Binnestad ku Amsterdam.



English : The whole district is designated as a UNESCO World Heritage Site for its unique cultural and historical value, and its property values are among the highest of the country.

Nyanja : Boma lonseli adalisankha ngati dera la UNESCO World Heritage chifukwa cha chikhalidwe chawochawo komaso mbiri yake, ndiponso chifukwa cha katundu wake amene ali mgulu lokwera mtengo mdzikomo.



English : Cinque Terre, which means Five Lands, comprises the five small coastal villages of Riomaggiore, Manarola, Corniglia, Vernazza and Monterosso located in the Italian region of Liguria.

Nyanja : Cinque Terre, imene imatanthawuza kuti Maiko Asanu, kuli midzi isanu ying´onoying´ono yamphepete mwanyanja ya Riomaggiore, Manarola, Corniglia, Vernazza komanso Monterosso imene ikupezeka mchigawo cha Liguria mdziko la Italy.



English : They are listed on the UNESCO World Heritage List.

Nyanja : Ali pa mndandanda wa UNESCO World Heritage.



English : Over the centuries, people have carefully built terraces on the rugged, steep landscape right up to the cliffs that overlook the sea.

Nyanja : Patapita zaka mazana ambiri, anthu amanga mosamala masitepe pa malo amabampu, malo otsetseleka mpaka kukafika ku mapiri omwe akuyang´anizana ndi nyanja yayikulu.



English : Part of its charm is the lack of visible corporate development. Paths, trains and boats connect the villages, and cars cannot reach them from the outside.

Nyanja : Mbali ina yaziNthuzi ndichakuti chitukuko chake sichioneka bwinobwino. Njira, masitima ndi maboti amalumikiza midzi, chifukwa magalimoto sangafikeko.



English : The varieties of French which are spoken in Belgium and Switzerland differ slightly from the French spoken in France, though they are similar enough to be mutually intelligible.

Nyanja : Mitundu yachi Falansa imene imalankhulidwa ku Belgium ndi Switzerland imasiyanako ndichi Falansa chimene chimalankhulidwa ku France, ngakhale kuti amafanana kwambiri ndikumva msanga.



English : In particular, the numbering system in French-speaking Belgium and Switzerland has some slight peculiarities that are different from the French spoken in France, and the pronunciation of some words is slightly different.

Nyanja : Makamaka kumbali ya manambala kwa anthu olankhula chi Faransa aku Belgium ndiku Switzerland omwe mayakhulidwe ake amakhala ndi zina zosiyana kufananizira ndi chi Falansa chomwe chimayakhulidwa ku France, ndipo matchulidwe amawu ena amakhala osiyana.



English : Nevertheless, all French-speaking Belgians and Swiss would have learned standard French in school, so they would be able to understand you even if you used the standard French numbering system.

Nyanja : Choncho, onse aku Belgium olankhula chi Falansa ndi aku Switzerland amene adaphunzira chifalansa ku sukulu, kuti azitha kukumvani ngakhale mukagwilitsa ntchito chifalansa polemba ma nambala.



English : In many parts of the world, waving is a friendly gesture, indicating ¨hello.¨

Nyanja : M´maiko ambiri kubaibitsa ndi chizindikilo cha ubale kutanthauza "moni".



English : However, in Malaysia, at least among the Malays in rural areas, it means ¨come over,¨ similar to the index finger bent toward the body, a gesture which is used in certain Western countries, and should be used only for that purpose.

Nyanja : Ngakhale choncho, ku Malysia pafupifupi anthu a ku Malysia ambiri akumidzi, zimatathauza tabwerani chimodzimodzinso ndikachala kochepa kumapeto kakapindidwa kuloza thupi , chisimu chomwe mayiko akunja ambiri amapanga ndipo amagwilitsa ntchito nthawi yokhayi.



[Day40]

English : Similarly, a British traveller in Spain may mistake a wave goodbye involving the palm facing the waver (rather than the person being waved at) as a gesture to come back.

Nyanja : Chimodzimodzi nzika yaku Britain ku Spain itha kusokoneza kutsanzikana kokweza chikhatho chankono moyang´ana ndi wotsanzikanayo kusiyana ndikutsanzika munthu munjirayi, ngati chizindikiro chobweranso.



English : Auxiliary languages are artificial or constructed languages created with the intent of facilitating communication between peoples who would otherwise have difficulty communicating.

Nyanja : Ziyankhulo zothandizira zimachita kupangidwa ndi anthu kuti kumvana kusamavute pakati pawo, zomwe zikadachititsa kulumikizana kuvuta.



English : They are separate from lingua francas, which are natural or organic languages that become dominant for one reason or another as means of communication between speakers of other languages.

Nyanja : Adawasiyanitsa kuchokera ku ziyankhulo za ku France, zomwe zili zilankhulo zachilengedwe, zomwe zidadziwika paliponse ngati njira yolumikizirana kwa oyankhula.



English : In the heat of the day, travelers can experience mirages that give the illusion of water (or other things).

Nyanja : Kukatentha kwambiri makamaka masana ndi m´mawa, woyenda atha kumaona zilubwelubwe zowoneka ngati madzi (kapena zinthu zina).



English : These can be dangerous if the traveler pursue the mirage, wasting precious energy and remaining water.

Nyanja : Izi zitha kukhala zowopsa, ngati woyenda angapitilire kupangitsa kuononga mphamvu ndi madzi wotsala.



English : Even the hottest of deserts can become extremely cold at night. Hypothermia is a real risk without warm clothing.

Nyanja : Ngakhale zipululu zotentha kwambiri zimatha kuzizira kwambiri usiku. Matenda a Hypothermia atha kukhala chiopsezo chenicheni ngati mulibe zovala zofundirako.



English : In summer, especially, you´ll need to watch out for mosquitoes if you decide to hike through the rainforest.

Nyanja : Makamaka mchilimwe musamale kwambiri udzudzu ngati mwaganiza zokayenda mu nkhalango.



English : Even if you´re driving through the subtropical rainforest, a few seconds with the doors open while you get inside the vehicle is enough time for mosquitoes to get in the vehicle with you.

Nyanja : Ngakhale mukudutsa m´nkhalango zam´malo osatentha kwambiri, kanthawi kochepa zitseko zili zotsegula, pamene muzilowaso mgalimoto ndi nthawi yokwanira kwa udzudzu kulowa namu limodzi mgalimoto.



English : Bird flu, or more formally avian influenza, can infect both birds and mammals.

Nyanja : Chimfine cha mbalame, kapena kuti avian influenza, chimatha kukhudza mbalame ndi nyama zomwe.



English : Fewer than a thousand cases have ever been reported in humans, but some of them have been fatal.

Nyanja : Izi zanenedwa kosachepera chikwi zokhuza anthu, koma zina mwayizo zinali zobweretsa imfa.



English : Most have involved people who work with poultry, but there is also some risk to birdwatchers.

Nyanja : Ambiri agwiritsa ntchito anthu amene amagwira ntchito ndi nkhuku, koma palinso chiopsezo kwa amene amakaonelera kuwuluka kwa mbalame.



English : Typical for Norway are steep fjords and valleys that suddenly give way to a high, more or less even plateau.

Nyanja : Makamaka ku Norway kulizikweza ndi zigwa zimene zimangopezeka zafika pachidikha.



English : These plateaus are often referred to as ¨vidde¨ meaning a wide, open treeless space, a boundless expanse.

Nyanja : Mapiriwa amatchedwa "vidde" kutanthauza malo otakasuka, opanda mitengo, chalo chopanda malire.



English : In Rogaland and Agder they are usually called ¨hei¨ meaning a treeless moorland often covered in heather.

Nyanja : Ku Rogaland ndi Agder amatchedwa kuti "hei" kutanthauza kuti moorland wopanda mtengo nthawi zambiri imakhala yokutilidwa mochititsa kaso.



English : The glaciers are not stable, but flow down the mountain. This will cause cracks, crevasses, which may be obscured by snow bridges.

Nyanja : Madzi wogwirana sadakhazikike koma kutsetseleka mu phiri. Izi zimapangitsa kusweka komwe kumaphimbika ndi mitsinje yamadzi wouma wofewa.



English : The walls and roofs of ice caves can collapse and cracks can get closed.

Nyanja : Zipupa komanso madenga a mapanga amadzi wowundana atha kugwa komanso ming´alu itha kutsekeka.



English : At the edge of glaciers huge blocks break loose, fall down and perhaps jump or roll farther from the edge.

Nyanja : Mphepete mwa madzi oundana okula kwambiri mbali zina zimasweka kukhala pazokha, amagwera pansi ndipo ena amalumpha kapena kugubuduzika patali ndi mphepete.



English : The tourist season for the hill stations generally peaks during the Indian summer.

Nyanja : Nthawi ya alendo yopita ku kokwelera sitima zapamtunda kumapiri imafika pachimake nthawi yotentha yaku India.



English : However, they have a different kind of beauty and charm during winter, with many hill stations receiving healthy amounts of snow and offering activities such as skiing and snowboarding.

Nyanja : Komabe, zilindikukongola ndi kukomedwetsa nthawi yozizira, pamene mapiri ambiri amakhala ndi chpale chofewa ndipo utha kuchita masewero a skiing ndi snowballing.



English : Only a few airlines still offer bereavement fares, which slightly discount the cost of last-minute funeral travel.

Nyanja : Makampani andege ochepa okha amaperekabe mitengo yonyamulira maliro zomwe zimachepetsa pang´ono mtengo wa nthawi yomaliza ya pauledo wa maliro.



English : Airlines that offer these include Air Canada, Delta Air Lines, Lufthansa for flights originating from the U.S. or Canada, and WestJet.

Nyanja : Ndege zimene zimapeleka izi zikuphatikizapo za ku Canada, Delta, Lufthansa maka ndege zake zochokera ku U.S. kapena Canada, ndi WestJet.



English : In all cases, you must book by phone directly with the airline.

Nyanja : Nthawi ina iliyonse funsani malo amundege pogwiritsa ntchito foni.



Languages

Popular posts from this blog

40 days English and Javanese conversation with Flores.

40 days Chinese (Traditional) and Modern Standard Arabic (Romanized) conversation with Flores.

40 days Korean and South Levantine Arabic conversation with Flores.